Deuteronomo 29 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Deuteronomo 29:1-29

Kukonzanso Pangano

1Awa ndiwo mawu a mʼpangano limene Yehova analamula Mose kuti achite ndi Aisraeli ku Mowabu, powonjezera pa pangano limene anapangana nawo ku Horebu.

2Mose anayitanitsa Aisraeli onse nati kwa iwo:

Inu munaona zonse zimene Yehova anachita kwa Farao, nduna zake ndi dziko lake lonse ku Igupto. 3Ndi maso anu munaona mayesero onse aja, zizindikiro zozizwitsa ndi zodabwitsa zazikulu zija. 4Koma mpaka lero Yehova sanakupatseni mtima wozindikira kapena maso openya kapena makutu akumva. 5Mʼzaka makumi anayi zimene ndinakutsogolerani mʼchipululu, zovala zanu ndiponso nsapato za ku mapazi anu sizinangʼambike. 6Inu simunadye buledi ndi kumwa vinyo kapena chakumwa chilichonse choledzeretsa. Ndinachita izi kuti mudziwe kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

7Pamene munafika malo ano, Sihoni mfumu ya ku Hesiboni ndi Ogi mfumu ya ku Basani anabwera kudzamenyana nafe koma tinawagonjetsa iwo. 8Tinatenga dziko lawo ndi kulipereka ngati cholowa cha fuko la Rubeni, fuko la Gadi ndi theka la fuko la Manase.

9Tsatirani mosamalitsa mawu a mʼpangano ili kuti zinthu zizikuyenderani bwino pa zochitika zanu zonse. 10Lero lino nonse mukuyima pamaso pa Yehova Mulungu wanu, atsogoleri a mafuko anu, akuluakulu ndi nduna zanu, ndi amuna ena onse a mu Israeli, 11pamodzi ndi ana ndi akazi anu, kudzanso alendo amene akukhala pakati panu omwe amakuwazirani nkhuni ndi kukutungirani madzi. 12Mukuyimirira pano kuti mulowe mʼpangano ndi Yehova Mulungu wanu, pangano limene Yehova akuchita ndi inu lero ndi kulisindikiza ndi malumbiro, 13kukukhazikitsani lero lino ngati anthu ake, ndi kuti Iye akhale Mulungu wanu monga anakulonjezani inu ndiponso monga analumbira kwa makolo anu Abrahamu, Isake ndi Yakobo. 14Ndikupanga pangano ili ndi malumbiro ake osati kwa inu nokha, 15amene muli pano pamaso pa Yehova Mulungu wathu, koma ndi iwonso amene sali pano lero.

16Inu nomwe mukudziwa mmene tinkakhalira ku Igupto ndi mmene tinadutsira mayiko pa ulendo wobwera kuno. 17Ife tinaona pakati pawo mafanizo ndi mafano awo onyansa, amtengo ndi amiyala, asiliva ndi agolide. 18Onetsetsani kuti pasapezeke mwamuna kapena mkazi, banja kapena fuko pakati panu lero amene mtima wawo udzapandukira Yehova Mulungu wanu ndi kupita kukapembedza milungu ya mitundu iyo. Onetsetsani kuti pasapezeke muzu pakati panu wotulutsa mankhwala akupha otere.

19Munthu wotere akamva mawu a lumbiro ili, asadzidalitse yekha mʼmaganizo mwake namati, “Ine ndidzapulumuka ngakhale nditapitiriza kuyenda njira yanga.” Zoterezi zidzadzetsa masautso pa nthaka ya chinyontho ndi yowuma yomwe. 20Yehova sadzamukhululukira. Mkwiyo ndi nsanje ya Yehova zidzamuyakira munthuyo. Matemberero onse wolembedwa mʼbukuli adzamugwera iye ndipo Yehova adzafafaniza dzina lake pa dziko lapansi. 21Yehova adzasankha pakati pa Aisraeli anthu oyenera masautso monga mwa matemberero onse a mʼpangano olembedwa Mʼbuku la Malamulo.

22Ana anu a mibado yakutsogolo ndi alendo amene adzachokera kutali adzaona matsoka amene adzakugwerani mʼdziko muno ndiponso matenda amene Yehova adzabweretsa pa dzikoli. 23Dziko lonse lidzasanduka nthaka ya mchere ndi ya sulufule. Simudzadzalamo kanthu, simudzakhala chomera chilichonse, ndi mbewu yomera mʼmenemo. Dziko lanu lidzakhala lowonongeka ngati Sodomu ndi Gomora, Adima ndi Zeboimu, mizinda imene Yehova anayiwononga ndi mkwiyo wake waukulu. 24Mitundu yonse ya anthu idzafunsa kuti, “Kodi chifukwa chiyani Yehova anachita zotere mʼdziko lake? Kodi chifukwa chiyani anaonetsa mkwiyo woopsa wotere?”

25Ndipo yankho la mafunso amenewa lidzakhala lakuti, “Chifukwa chakuti anthu awa aphwanya pangano la Yehova Mulungu wa makolo awo, pangano limene Iye anapangana nawo pamene anawatulutsa ku Igupto. 26Iwo anachoka ndi kukatumikira milungu ina ndi kuyipembedza, milungu imene sanayidziwe, milungu imene sanawapatse. 27Choncho Yehova anakwiyira dziko lino, kotero anabweretsa matemberero onse amene analembedwa mʼbuku lino. 28Ndi mkwiyo komanso ukali wake woopsa Yehova anawazula mʼdziko lawo ndi kuwaponyera mʼdziko lina, monga mmene zilili lero lino.”

29Zinsinsi ndi za Yehova Mulungu wathu koma zinthu zimene zaululidwa ndi zathu ndi ana athu kwamuyaya, kuti titsatire mawu onse a mʼmalamulowa.