Deuteronomo 31 – CCL & PCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Deuteronomo 31:1-30

Yoswa Alowa Mʼmalo mwa Mose

1Tsono Mose anapita ndi kukayankhula mawu awa kwa Aisraeli onse: 2“Tsopano ndili ndi zaka 120, ndipo sindingathenso kukutsogolerani. Yehova wandiwuza kuti, ‘Iwe sudzawoloka Yorodani.’ 3Mwini wake Yehova Mulungu wanu ndiye amene adzakutsogolerani powoloka. Iye adzawononga mitundu ina yonse, ndipo inu mudzatenga dziko lawo. Yoswa adzakutsogoleraninso powoloka, monga momwe ananenera Yehova. 4Ndipo Yehova adzawawononga iwo monga momwe anawonongera Sihoni ndi Ogi, mafumu Aamori, amene Iye anawawononga pamodzi ndi dziko lawo. 5Ambuye adzawapereka kwa inu, ndipo inu mukawachitire zonse zimene ndakulamulani. 6Khalani amphamvu ndi olimba mtima. Musachite nawo mantha kapena kunjenjemera pamaso pawo, chifukwa Yehova Mulungu wanu apita nanu. Sadzakusiyani kapena kukutayani.”

7Pamenepo Yehova anayitana Yoswa pamaso pa Aisraeli onse ndipo anamuwuza kuti, “Khala wamphamvu ndi wolimba mtima, pakuti iwe udzatsogolera anthu awa ku dziko limene Yehova analumbira kulipereka kwa makolo awo, ndipo iwe ukaligawe pakati pawo kuti likakhale cholowa chawo. 8Yehova mwini ndiye akukutsogolerani ndipo adzakhala nanu. Sadzakusiyani kapena kukutayani. Usachite mantha ndiponso usataye mtima.”

Kuwerenga Malamulo

9Choncho Mose analemba malamulo awa nawapereka kwa ansembe, ana Alevi, amene amanyamula Bokosi la Chipangano la Yehova, ndiponso kwa akuluakulu onse a Aisraeli. 10Kenaka Mose anawalamula kuti, “Pamapeto pa zaka zisanu ndi ziwiri zilizonse, chaka cha kukhululukidwa ngongole, pa nthawi ya Chikondwerero cha Misasa, 11pamene Aisraeli onse abwera kudzaonekera pamaso pa Yehova Mulungu wanu pamalo pamene Iye adzasankhe, mudzawerenge malamulo onsewa iwo akumva. 12Mudzasonkhanitse anthu onse pamodzi, amuna, akazi ndi ana pamodzi ndi alendo amene akukhala mʼmizinda yanu, kuti adzawamve ndi kuphunzira kuopa Yehova Mulungu wanu ndi kutsatira mosamala mawu onse a mʼmalamulowa. 13Ana awo amene sadziwa malamulo awa, ayenera kuwamva ndi kuphunzira kuopa Yehova Mulungu wanu nthawi zonse pamene mukukhala mʼdziko limene mukuwoloka Yorodani kukalitenga.”

Aneneratu za Kuwukira kwa Aisraeli

14Yehova anawuza Mose kuti, “Nthawi ya kufa kwako yafika. Itana Yoswa ndipo mubwere ku tenti ya msonkhano, kumene Ine ndidzamulangiza.” Choncho Mose ndi Yoswa anabwera ku tenti ya msonkhano.

15Pamenepo Yehova anaonekera ku tenti mʼchipilala cha mtambo, ndipo mtambowo unayima pamwamba pa khomo lolowera mu tenti. 16Ndipo Yehova anawuza Mose kuti, “Iwe ukupita kukapuma kumene kuli makolo ako, ndipo ukangomwalira, anthu awa adzayamba kupembedza milungu yachilendo ya mʼdziko limene akukalowamo. Adzanditaya ndi kuphwanya pangano lomwe ndinachita nawo. 17Tsiku limenelo Ine ndidzawakwiyira ndi kuwataya. Ndidzawabisira nkhope yanga, ndipo adzawonongedwa. Masautso ambiri ndi zovuta zambiri zidzawagwera, ndipo tsiku limenelo adzafunsa kuti, ‘Kodi masautso awa sanagwere ife chifukwa Yehova Mulungu wathu sali nafe?’ 18Ndipo Ine ndidzabisa ndithu nkhope yanga pa tsiku limenelo chifukwa cha zoyipa zimene anachita potembenukira kwa milungu ina.

