Deuteronomo 34 – CCL & CARST

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Deuteronomo 34:1-12

Mose Amwalira

1Ndipo Mose anakwera Phiri la Nebo kuchokera ku chigwa cha Mowabu ndi kukafika pamwamba pa Phiri la Pisiga, kummawa kwa Yeriko. Kumeneko Yehova anamuonetsa dziko lonse; kuchokera ku Giliyadi mpaka ku Dani. 2Dera lonse la Nafutali, dziko lonse la Efereimu ndi Manase, dziko lonse la Yuda mpaka kukafika kumadzulo kwa nyanja, 3Negevi ndi chigawo chonse kuchokera ku Chigwa cha Yeriko, Mzinda wa mitengo ya migwalangwa, mpaka ku Zowari. 4Kenaka Yehova anawuza Mose kuti, “Limenelo ndi dziko limene ndinalonjeza mwa lumbiro kwa Abrahamu, Isake ndi Yakobo pamene ndinanena kuti, ‘Ndidzalipereka kwa zidzukulu zanu.’ Ndakulola kuti ulione, koma sudzawoloka kuti ukalowemo.”

5Choncho Mose mtumiki wa Yehova anamwalira kumeneko ku Mowabu, monga momwe ananenera Yehova. 6Yehova anamuyika mʼmanda ku Mowabu, mʼchigwa choyangʼanana ndi Beti-Peori, koma mpaka lero palibe amene amadziwa pamene pali manda ake. 7Mose anamwalira ali ndi zaka 120, koma maso ake ankaonabe ndipo anali amphamvu. 8Aisraeli analira maliro a Mose mʼchikhwawa cha Mowabu kwa masiku makumi atatu mpaka nthawi ya kulira maliro ndi kukhuza inatha.

9Tsono Yoswa, mwana wa Nuni anadzazidwa ndi mzimu wanzeru chifukwa nʼkuti Mose atamusanjika manja. Choncho Aisraeli anamumvera ndipo anachita zomwe Yehova analamula Mose.

10Kuyambira nthawi imeneyi, mu Israeli simunakhalepo mneneri wina aliyense wofanana ndi Mose, amene Yehova amayankhula naye maso ndi maso. 11Amene anachita zizindikiro zozizwitsa zonsezi ndi zozizwitsa zimene Yehova anamutuma kuti achite mu Igupto, kwa Farao ndi kwa nduna zake zonse ndiponso mʼdziko lake lonse. 12Ndithudi palibe mneneri wina aliyense amene anachita zinthu zazikulu ndi zoopsa zofanana ndi zomwe Mose anachita pamaso pa Aisraeli onse.

Священное Писание (Восточный перевод), версия для Таджикистана

Второзаконие 34:1-12

Смерть Мусо

1Затем Мусо поднялся на гору Нево, с равнин Моава на вершину Фасги, что напротив Иерихона. Там Вечный показал ему всю ту землю – от Галаада до Дона, 2все владения Неффалима, землю Ефраима и Манассы, всю землю Иуды до самого Средиземного моря34:2 Букв.: «западного моря»., 3Негев и всю область от равнины Иерихона, города Пальм, до самого города Цоара.

4Вечный сказал ему:

– Вот земля, которую Я с клятвой обещал Иброхиму, Исхоку и Якубу, когда сказал: «Я дам её твоим потомкам». Я позволил тебе увидеть её своими глазами, но ты не вступишь в неё.

5И Мусо, раб Вечного, умер там, в Моаве, как и сказал Вечный. 6Он похоронил его34:6 Или: «Его похоронили». в Моаве, в долине напротив Бет-Пеора, но и до сегодняшнего дня никто не знает, где его могила. 7Мусо было сто двадцать лет, когда он умер, но до самой смерти глаза его не ослабли и сила не истощилась. 8Исроильтяне оплакивали Мусо на равнинах Моава тридцать дней, пока не прошло время плача и скорби.

9Иешуа же, сын Нуна, исполнился духа34:9 Также возможно, что здесь говорится о Духе Всевышнего как об источнике мудрости. мудрости, потому что Мусо возложил на него руки. И исроильтяне слушали его и делали то, что Вечный повелел Мусо.

10С тех пор в Исроиле не было пророка, подобного Мусо, которого Вечный знал бы лицом к лицу. 11Никто не превзошёл Мусо в знамениях и чудесах, которые он совершил в Египте по слову Вечного над фараоном, над всеми его приближёнными и над всей его землёй. 12Никто не показывал такой великой силы и не совершал таких великих и страшных чудес, какие Мусо совершил на глазах у всего Исроила.