Eksodo 12 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Eksodo 12:1-51

Kukhazikitsidwa kwa Paska

1Yehova anayankhula kwa Mose ndi Aaroni mʼdziko la Igupto kuti, 2“Mwezi uno uzikhala mwezi wanu woyamba wa chaka. 3Muliwuze khamu lonse la Israeli kuti pa tsiku la khumi la mwezi uno, munthu aliyense asankhire banja lake mwana wankhosa mmodzi. Banja lililonse litenge mwana wankhosa mmodzi. 4Ngati banja lili lochepa moti silingathe kudya nyama yonse ya nkhosa, ligawane ndi banja lomwe layandikana nalo nyumba. Mabanja adziwiretu chiwerengero cha anthu amene alipo pokonzekera zimenezi. Muwerengere kuchuluka kwa nyama imene anthu adzadye potengera mmene munthu mmodzi angadyere. 5Ziweto zimene musankhe ziyenera kukhala zazimuna za chaka chimodzi, zopanda chilema, ndipo zikhale nkhosa kapena mbuzi. 6Muzisunge mpaka tsiku la khumi ndi chinayi la mwezi, pamene gulu lonse la Aisraeli lidzaphe nyamazo madzulo. 7Ndipo adzatengeko magazi anyamazo ndi kuwaza pa mphuthu ziwiri za chitseko ndiponso pamwamba pa chitseko cha nyumba mmene adzadyeremo ana ankhosawo. 8Adzawotche nyamayo ndi kudya usiku womwewo, ndipo adzayidye ndi buledi wophikidwa popanda yisiti pamodzi ndi masamba wowawa. 9Musadzadye yayiwisi kapena yophika, koma mudzawotche yonse, mutu, miyendo ndi zamʼmimba. 10Musadzasiye nyama ina mpaka mmawa, ngati ina idzatsala mpaka mmawa, mudzayitenthe. 11Muzidzadya nyamayo mutavala chotere, pokonzekera ulendo: mudzazimangirire lamba mʼchiwuno, nsapato zanu kuphazi ndi ndodo yanu kumanja. Mudzadye mofulumira. Imeneyi ndi Paska ya Yehova.

12“Usiku umenewo Ine ndidzadutsa mʼdziko la Igupto ndipo ndidzapha chilichonse choyamba kubadwa kuyambira mwana wa munthu aliyense mpaka ana aziweto. Ndidzalanganso milungu yonse ya Igupto. Ine ndine Yehova. 13Magazi amene mudzawaze pa mphuthu za zitseko ndi pamwamba pa zitseko aja adzakhala ngati chizindikiro. Ine ndikadzaona magaziwo ndidzakudutsani, ndipo ndikadzamakantha anthu a Igupto, mliri wosakazawu sudzakukhudzani.

14“Ili ndi tsiku la chikumbutso. Tsiku limeneli muzidzachita chikondwerero, kupembedza Yehova. Mibado yonse imene ikubwera izidzakumbukira tsiku limeneli ngati lamulo lamuyaya ndi kuti pa tsikuli azidzachita chikondwerero cholemekeza Yehova. 15Kwa masiku asanu ndi awiri muzidya buledi wopanda yisiti. Tsiku loyamba muzichotsa yisiti mʼnyumba zanu, ngati aliyense adzadya kanthu kalikonse kali ndi yisiti kuyambira tsiku loyamba mpaka tsiku lachisanu ndi chiwiri, munthu ameneyo adzayenera kuchotsedwa mʼgulu la Israeli. 16Pa tsiku loyamba muzichita msonkhano wopatulika, ndipo winanso uzikhala pa tsiku lachisanu ndi chiwiri. Musamagwire ntchito masiku onsewa, koma ntchito yokonza chakudya yokha kuti aliyense adye. Izi ndi zimene muzichita.

17“Muzichita chikondwerero cha buledi wopanda yisiti, chifukwa ndi pa tsiku limeneli ndinatulutsa magulu anu mʼdziko la Igupto. Muzikondwerera tsiku limeneli pa mibado yonse ngati lamulo lamuyaya. 18Mwezi woyamba muzidzadya buledi wopanda yisiti kuyambira madzulo tsiku la 14 la mweziwo mpaka tsiku la 21 mwezi womwewo. 19Yisiti asamapezeka mʼnyumba zanu kwa masiku asanu ndi awiri. Ndipo aliyense amene adya chakudya chimene muli yisiti, munthu ameneyo ayenera kuchotsedwa mʼgulu la Aisraeli, kaya iyeyo ndi mlendo kapena mbadwa. 20Musadye chilichonse chokhala ndi yisiti. Kulikonse kumene mukukhala, muyenera kudya buledi wopanda yisiti.”

21Ndipo Mose anasonkhanitsa akuluakulu onse a Israeli nati, “Pitani msanga kukasankha nkhosa zokwanira pa mabanja anu, ndipo muziphe ngati Paska. 22Mutengenso nthambi ya chitsamba cha hisope, muchiviyike mʼmagazi amene mwawayika mʼbeseni ndipo muwaze ena mwa magaziwo pamwamba ndi mʼmbali mwa mphuthu za chitseko. Palibe aliyense wa inu amene adzatuluke mʼnyumba yake mpaka mmawa. 23Pamene Yehova adzadutsa mʼdziko kudzakantha Aigupto, nʼkuona magazi pamwamba ndi mʼmbali mwa mphuthu za chitseko, Iye adzadutsa khomo limenelo ndipo sadzalola woonongayo kuti alowe mʼnyumba zanu kuti akukantheni.

