Deuteronomo 25 – CCL & NVI

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Deuteronomo 25:1-19

1Anthu akasemphana mawu, ayenera kupita ku bwalo la milandu ndipo woweruza adzaweruza mlanduwo. Adzamasula wosalakwa nalanga wolakwa. 2Munthu akapezeka wolakwa ayenera kukwapulidwa, woweruza amugoneke pansi wolakwayo ndipo akwapulidwe pamaso pake zikoti zochuluka molingana ndi mlandu wake, 3koma asamukwapule zikoti zopitirira makumi anayi. Akakwapulidwa kupitirira apo ndiye kuti mʼbale wanuyo anyozeka pamaso panu.

4Musamange ngʼombe pakamwa pamene ikupuntha tirigu.

5Ngati abale akukhala pamodzi ndipo wina mwa iwo akamwalira wosasiya mwana wamwamuna, mkazi wamasiyeyo asakakwatiwe ndi mlendo. Mʼbale wake wa mwamuna wakeyo amukwatire kukwaniritsa chimene akuyenera kuchita kwa mlamu wakeyo. 6Mwana wamwamuna woyamba amene mayiyo angabereke ayenera kutenga dzina la mwamuna wake womwalirayo kuti dzina lake lisafafanizike mu Israeli.

7Komabe, ngati munthu sakufuna kukwatira mkazi wa mʼbale wakeyo, mkaziyo ayenera kupita kwa akuluakulu ku chipata cha mzinda ndi kukanena kuti, “Mʼbale wake wa mwamuna wanga akukana kupitiriza dzina la mʼbale wake mu Israeli. Iye akukana kulowa chokolo.” 8Pamenepo akuluakulu a mu mzinda wawowo adzamuyitanitsa nakamba naye. Ngati alimbikirabe kunena kuti, “Ine sindikufuna kumukwatira mkaziyu,” 9mkazi wamasiye wa mʼbale wakeyo adzapita kwa iye pamaso pa akuluakuluwo namuvula nsapato imodzi, adzamulavulire kumaso nʼkunena kuti, “Izi ndi zimene amachitira munthu amene safuna kupitiriza mbiri ya banja la mʼbale wake.” 10Mbiri ya banja la munthu ameneyo idzadziwika mu Israeli kuti ndi Banja la Wovulidwa nsapato.

11Ngati anthu awiri akuchita ndewu ndipo mkazi wa mmodzi wa iwo abwera kudzaleretsa mwamuna wake kwa mnzakeyo natambasula dzanja lake kugwira ku maliseche kwa winayo, 12muyenera kumudula dzanja, osamumvera chisoni.

13Musamakhale ndi miyeso iwiri yosiyana mʼthumba mwanu, wolemera ndi wopepuka. 14Musamakhale ndi milingo iwiri yosiyana mʼnyumba mwanu, waukulu ndi waungʼono. 15Muyenera kukhala ndi miyeso ndi milingo yoyenera ndi yosanyenga kuti mukhalitse mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani. 16Pakuti Yehova Mulungu wanu amanyansidwa ndi aliyense wochita za chinyengo zoterezi.

17Kumbukirani zimene Aamaleki anakuchitirani pamene munali pa ulendo wochokera ku Igupto. 18Pamene munali otopa ndi ofowoka, iwo anakumana nanu pa ulendo wanu ndi kukantha onse otsalira mʼmbuyo ndipo iwo sanaope Mulungu. 19Pamene Yehova Mulungu wanu akupumulitsani kwa adani onse okuzungulirani mʼdziko limene akupatsani inu ngati cholowa chanu, mudzawafafanize Aamaleki, asadzawakumbukirenso pa dziko lapansi. Musadzayiwale chimenechi!

Nueva Versión Internacional

Deuteronomio 25:1-19

1Cuando dos hombres tengan un pleito, se presentarán ante el tribunal y los jueces decidirán el caso, absolviendo al inocente y condenando al culpable. 2Si el culpable merece que lo azoten, el juez le ordenará tenderse en el suelo y hará que allí mismo le den el número de azotes que su crimen merezca. 3Pero no se le darán más de cuarenta azotes; más de eso sería humillante para tu hermano.

4No pongas bozal al buey mientras esté sacando el grano.

5Si dos hermanos viven juntos y uno muere sin dejar hijos, su viuda no se casará fuera de la familia. El hermano del esposo la tomará y se casará con ella para cumplir con su deber de cuñado. 6El primer hijo que ella tenga llevará el nombre del hermano muerto para que su nombre no desaparezca de Israel.

7Si tal hombre no quiere casarse con la viuda de su hermano, ella recurrirá a los jefes, a la entrada de la ciudad, y dirá: «Mi cuñado no quiere mantener vivo en Israel el nombre de su hermano. Se niega a cumplir conmigo su deber de cuñado». 8Entonces los jefes lo llamarán y le hablarán. Si persiste en decir: «No quiero casarme con ella», 9la cuñada se acercará a él y, en presencia de los jefes, le quitará una de las sandalias, le escupirá en la cara y dirá: «Esto es lo que se hace con quien no quiere mantener viva la descendencia de su hermano». 10Y para siempre se conocerá en Israel a ese hombre y a su familia como «los descalzos».

11Si dos hombres se están peleando y la mujer de uno de ellos, para rescatar a su esposo, agarra al atacante por los genitales, 12tú le cortarás a ella la mano. No le tendrás compasión.

13No tendrás en tu bolsa dos pesas diferentes, una más pesada que la otra. 14Tampoco tendrás en tu casa dos medidas diferentes, una más grande que la otra. 15Más bien, tendrás pesas y medidas precisas y justas, para que vivas mucho tiempo en la tierra que te da el Señor tu Dios. 16El Señor tu Dios aborrece a quien actúa deshonestamente.

17Recuerda lo que te hicieron los amalecitas después de que saliste de Egipto: 18cuando estabas cansado y fatigado, salieron a tu encuentro y atacaron por la espalda a todos los rezagados. ¡No tuvieron temor de Dios! 19Por eso, cuando el Señor tu Dios te dé la victoria sobre todas las naciones enemigas que rodean la tierra que él te da como herencia, borrarás para siempre el recuerdo de los descendientes de Amalec. ¡No lo olvides!