Deuteronomo 16 – CCL & NIRV

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Deuteronomo 16:1-22

Paska

1Samalirani mwezi wa Abibu ndi kukondwerera Paska wa Yehova Mulungu wanu, chifukwa pa mwezi wa Abibu, usiku, Iye anakutulutsani mu Igupto. 2Mumuphere Yehova Mulungu wanu nsembe ya Paska, chiweto chochokera pa nkhosa zanu kapena ngʼombe zanu kumalo kumene Yehova adzasankha kuti akhazikeko dzina lake. 3Musadyere pamodzi ndi buledi wopanga ndi yisiti, koma kwa masiku asanu ndi awiri muzidya buledi wopanda yisiti, buledi wa masautso, chifukwa munachoka ku Igupto mwamsangamsanga kuti pa masiku onse a moyo wanu muzikumbukira nthawi imene munanyamukira ku Igupto. 4Yisiti asapezeke kwa masiku asanu ndi awiri pa katundu wanu mʼdziko lanu lonse. Ndipo musasunge nyama imene mwapereka nsembe madzulo a tsiku loyamba mpaka mmawa.

5Musamangopereka nsembe ya Paska mu mzinda wina uliwonse umene Yehova Mulungu wanu wakupatsani, 6koma ku malo wokhawo amene Iye adzawasankhe kukhazikitsako Dzina lake. Kumeneko ndiye muzikapereka nsembe ya Paska madzulo, pamene dzuwa likulowa, pa tsiku lokumbukira kutuluka mu Igupto. 7Muyiwotche ndi kuyidya pa malo pamene Yehova Mulungu wanu adzasankhe. Kenaka mmawa mubwerere ku matenti anu. 8Kwa masiku asanu ndi limodzi muzidya buledi wopanda yisiti ndipo pa tsiku lachisanu ndi chiwiri muzikhala ndi msonkhano wa Yehova Mulungu wanu ndipo musamagwire ntchito iliyonse.

Chikondwerero cha Masabata

9Muziwerenga masabata asanu ndi awiri kuyambira pamene mwatenga chikwakwa ndi kuyamba kumweta tirigu wachilili. 10Pamenepo muzichita Chikondwerero cha Masabata pamaso pa Yehova Mulungu wanu popereka chopereka chaufulu mofanana ndi madalitso amene Yehova Mulungu wakupatsani 11Ndipo inu, ana anu aamuna, aakazi, antchito anu aamuna, adzakazi, Alevi a mʼmizinda mwanu, alendo, ana ndi akazi amasiye okhala pakati panu, mukondwere pamaso pa Yehova Mulungu wanu ku malo amene adzawasankhe kukhazikitsako dzina lake. 12Kumbukirani kuti inunso munali akapolo ku Igupto, ndiye muzitsatira malangizo awa mosamalitsa.

Chikondwerero cha Misasa

13Mukatha kukolola tirigu wanu ndi kupsinya vinyo wanu, muzikhala ndi Chikondwerero cha Misasa kwa masiku asanu ndi awiri. 14Musangalale pa chikondwerero chanu, inu, ana anu aamuna, aakazi, antchito anu aamuna, adzakazi, Alevi, alendo, ana ndi akazi amasiye amene ali mʼmizinda yanu. 15Kwa masiku asanu ndi awiri muzichita chikondwererochi kwa Yehova Mulungu wanu kumalo kumene Yehova adzasankhe. Pakuti Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani inu pa zokolola zanu ndi pa ntchito za manja anu, ndipo chimwemwe chanu chidzakhala chathunthu.

16Amuna onse azionekera pamaso pa Yehova Mulungu katatu pa chaka ku malo amene Iye adzasankha. Pa Chikondwerero cha Buledi wopanda Yisiti, pa Chikondwerero cha Masabata ndi pa Chikondwerero cha Misasa. Munthu aliyense asadzapite pamaso pa Yehova wopanda kanthu mʼmanja mwake. 17Aliyense wa inu adzabweretse mphatso molingana ndi momwe Yehova Mulungu wanu wakudalitsirani.

Oweruza

18Musankhe oweruza ndi akuluakulu a fuko lanu lililonse mu mzinda uliwonse umene Yehova Mulungu wanu akukupatsani, ndipo adzaweruza anthuwa mwachilungamo. 19Musamakhotetse chiweruzo kapena kukondera. Musamalandire chiphuphu pakuti chiphuphu chimadetsa mʼmaso anthu a nzeru ndi kusintha mawu awo kuti mlandu uyipire osalakwa. 20Tsatani chilungamo chokhachokha basi kuti mukhale ndi moyo ndi kutenga dziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani.

Kupembedza Milungu Ina

21Musazike mtengo wina uliwonse wa mafano a Asera pambali pa guwa lansembe la Yehova Mulungu wanu, 22ndipo musayimike mwala wachipembedzo pakuti Yehova Mulungu wanu amadana nazo zimenezi.

New International Reader’s Version

Deuteronomy 16:1-22

The Passover Feast

1Celebrate the Passover Feast of the Lord your God in the month of Aviv. In that month he brought you out of Egypt at night. 2Sacrifice an animal from your flock or herd. It is the Passover sacrifice to honor the Lord your God. Sacrifice it at the special place the Lord will choose. He will put his Name there. 3Don’t eat the animal along with bread made with yeast. Instead, for seven days eat bread made without yeast. It’s the bread that reminds you of how much you suffered. Remember that you left Egypt in a hurry. Remember it all the days of your life. Don’t forget the day you left Egypt. 4Don’t keep any yeast anywhere in your land for seven days. You will sacrifice the Passover animal on the evening of the first day. Do not let any of its meat be left over until the next morning.

5You must not sacrifice the Passover animal in just any town the Lord your God is giving you. 6Sacrifice it only in the special place he will choose for his Name. Sacrifice it there in the evening when the sun goes down. Do it on the same day every year. Be sure it’s the day you left Egypt. 7Cook the animal and eat it. Do it at the place the Lord your God will choose. Then in the morning return to your tents. 8For six days eat bread made without yeast. On the seventh day come together for a service to honor the Lord your God. Don’t do any work on that day.

The Feast of Weeks

9Count off seven weeks from the time you begin to cut your grain in the field. 10Then celebrate the Feast of Weeks to honor the Lord your God. Give to the Lord anything you choose to give as an offering. Give, just as the Lord has given to you. 11Be filled with joy in the sight of the Lord your God. Be joyful at the special place he will choose for his Name. You, your children, and your male and female servants should be joyful. So should the Levites living in your towns. So should the outsiders and widows living among you. And so should the children whose fathers have died. 12Remember that you were slaves in Egypt. Be careful to obey the rules I’m giving you.

The Feast of Booths

13Gather the grain from your threshing floors. Take the fresh wine from your winepresses. Then celebrate the Feast of Booths for seven days. 14Be filled with joy at your feast. You, your children, and your male and female servants should be joyful. So should the Levites, the outsiders, and the widows living in your towns. And so should the children whose fathers have died. 15For seven days celebrate the feast to honor the Lord your God. Do it at the place he will choose. The Lord will bless you when you gather all your crops. He’ll bless you in everything you do. And you will be full of joy. 16All your men must appear in front of the Lord your God at the holy tent. They must go to the place he will choose. They must do it three times a year. They must go there to celebrate the Feast of Unleavened Bread, the Feast of Weeks and the Feast of Booths. None of your men should appear in front of the Lord without bringing something with him. 17Each of you must bring a gift. Give to the Lord your God, just as he has given to you.

Appoint Judges and Officials

18Appoint judges and officials for each of your tribes. Do it in every town the Lord your God is giving you. They must judge the people fairly. 19Do what is right. Treat everyone the same. Don’t take money from people who want special favors. It makes those who are wise close their eyes to the truth. It twists the words of those who have done nothing wrong. 20Do only what is right. Then you will live. You will take over the land the Lord your God is giving you.

Don’t Worship Other Gods

21Don’t set up a wooden pole used to worship the female god named Asherah. Don’t set it up beside the altar you build to worship the Lord your God. 22Don’t set up a sacred stone to honor another god. The Lord your God hates Asherah poles and sacred stones.