Deuteronomo 6 – CCL & CCBT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Deuteronomo 6:1-25

Konda Yehova Mulungu Wako

1Awa ndi malamulo, malangizo ndi ziphunzitso zimene Yehova Mulungu wanu anandilamula kuti ndikuphunzitseni kuti mukawatsatire mʼdziko limene mukuwolokera Yorodani kuti mukalitenge, 2kuti inuyo, ana anu, ndi zidzukulu zanu mʼtsogolomo mudzaope Yehova Mulungu wanu moyo wanu wonse posunga malangizo ndi malamulo ake onse amene ndinakupatsani inu kuti musangalale ndi moyo wautali. 3Mvera Israeli ndipo usamalitse kuchita malamulowa kuti zinthu zikuyendere bwino mʼdziko ndi kuti muchuluke kwambiri mʼdziko loyenda mkaka ndi uchi monga momwe Yehova Mulungu wa makolo anu anakulonjezerani.

4Tamvani inu Aisraeli, Yehova Mulungu wathu, Yehova ndi mmodzi. 5Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu zako zonse. 6Malamulo amene ndakupatsani lero ayenera kukhala mu mtima mwanu. 7Muziwaphunzitsa mwachangu kwa ana anu. Muzikamba za malamulowa pamene muli mʼnyumba zanu, pamene mukuyenda mʼnjira, pamene mukugona ndi pamene mukudzuka. 8Muwamange ngati zizindikiro pa manja anu ndi kuwamangirira pa zipumi zanu. 9Muwalembe pa mphuthu za nyumba zanu ndi pa zipata zanu.

10Pamene Yehova Mulungu wanu akukulowetsani ndi kukupatsani dziko limene analumbirira makolo anu Abrahamu, Isake ndi Yakobo, dziko lokhala ndi mizinda ikuluikulu imene inu simunamange, 11nyumba zodzaza ndi zinthu za mitundu yonse zimene inu simunayikemo, zitsime zimene inu simunakumbe, minda ya mpesa ndi mitengo ya olivi zimene inuyo simunadzale, tsono mukadya ndi kukhuta, 12samalani kuti mungayiwale Yehova amene anakutulutsani ku Igupto, kukuchotsani mu ukapolo.

13Muziopa Yehova Mulungu wanu ndi kumutumikira Iye yekha, ndipo muzilumbira pa dzina lake. 14Musamatsatire milungu ina, milungu ya anthu ena okuzungulirani, 15pakuti Yehova Mulungu wanu amene ali pakati panu, ndi Mulungu wansanje ndipo adzakukwiyirani kwambiri ndi kukuwonongani, kukufafanizani mʼdziko. 16Musamuyese Yehova Mulungu wanu monga munachitira ku Masa. 17Onetsetsani kuti mukusunga malamulo a Yehova Mulungu wanu, malangizo ake ndi zikhazikitso zake zimene anakulamulirani. 18Chitani zoyenera ndi zabwino pamaso pa Yehova, kuti zikuyendereni bwino ndi kuti mukhoza kukalowa ndi kulanda dziko labwinolo limene Yehova analonjeza molumbira kwa makolo anu, 19kupirikitsiratu adani anu onse, monga Yehova wanenera.

20Mʼtsogolo muno, ana anu akadzakufunsani kuti, “Kodi tanthauzo la ndondomeko, malangizo, zikhazikitso ndi malamulo amene Yehova Mulungu wathu anakulamulani nʼchiyani?” 21Inu mudzawawuze kuti, “Ife tinali akapolo a Farao ku Igupto, koma Yehova anatitulutsa ku Igupto ndi dzanja lamphamvu. 22Ifeyo tikuona Yehova anatumiza zizindikiro zozizwitsa ndi zodabwitsa, zazikulu ndi zoopsa, pa Aigupto ndi Farao pamodzi ndi banja lake lonse. 23Koma anatitulutsa kumeneko ndi kutilowetsa kuno natipatsa dziko limene analonjeza mwa lumbiro kwa makolo athu. 24Yehova anatilamula kuti tizimvera malamulo onsewa, kuti tizimuopa kuti zinthu zizitiyendera bwino pa moyo wathu monga momwe zilili leromu. 25Ndipo ngati tisamala kumvera malamulo onsewa pamaso pa Yehova Mulungu wathu monga momwe anatilamulira ife, chimenecho chidzakhala chilungamo chathu.”

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

申命記 6:1-25

最大的誡命

1「你們的上帝耶和華吩咐我教導你們以下的誡命、律例和典章,以便你們在將要佔領的土地上遵行。 2這樣,你們就會得享長壽,你們及子孫就會終生敬畏你們的上帝耶和華,遵守祂藉我吩咐你們的一切律例和誡命。 3以色列人啊,你們要留心聽,謹慎遵行,以便你們在那奶蜜之鄉可以凡事順利、子孫眾多,正如你們祖先的上帝耶和華給你們的應許。 4聽啊,以色列人,耶和華是我們的上帝,耶和華是獨一的。 5你們要全心、全意、全力愛你們的上帝耶和華。 6要將我今天吩咐你們的話牢記在心, 7並教導你們的兒女,無論在家在外,或起或臥,都要講論這些律例和誡命。 8要把它們繫在手上、戴在額上作記號, 9要寫在城門上和自家的門框上。

10「你們的上帝耶和華將帶你們進入祂向你們祖先亞伯拉罕以撒雅各起誓要賜給你們的土地。那裡的宏偉城邑不是你們建造的, 11滿屋的美物不是你們積攢的,井不是你們挖掘的,葡萄園和橄欖樹也不是你們栽種的。你們在那裡吃飽喝足之後, 12要小心,不可忘記把你們從受奴役之地——埃及救出來的耶和華。 13要敬畏你們的上帝耶和華,事奉祂,憑祂的名起誓。 14不可隨從周圍各族的神明, 15免得你們的上帝耶和華向你們發怒,把你們從世上消滅;因為祂住在你們當中,祂痛恨不貞。

16「不可像在瑪撒那樣試探你們的上帝耶和華。 17要謹遵你們的上帝耶和華吩咐你們的誡命、法度和律例。 18你們要做耶和華視為正與善的事,以便你們可以凡事順利,得到耶和華起誓賜給你們祖先的佳美之地, 19趕出所有敵人,正如耶和華所言。

20「將來你們的子孫會問,『我們的上帝耶和華給你們頒佈這些法度、律例和典章是什麼意思?』 21你們要告訴他們,『我們曾在埃及做法老的奴隸,耶和華用大能的手領我們離開埃及22我們親眼看見耶和華行偉大而可畏的神蹟奇事,懲罰埃及和法老全家。 23祂帶領我們離開埃及,為要把我們帶進祂起誓賜給我們祖先的這片土地。 24我們的上帝耶和華吩咐我們遵守這一切律例、敬畏祂,以便我們可以常常受益,生命無憂,正如今日的情形。 25如果我們按照我們的上帝耶和華的吩咐,在祂面前謹遵這一切誡命,我們便被算為義人。』