Deuteronomo 24 – CCL & CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Deuteronomo 24:1-22

1Ngati mwamuna wakwatira mkazi amene sakukondwera naye chifukwa wapeza vuto pa mkaziyo, namulembera mkaziyo kalata ya chisudzulo, namupatsa ndi kumutulutsa mʼnyumba mwake, 2mkaziyo ndi kukakwatiwa ndi mwamuna wina, 3ndipo mwamuna wachiwiriyo nʼkuyipidwa nayenso ndi kumulemberanso kalata ya chisudzulo nʼkumutulutsa mʼnyumba mwake, kapena ngati mwamunayo amwalira, 4mwamuna wake woyamba uja, amene anamuleka saloledwanso kumukwatira kachiwiri popeza mkaziyo wadetsedwa. Chimenechi ndi chonyansa pamaso pa Yehova. Musalowetse tchimo mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani ngati cholowa chanu.

5Mwamuna akangokwatira kumene asamatumizidwe ku nkhondo kapena kupatsidwa ntchito ina iliyonse. Kwa chaka chathunthu akhale ndi ufulu wokhala pa khomo pake kumasangalatsa mkazi wakeyo.

6Munthu akakhala nanu ndi ngongole musamutengere mwala wake wa mphero ngati chikole, chifukwa kutero nʼkumutengera moyo kukhala chikole cha ngongole.

7Ngati munthu agwidwa akuba mʼbale wake wa Chiisraeli namamuzunza ngati kapolo kapena kumugulitsa, wogulitsa mnzakeyo ayenera kuphedwa. Muyenera kuchotsa choyipa pakati panu.

8Pakagwa matenda a khate, samalitsani kuchita zonse zimene ansembe, amene ndi Alevi, anakulangizani. Mutsatire mosamalitsa zimene ndinawalamula. 9Kumbukirani zimene Yehova Mulungu wanu anachita kwa Miriamu muli paulendo mutatuluka mu Igupto.

10Ukabwereketsa mnzako kanthu kena kalikonse, usalowe mʼnyumba mwake kukatenga chimene wachipereka ngati chikole. 11Uziyima kunja kwa nyumba kuti munthu amene wamubwereketsa kanthuyo akubweretsere kunja komweko. 12Ngati munthuyo ndi wosauka, usamutengere chikolecho mpaka kukagona nacho kwanu. 13Pomalowa dzuwa ukhale utamubwezera mkanjo wakewo kuti akafunde. Pamenepo adzakuthokoza, ndipo amenewa adzawerengedwa ngati machitidwe olungama kwa iweyo pamaso pa Yehova Mulungu wako.

14Osamapezera mwayi pa anthu aganyu osauka ndi aumphawi, kaya ndi Mwisraeli kapena mlendo wokhala mu umodzi mwa mizinda yanu. 15Mumulipire malipiro ake a tsiku dzuwa lisanalowe chifukwa ndi wosauka ndipo akudalira malipirowo. Kupanda kutero adzakudandaulirani kwa Yehova ndipo mudzapezeka ochimwa.

16Makolo asaphedwe chifukwa cha ana awo, ndipo ana asaphedwe chifukwa cha makolo awo, koma aliyense ayenera kufa chifukwa cha zolakwa zake.

17Musachitire mlendo kapena mwana wamasiye zoyipa, kapena kulanda mkazi wamasiye chovala ngati chikole cha ngongole. 18Kumbukirani kuti munali akapolo mʼdziko la Igupto ndipo Yehova Mulungu wanu anakuwombolani kumeneko. Nʼchifukwa chake ndikukulamulani kuti muzichita zimenezi.

19Mukamakolola mʼmunda mwanu ndipo zokolola zina zikasiyidwa, musamabwerere kukazitola. Muzilekere alendo, ana ndi akazi amasiye, kuti Yehova Mulungu wanu akudalitseni pa zochita zanu zonse. 20Mukathyola zipatso mu mtengo wa olivi, musamabwererenso kachiwiri ku mtengo womwewo. Zotsalazo zilekereni alendo, ana ndi akazi amasiye. 21Mukakolola mphesa mʼmunda mwanu musamabwereremonso kachiwiri. Zotsalazo muzilekere alendo, ana ndi akazi amasiye. 22Kumbukirani kuti munali akapolo mʼdziko la Igupto. Nʼchifukwa chake ndikukulamulani kuti muzichita zimenezi.