Deuteronomo 22 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Deuteronomo 22:1-30

1Ngati uwona ngʼombe kapena nkhosa ya mʼbale wako ikusochera, usayilekerere koma uyesetse kuyibwezera kwa iye. 2Ngati mʼbale wakoyo sakhala pafupi kapena sukudziwa kuti ndi yandani, uyitengere ku nyumba kwako ndi kuyisamala mpaka mwini wake atayilondola ndipo umubwezere. 3Uzitero ndithu ngati upeza bulu kapena mkanjo kapena chilichonse chimene chatayika. Osachilekerera.

4Ngati wapeza bulu kapena ngʼombe ya mʼbale wako itagwa panjira, usayilekerere. Ithandize kuti idzuke.

5Akazi asavale zovala za amuna, kapena mwamuna kuvala zovala za akazi, pakuti Yehova Mulungu wanu amanyansidwa ndi aliyense wochita izi.

6Ukapeza chisa cha mbalame mʼmphepete mwa msewu, kaya ndi mu mtengo kapena pansi, mbalame yayikazi itafungatira ana kapena mazira, usatenge mbalameyo pamodzi ndi ana ake omwe. 7Anawo mukhoza kutenga koma onetsetsani kuti mayi wawo mwamutaya kuti apite, kuti zinthu zizikuyenderani bwino ndiponso kuti mukhale ndi moyo wautali.

8Mukamanga nyumba yatsopano, mutchingire khonde lake la pa denga kuti inu musapezeke ndi mlandu wopha munthu ngati wina agwa kuchokera pa khonde la pa dengalo.

9Musadzale mbewu zamitundu iwiri mʼmunda wanu wa mpesa, ngati mutero, si mbewu zanu zokha zimene zidzakhale zodetsedwa, komanso zipatso za mʼmunda wamphesawo.

10Musatipule pogwiritsa ntchito ngʼombe ndi bulu pa goli limodzi.

11Musamavale chovala chopangidwa mophatikiza ubweya ndi thonje.

12Muzipanga mphonje mʼngodya za mkanjo umene mumavala.

Malamulo a Ukwati

13Ngati munthu akwatira mkazi, ndipo atagona naye nʼkusamufunanso 14namunyoza ndi kumuyipitsira dzina nʼkumati, “Ine ndinakwatira mkazi uyu, koma pamene ndinakhala naye, sindinachione chizindikiro cha unamwali wake,” 15zikatero abambo ndi amayi ake ayenera kubweretsa chitsimikizo chakuti anali namwali kwa akuluakulu a mzinda ku chipata. 16Abambo ake a mtsikanayo adzanene kwa akuluakuluwo kuti, “Ine ndinamupatsa munthu uyu mwana wanga wamkazi kuti amukwatire, koma sakumufunanso. 17Tsopano wamunyoza ndipo wanena kuti, ‘Ine sindinapeze kuti mwana wanu wamkaziyu ndi namwali.’ Koma tsopano onani chitsimikizo ichi cha unamwali wa mwana wanga wamkazi.” Kenaka makolo a mtsikanayo adzaonetse kansalu kwa akuluakulu aja, 18ndipo akuluakuluwo adzamugwire munthuyo namupatsa chilango. 19Iwo adzamulipitse ndalama zasiliva zokwana 100 nazipereka kwa abambo a mtsikana, chifukwa munthu uyu wayipitsa dzina la mtsikana wa Chiisraeli. Ayenera kukhalabe mkazi wake ndipo asadzamuleke moyo wake wonse.

20Koma ngati zomunenerazo ndi zoona, ndipo kuti chitsimikizo cha unamwali wa mtsikanayo sichinapezeke, 21iyeyu ayenera kumutengera pa khomo pa abambo ake pamene anthu a mu mzinda wake akamuphere ndi miyala. Iyeyo wachita chinthu chochititsa manyazi mu Israeli pochita chiwerewere akanali pa khomo pa abambo ake. Muyenera kuchotsa zoyipa pakati panu.

22Ngati munthu apezeka akugona ndi mkazi wa mwini wake, ayenera kuphedwa munthuyo pamodzi ndi mkazi yemwe wagona nayeyo. Muyenera kuchotsa zoyipa mu Israeli.

23Ngati munthu mu mzinda akumana ndi mkazi yemwe anachita kale chinkhoswe nagona naye, 24muwatengere awiriwo ku chipata cha mzinda ndi kuwapha ndi miyala. Aphedwe chifukwa mtsikanayo anali pafupi ndi anthu ndipo sanakuwe kuti ena amuthandize ndipo mwamunayo chifukwa anayipitsa mkazi wa mwini. Muyenera kuchotsa choyipa pakati panu.

25Koma ngati munthu akumana ndi mkazi kutchire yemwe anachita kale chinkhoswe namugwiririra, mwamuna yekhayo ndiye woyenera kuphedwa. 26Mtsikanayo musamuchite chilichonse, palibe tchimo limene wachita loti ayenera kuphedwa. Mlandu uwu ufanana ndi wa munthu amene alimbana ndi kupha mnzake woyandikana naye, 27pakuti mwamunayo anamupeza mtsikanayo kutchire, ndipo ngakhale mtsikana wachinkhosweyo anakuwa, panalibe anamulanditsa.

28Ngati munthu apezana ndi namwali woti sanachite chinkhoswe, namugwiririra, munthuyo nʼkupezeka, 29ayenera kuwalipira abambo ake a namwaliyo ndalama za siliva makumi asanu. Iye ayenera kumukwatira mkaziyo chifukwa wamuyipitsa, ndipo sadzamulekanso moyo wake wonse.

30Munthu asakwatire mkazi wa abambo ake pakuti ayenera kuchitira ulemu pogona pa abambo ake.