Deuteronomo 23 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Deuteronomo 23:1-25

Wosayenera mu Msonkhano

1Mwamuna aliyense wofulidwa kapena woduka chiwalo chachimuna asalowe nawo mu msonkhano wa Yehova.

2Aliyense wobadwa mʼbanja losavomerezeka, kapena mdzukulu wake wina aliyense, ngakhale mibado khumi pambuyo pake, asalowe mu msonkhano wa Yehova.

3Mwamoni kapena Mmowabu asalowe mu msonkhano wa anthu a Yehova ngakhale mibado khumi yobwera pambuyo pake. 4Pakuti iwowa sanabwere kudzakulonjerani ndi chakudya kapena madzi pamene mumadutsa pochokera ku Igupto, mʼmalo mwake anakalemba ganyu Balaamu mwana wa Beori wochokera ku Petori ku Mesopotamiya kuti akutemberereni. 5Komabe Yehova Mulungu wanu sanamvere Balaamu koma anatembenuza temberero kukhala dalitso kwa inu chifukwa Yehova Mulungu wanu amakukondani. 6Musachite nawo mgwirizano uliwonse wa mtendere pa moyo wanu wonse.

7Musapeputse Mwedomu pakuti ndi mʼbale wanu ndithu. Musapeputse Mwigupto chifukwa munali alendo mʼdziko lake. 8Mʼbado wachitatu wa ana awo akhoza kulowa mu msonkhano wa anthu a Yehova.

Masamalidwe a Msasa

9Mukamakhala pa msasa pokonzekera adani anu, musayandikane ndi china chilichonse chodetsedwa. 10Wina mwa asilikali anu akadziwonongera ndi umuna usiku, ayenera kuchoka pa msasapo ndipo akhale kunja kwa msasa. 11Koma dzuwa likapendeka ayenera kusamba ndipo polowa dzuwa akhoza kubwerera ku msasa.

12Mukonze malo kunja kwa msasa kumene mukhoza kukadzithandizirako. 13Pakati pa zida zanu muzikhala ndi china chokumbira, ndipo pokadzithandiza muzikumba kadzenje ndi kukwirira chimbudzi chanu. 14Pakuti Yehova Mulungu wanu amayendayenda ku msasa wanu kukutchinjirizani ndi kupereka adani anu kwa inu. Nʼchifukwa chake msasa wanu uzikhala wopatulika kuti mwina angaone china chonyansa nabwerera osakuyandikirani.

Malamulo Osiyanasiyana

15Ngati kapolo wathawa mbuye wake nakabisala kwanu, musamuperekenso kwa mbuye wakeyo. 16Mumulole akhale pakati panu, paliponse pamene angakonde, mʼmudzi umene angasankhe ndipo musamupondereze.

17Pasapezeke Mwisraeli wamwamuna kapena wamkazi wochita chiwerewere ku Nyumba ya Mulungu. 18Musabweretse malipiro a wachiwerewere wamkazi kapena wamwamuna Mʼnyumba ya Yehova Mulungu wanu kudzapereka za malumbiro aliwonse, chifukwa Yehova Mulungu wanu amadana ndi zimenezi.

19Musamalipitse mʼbale wanu chiwongoladzanja, kaya pa ndalama, kapena pa chakudya, kapena pa china chilichonse choti nʼkupereketsa chiwongoladzanja. 20Mlendo mukhoza kumulipitsa chiwongoladzanja koma osati mʼbale wanu Mwisraeli, kuti Yehova Mulungu wanu akudalitseni pa zochitika zanu zonse mʼdziko mukulowamoli.

21Mukalumbira kupereka kanthu kwa Yehova Mulungu wanu, musamachedwetse kupereka, chifukwa Yehova Mulungu wanu adzakufunsanibe kanthuko ndipo mudzapezeka wochimwa. 22Koma ngati mupewa kupanga mapangano simudzapezeka ochimwa. 23Zilizonse zimene mulumbira ndi pakamwa panu muzitsimikiza kuzichita, chifukwa mwalumbira mwaufulu pamaso pa Yehova Mulungu wanu ndi pakamwa panu.

24Mukalowa mʼmunda wamphesa wa mnzanu mukhoza kudya mphesa mmene mungafunire koma musayike zina mʼdengu mwanu. 25Mukalowa mʼmunda wa tirigu wa mʼbale wanu, mukhoza kutengako ngala mʼmanja mwanu, koma osasenga tirigu ndi chikwakwa.