Deuteronomo 20 – CCL & CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Deuteronomo 20:1-20

Za ku Nkhondo

1Pamene mukupita kokachita nkhondo ndi adani anu, mukaona akavalo kapena magaleta kapena gulu la ankhondo kuposa inuyo musamaope chifukwa Yehova Mulungu wanu, amene anakutulutsani ku Igupto adzakhala nanu. 2Pamene mwatsala pangʼono kuyamba nkhondo, wansembe azibwera kutsogolo ndipo aziyankhula ku gulu lonse lankhondolo. 3Iye aziti, “Tamverani inu Aisraeli, mukupita kukachita nkhondo ndi adani anu lero. Musataye mitima kapena kuchita mantha ayi. Musaopsedwe kapena kunjenjemera pamaso pawo, 4pakuti Yehova Mulungu wanu ndiye amene apite nanu kukakumenyerani nkhondo ndi kugonjetsa adani anu.”

5Akuluakulu ankhondo adzati kwa gulu la ankhondolo, “Kodi pali wina amene wangomanga nyumba kumene ndipo sanayitsekulire? Ayambe wapita ku mudzi chifukwa mwina akafera ku nkhondoko ndipo wina ndi kudzayitsekulira. 6Kodi pali wina amene analima munda wamphesa ndipo sanayambe kudyerera? Ayambe wapita ku mudzi chifukwa mwina akafera ku nkhondo ndipo wina adzadyerera mundawo. 7Kodi pali amene wachita chinkhoswe ndi mkazi ndipo sanamukwatire mkaziyo? Ayambe wabwerera ku mudzi chifukwa mwina akafera ku nkhondo ndipo wina adzakwatira mkaziyo.” 8Ndipo akuluakulu ankhondowo akapitirize kuti, “Kodi pali amene akuchita mantha kapena kutaya mtima? Abwerere ku mudzi kuopa kuti abale ake angatayenso mtima.” 9Akuluakuluwo akatsiriza kuyankhula ndi gulu la ankhondolo, adzasankhe olilamulira.

10Pamene mukuyandikira kuphwanya mzinda, muyambe mwafunsa anthu a mu mzindawo ngati afuna zamtendere. 11Akavomera natsekula zipata zawo, anthu wonse mu mzindawo adzagwidwa ukapolo nakugwirirani ntchito. 12Koma akakana za mtendere nachita nanu nkhondo, muwuphwanye mzindawo. 13Yehova Mulungu wanu akakupatsani mzindawo, muwaphe amuna onse. 14Akazi, ana, ziweto ndi china chilichonse mu mzindamo, mukhoza kuzitenga kuti zikhale zanu monga katundu wolanda ku nkhondo. Katundu wa adani anuyu amene Yehova Mulungu wanu akukupatsani, mukhoza kumugwiritsa ntchito. 15Mizinda yonse yakutali osati ya mitundu yapafupi, muzichita nayo chomwechi.

16Komabe mʼmizinda imene Yehova Mulungu wanu akukupatsani ngati cholowa chanu, musasiyemo chamoyo chilichonse. 17Muwawononge kwathunthu Ahiti, Aamori, Akanaani, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi monga momwe Yehova Mulungu wanu anakulamulirani. 18Mukapanda kutero adzakuphunzitsani kuti mutengere zinthu zonyansa zimene amachita popembedza milungu yawo ndipo mudzachimwira Yehova Mulungu wanu.

19Mukalimbana ndi mzinda nthawi yayitali, kuchita nawo nkhondo pofuna kuwugonjetsa, musawononge podula mitengo yake ndi nkhwangwa, osayidula chifukwa zipatso zakezo mukhoza kudya. Kodi mitengo ya ku munda ndi anthu kuti mukalimbane nayo? 20Komabe mukhoza kudula mitengo imene mukudziwa kuti si ya zipatso ndi kuyigwiritsa ntchito pa nkhondo mpaka mzinda umene mukumenyana nawowo utagwetsedwa.