19“Tsopano ulembe mawu a nyimbo iyi ndipo uwaphunzitse Aisraeli, uwawuze kuti aziyimba, kuti ikhale mboni yanga yowatsutsa. 20Pamene ndawalowetsa mʼdziko loyenda mkaka ndi uchi, dziko limene ndinalonjeza mwalumbiro kwa makolo awo, ndipo pamene adzadya ndi kukhuta ndi kumasangalala, iwo adzatembenukira kwa milungu ina ndi kumayipembedza, kundikana Ine ndi kuphwanya pangano langa. 21Ndipo pamene masautso ambiri ndi zovuta zambiri zidzawagwera, nyimbo iyi idzakhala mboni yanga yowatsutsa, chifukwa zidzukulu zawo sizidzayiwala nyimboyi. Ine ndikudziwa zimene iwo akulingalira kuchita, ngakhale kuti sindinawalowetse mʼdziko limene ndinalonjeza mwa lumbiro.” 22Choncho Mose analemba nyimbo iyi tsiku limenelo ndi kuwaphunzitsa Aisraeli.

23Yehova analamula Yoswa mwana wa Nuni kuti, “Khala wamphamvu ndipo limba mtima, chifukwa udzalowetsa Aisraeli mʼdziko limene ndinawalonjeza mwa lumbiro, ndipo Ine mwini ndidzakhala nawe.”

24Mose atatha kulemba malamulowa mʼbuku, osasiyako kanthu, 25analamula Alevi amene ananyamula Bokosi la Chipangano la Yehova kuti, 26“Tengani Buku ili la Malamulo ndi kuliyika pambali pa Bokosi la Chipangano la Yehova Mulungu wanu. Likhale kumeneko ngati mboni yokutsutsani. 27Pakuti Ine ndikudziwa kuwukira kwanu ndi kuwuma mtima kwanu. Ngati inu mwakhala mukuwukira Yehova ine ndili moyo ndiponso ndili nanu pamodzi, nanga mudzawukira motani ine ndikamwalira! 28Mundisonkhanitsire atsogoleri onse a mafuko anu pamodzi ndi akuluakulu onse, kuti ndiyankhule mawu awa iwo akumva ndipo kumwamba ndi dziko lapansi zikhale mboni yowatsutsa. 29Chifukwa ndikudziwa kuti ine ndikamwalira mudzayipa kwambiri ndi kutembenuka kuleka njira imene ndinakulamulani. Masiku amene akubwera, masautso adzakugwerani chifukwa mudzachita zoyipa pamaso pa Yehova ndi kuputa mkwiyo wake chifukwa cha zimene manja anu anapanga.”

Nyimbo ya Mose

30Ndipo Mose ananena mawu a nyimbo iyi kuyiimba koyambira mpaka potsiriza gulu lonse la Aisraeli likumva:

Persian Contemporary Bible

تثنيه 31:1‏-30

يوشع جانشين موسی می‌شود

1‏-2موسی در ادامهٔ سخنان خود به قوم اسرائيل چنين گفت: «من اكنون صد و بيست سال دارم و ديگر قادر نيستم شما را رهبری كنم. خداوند به من گفته است از رود اردن عبور نخواهم كرد. 3خود خداوند شما را رهبری خواهد نمود و قومهایی را كه در آنجا زندگی می‌كنند نابود خواهد كرد و شما سرزمين ايشان را به تصرف خود در خواهيد آورد. طبق فرمان خداوند، يوشع رهبر شما خواهد بود. 4خداوند همانطور كه سيحون و عوج، پادشاهان اموری را هلاک ساخته، سرزمينشان را ويران نمود، قومهایی را نيز كه در اين سرزمين زندگی می‌كنند نابود خواهد كرد. 5خداوند، ايشان را به دست شما تسليم خواهد كرد و شما بايد طبق دستوری كه داده‌ام با آنها رفتار كنيد. 6قوی و دلير باشيد. از ايشان نترسيد. خداوند، خدايتان با شما خواهد بود. او شما را تنها نخواهد گذاشت و ترک نخواهد كرد.»

7آنگاه موسی يوشع را احضار كرده، در حضور تمامی قوم اسرائيل به او گفت: «قوی و دلير باش، زيرا تو اين قوم را به سرزمينی كه خداوند به اجدادشان وعده داده است رهبری خواهی كرد تا آنجا را تصرف كنند. 8ترسان نباش، زيرا خداوند با تو خواهد بود و پيشاپيش تو حركت خواهد كرد. او تو را تنها نخواهد گذاشت و ترک نخواهد كرد.»