24“Muzimvera malamulo amenewa kwa muyaya, inu ndi zidzukulu zanu. 25Mukakalowa mʼdziko limene Yehova adzakupatseni monga analonjeza, mukasunge mwambo umenewu. 26Ndipo ana anu akakakufunsani kuti, ‘Mwambo umenewu ukutanthauza chiyani?’ 27Inu mukawawuze kuti, ‘Ndi nsembe ya Paska ya Yehova, popeza pamene ankakantha nyumba za Aigupto anasiya nyumba zathu.’ ” Kenaka anthu anawerama napembedza. 28Aisraeli anachita monga momwe Yehova analamulira Mose ndi Aaroni.

29Pakati pa usiku Yehova anakantha ana onse oyamba kubadwa mʼdziko la Igupto, kuyambira woyamba kubadwa wa Farao, amene amakhala pa mpando waufumu wa Faraoyo, mpaka mwana woyamba kubadwa wa munthu amene anali mʼdzenje, pamodzinso ndi ana oyamba kubadwa a ziweto zawo. 30Farao ndi nduna zake zonse ndiponso Aigupto onse anadzuka pakati pa usiku, ndipo kunali kulira kwakukulu mʼdziko lonse la Igupto, pakuti panalibe nyumba imene munalibe munthu wakufa.

Kutuluka kwa Aisraeli

31Pakati pa usiku Farao anayitanitsa Mose ndi Aaroni ndipo anati, “Nyamukani! Asiyeni anthu anga, inu ndi Aisraeli! Pitani, kapembedzeni Yehova monga munapempha. 32Tengani ziweto ndi ngʼombe zanu ndipo pitani kapembedzeni Mulungu wanu monga munanenera kuti ine ndidalitsike.”

33Aigupto anawawumiriza anthuwo kuti atuluke mofulumira ndi kusiya dziko lawo. Iwo anati, “Ngati sitiwalola kutero, tonse tidzafa.” 34Motero anthuwo ananyamula ufa wawo wopangira buledi asanathiremo yisiti ndipo anasenza pa mapewa awo pamodzi ndi zokandiramo buledi atazikulunga mu nsalu. 35Aisraeli anachita monga anawawuzira Mose kuti apemphe kwa Aigupto zozikongoletsera zasiliva ndi zagolide ndi zovala. 36Yehova anafewetsa mtima Aigupto kuti akomere mtima Aisraeliwo ndipo anawapatsa zimene anawapempha. Motero Aisraeli anawalanda zinthu Aigupto.

37Aisraeli anayenda ulendo kuchokera ku Ramesesi mpaka kukafika ku Sukoti. Anthu aamuna oyenda pansi analipo 600,000 osawerengera akazi ndi ana. 38Anthu enanso ambiri anapita nawo, kuphatikizanso gulu lalikulu la ziweto, mbuzi, nkhosa pamodzi ndi ngʼombe. 39Iwo anapanga buledi wopanda yisiti ndi ufa umene anachoka nawo ku Igupto. Ufawo unalibe yisiti chifukwa anachita kuthamangitsidwa ku Igupto ndipo analibe nthawi yokonzera chakudya chawo.

40Ndipo Aisraeli anakhala ku Igupto kwa zaka 430. 41Pa tsiku lomwelo limene anakwanitsa zaka 430, magulu onse a Yehova anatuluka mʼdziko la Igupto. 42Usiku wonse Yehova anachezera kutulutsa ana a Israeli mʼdziko la Igupto. Nʼchifukwa chake pa tsiku limeneli Aisraeli onse azichezera usiku wonse kulemekeza Mulungu kamba ka mibado yonse ya mʼtsogolo.

Lamulo la Paska

43Yehova anati kwa Mose ndi Aaroni, “Malamulo a Paska ndi awa:

“Mlendo asadye Paska. 44Kapolo aliyense amene munagula angadye ngati atayamba wachita mdulidwe. 45Koma amene mukukhala naye kwa kanthawi kapena waganyu asadye Paska.

46“Muzidyera Paska mʼnyumba imodzi. Musatulutse nyama iliyonse kunja kwa nyumba. Musaswe mafupa aliwonse. 47Gulu lonse la Israeli lizichita mwambo wachikondwererochi.

48“Ngati mlendo wokhala pakati panu angafune kuchita nawo mwambo wa chikondwerero cha Paska, cha Yehovachi, amuna onse a mʼnyumba mwake ayenera kuchita mdulidwe. Akatero muzimutenga ngati mbadwa pakati panu. Koma aliyense wosachita mdulidwe asadye Paska. 49Lamulo limeneli likhudza mbadwa ngakhalenso alendo wochita mdulidwe wokhala pakati panu.

50“Aisraeli onse anachita monga momwe Yehova analamulira Mose ndi Aaroni. 51Ndipo tsiku lomwelo Yehova anatulutsa gulu lonse la ana a Israeli mʼdziko la Igupto.”