قرائت قوانين خداوند

9آنگاه موسی قوانين خدا را نوشت و آن را به كاهنان لاوی كه صندوق عهد خداوند را حمل می‌كردند و نيز به ريش‌سفيدان اسرائيل سپرد. 10‏-11او به ايشان فرمود: «اين قوانين را در پايان هر هفت سال، يعنی در سالی كه قرضها بخشيده می‌شود، هنگام عيد خيمه‌ها كه تمام قوم اسرائيل در حضور خداوند در مكانی كه او برای عبادت تعيين می‌كند جمع می‌شوند، برای آنها بخوانيد. 12تمام مردان، زنان، بچه‌ها و غريبانی را كه در ميان شما زندگی می‌كنند جمع كنيد تا قوانين خداوند را بشنوند و ياد بگيرند كه خداوند، خدايتان را احترام نمايند و دستوراتش را اطاعت كنند. 13چنين كنيد تا بچه‌هايتان كه با اين قوانين آشنايی ندارند آنها را بشنوند و بياموزند كه در سرزمين موعود تا هنگامی كه زنده‌اند، خداوند را احترام نمايند.»

آخرين دستورات خداوند به موسی

14آنگاه خداوند به موسی فرمود: «پايان عمرت نزديک شده است. يوشع را بخوان و با خود به خيمهٔ عبادت بياور تا دستورات لازم را به او بدهم.» پس موسی و يوشع به خيمهٔ عبادت وارد شدند.

15در خيمهٔ عبادت، خداوند در ابر ظاهر شد و ابر، بالای در خيمه ايستاد. 16سپس خداوند به موسی گفت: «تو خواهی مرد و به پدرانت ملحق خواهی شد. بعد از تو، اين قوم در سرزمين موعود به من خيانت كرده، به پرستش خدايان بيگانه خواهند پرداخت و مرا از ياد برده، عهدی را كه با ايشان بسته‌ام خواهند شكست. 17آنگاه خشم من بر ايشان شعله‌ور شده، ايشان را ترک خواهم كرد و رويم را از ايشان برخواهم گرداند تا نابود شوند. سختيها و بلاهای بسيار بر ايشان نازل خواهد شد به طوری كه خواهند گفت: خدا ديگر در ميان ما نيست. 18من به سبب گناه بت‌پرستی‌شان رويم را از ايشان برمی‌گردانم.

19«اكنون كلمات اين سرود را كه به تو می‌دهم بنويس و به مردم اسرائيل ياد بده تا هشداری به آنها باشد. 20زمانی كه ايشان را به سرزمينی كه به پدرانشان وعده داده بودم آوردم، يعنی به سرزمينی كه شير و عسل در آن جاری است و پس از اينكه سير و فربه شدند و به پرستش خدايان ديگر پرداختند و مرا رد نموده، عهد مرا شكستند 21و به سختيها و بلاهای بسيار دچار شدند، در آن هنگام، اين سرود چون شاهدی بر ضد آنها گواهی خواهد داد. اين سرود از نسلی به نسل ديگر، سينه به سينه نقل خواهد شد. من از همين حالا، حتی قبل از اينكه وارد سرزمين موعود شوند، افكار ايشان را می‌دانم.»

22پس در همان روز، موسی كلمات سرود را نوشت و آن را به قوم اسرائيل ياد داد. 23سپس خداوند به يوشع فرمود: «قوی و دلير باش، زيرا تو بايد مردم اسرائيل را به سرزمينی كه من به ايشان وعده داده‌ام هدايت كنی، و من با تو خواهم بود.»

24وقتی كه موسی كليهٔ قوانينی را كه در اين كتاب ثبت شده است نوشت، 25به لاويانی كه صندوق عهد خداوند را حمل می‌كردند فرمود: 26«اين كتاب قانون را به عنوان هشداری جدی به قوم اسرائيل، در کنار صندوق عهد خداوند، خدايتان قرار دهيد. 27چون می‌دانم كه اين قوم چقدر ياغی و سركشند. اگر امروز كه در ميان ايشان هستم نسبت به خداوند اينچنين ياغی شده‌اند، پس، بعد از مرگ من چه خواهند كرد. 28اكنون كليهٔ رهبران و ريش‌سفيدان قبيله‌هايتان را احضار كنيد تا اين سخنان را به ايشان بگويم و زمين و آسمان را بر ايشان شاهد بگيرم. 29می‌دانم كه پس از مرگ من، خود را به کلی آلوده كرده، از دستوراتی كه به شما داده‌ام سرپيچی خواهيد كرد. در روزهای آينده، مصيبت گريبانگير شما خواهد شد، زيرا آنچه را كه خداوند نمی‌پسندد همان را انجام خواهيد داد و او را بسيار غضبناک خواهيد كرد.»

سرود موسی

30سپس موسی اين سرود را برای تمام جماعت اسرائيل خواند: