Deuteronomo 10 – CCL & PCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Deuteronomo 10:1-22

Miyala Ngati Yoyamba Ija

1Pa nthawi imeneyo Yehova anati kwa ine, “Sema miyala iwiri yofanana ndi yoyamba ija ndipo ubwere nayo kwa Ine ku phiri. Upangenso bokosi lamatabwa. 2Ndidzalembapo mawu amene anali pa miyala yoyamba ija, imene unayiphwanya. Ndipo iwe ukuyenera kuyika miyalayo mʼbokosimo.”

3Choncho ndinapanga bokosi lamatabwa amtengo wa mkesha ndi kusema miyala iwiri yofanana ndi yoyamba ija, ndipo ndinapita ku phiri nditanyamula miyala iwiri mʼmanja mwanga. 4Yehova analemba pa miyala iwiriyo zimene analemba poyamba, Malamulo Khumi amene analengeza kwa inu pa phiri paja, mʼmoto, pa tsiku la msonkhano. Ndipo Yehova anawapereka kwa ine. 5Tsono ndinatsika ku phiri kuja ndi kuyika miyalayo mʼbokosi ndinapanga lija monga Yehova anandilamulira, ndipo panopa ili mʼmenemo.

6Aisraeli anayenda kuchokera ku Beeroti Beni Yaakani mpaka ku Mosera. Kumeneko Aaroni anamwalira nayikidwa mʼmanda, ndipo mwana wake Eliezara anakhala wansembe mʼmalo mwake. 7Kuchokera kumeneko Aisraeli anapita ku Gudigoda, napitirira mpaka ku Yotibata, ku dziko la mitsinje ya madzi. 8Pa nthawi imeneyo Yehova anapatula fuko la Levi kuti anyamule bokosi la pangano la Yehova lija, kuti ayimirire pamaso pa Yehova, kutumikira ndi kunena madalitso pa dzina lake monga amachitira mpaka lero. 9Nʼchifukwa chake Alevi alibe gawo kapena cholowa pakati pa abale awo. Yehova ndiye cholowa chawo monga momwe Yehova Mulungu wanu anawawuzira.

10Tsopano ndinakhala ku phiri kuja kwa masiku makumi anayi usana ndi usiku monga ndinachitira poyamba, ndipo Yehova anandimveranso nthawi iyi. Sichinali chifuniro chake kuti akuwonongeni. 11Yehova anati kwa ine, “Pita ndi kutsogolera anthuwa pa njira yawo, kuti alowe ndi kulandira dziko limene ndinalumbira kwa makolo awo kuti ndiwapatse.”

Kuopa Yehova

12Tsopano inu Aisraeli, nʼchiyani chimene Yehova afuna kwa inu? Iye akufuna kuti muzimuopa poyenda mʼnjira zake zonse ndi kumamukonda Iye, kumutumikira Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse, 13ndi kusunga malamulo ndi malangizo amene ndikukupatsani lero kuti zizikuyenderani bwino.

14Yehova Mulungu wanu ndiye mwini wake kumwamba ngakhale mmwambamwamba, dziko lapansi ndi zonse zimene zili mʼmenemo. 15Yehova anayika mtima wake pa makolo anu okha ndipo anawakondadi nasankha adzukulu awo mwa mitundu yonse pa dziko lapansi, kunena inuyo monga mulili lero. 16Motero chitani mdulidwe wa mitima yanu ndipo musakhalenso opulupudza. 17Pakuti Yehova Mulungu wanu ndi Mulungu wa milungu, Ambuye wa ambuye, Mulungu wamkulu, wamphamvu ndi woopsa, amene sakondera ndipo salandira ziphuphu. 18Iye amatchinjiriza ana amasiye ndi akazi amasiye, ndipo amakonda mlendo namupatsa chakudya ndi chovala. 19Muzikonda alendo popeza inuyo munali alendo mʼdziko la Igupto. 20Muziopa Yehova Mulungu wanu ndi kumutumikira Iye. Mumukakamire Iyeyo ndi kuchita malumbiro anu mʼdzina lake. 21Iye ndiye matamando anu, Mulungu wanu amene anakuchitirani zodabwitsa zazikulu ndi zoopsa zimene munaona ndi maso anu zija. 22Makolo anu amene anapita ku Igupto analipo makumi asanu ndi awiri onse pamodzi, ndipo tsopano Yehova Mulungu wanu wakuchulukitsani ngati nyenyezi zakumwamba.

Persian Contemporary Bible

تثنيه 10:1-22

ده فرمان بار ديگر نوشته می‌شود

(خروج 34‏:1‏-10)

1در آن هنگام خداوند به من فرمود: «دو لوح سنگی ديگر مانند لوحهای قبلی بتراش و يک صندوق چوبی برای نگهداری آنها بساز و لوحها را همراه خود نزد من به كوه بياور. 2من روی آن لوحها همان فرامينی را كه روی لوحهای اولی بود و تو آنها را شكستی، دوباره خواهم نوشت. آنگاه آنها را در صندوق بگذار.»

3بنابراين من يک صندوق از چوب اقاقيا ساخته، دو لوح سنگی مانند لوحهای اول تراشيدم و لوحها را برداشته، از كوه بالا رفتم. 4خدا دوباره ده فرمان را روی آنها نوشت و آنها را به من داد. (آنها همان فرامينی بودند كه وقتی همگی شما در پايين كوه جمع شده بوديد، از درون آتش روی كوه به شما داده بود.)

5آنگاه از كوه پايين آمدم و طبق فرمان خداوند لوحها را در صندوقی كه ساخته بودم گذاشتم. آن لوحها تا امروز هم در آنجا قرار دارند.

6سپس قوم اسرائيل از بئيروت بنی‌يعقان به موسيره كوچ كردند. در آنجا هارون درگذشت و مدفون گرديد و پسرش العازار به جای او به خدمت كاهنی پرداخت. 7آنگاه به جُدجوده و از آنجا به يُطبات كه نهرهای فراوانی داشت، سفر كردند. 8در آنجا بود كه خداوند قبيلهٔ لاوی را برای حمل صندوقی كه در آن ده فرمان خداوند قرار داشت انتخاب نمود تا در حضور او بايستند و او را خدمت كنند و به نام او بركت دهند، به طوری که تا امروز هم اين كار را انجام می‌دهند. 9(به همين دليل است كه برای قبيلهٔ لاوی مثل قبايل ديگر سهمی در سرزمين موعود در نظر گرفته نشده است، زيرا همچنانكه خداوند به ايشان فرمود او خود ميراث ايشان است.)

10چنانكه قبلاً هم گفتم برای دومين بار چهل شبانه روز در حضور خداوند در بالای كوه ماندم و خداوند بار ديگر التماس‌های مرا اجابت فرمود و از نابود كردن شما صرفنظر نمود. 11او به من فرمود: «برخيز و بنی‌اسرائيل را به سرزمينی كه به پدرانشان وعده داده‌ام هدايت كن تا به آنجا داخل شده، آن را تصاحب كنند.»

انتظار خدا از قوم اسرائيل

12‏-13اكنون ای قوم اسرائيل، خداوند از شما چه می‌خواهد، جز اينكه به سخنان او به دقت گوش كنيد و برای خير و آسايش خود، فرامينی را كه امروز به شما می‌دهد اطاعت كنيد و او را دوست داشته، با تمامی دل و جان او را پرستش كنيد.

14زمين و آسمان از آن خداوند، خدای شماست؛ 15با وجود اين، او آنقدر به پدرانتان علاقمند بود و به حدی ايشان را دوست می‌داشت كه شما را كه فرزندان آنها هستيد انتخاب نمود تا بالاتر از هر قوم ديگری باشيد، همچنانكه امروز آشكار است. 16بنابراين دست از سركشی برداريد و با تمام دل، مطيع خداوند شويد.

17خداوند، خدايتان، خدای خدايان و رب الارباب است. او خدايی بزرگ و تواناست، خدای مهيبی كه از هيچكس جانبداری نمی‌كند و رشوه نمی‌گيرد. 18به داد بيوه‌زنان و يتيمان می‌رسد. 19غريبان را دوست می‌دارد و به آنها غذا و لباس می‌دهد. (شما هم بايد غريبان را دوست بداريد، زيرا خودتان هم در سرزمين مصر غريب بوديد.) 20بايد از خداوند، خدايتان بترسيد و او را پرستش كنيد و از او جدا نشويد و فقط به نام او سوگند ياد كنيد. 21او فخر شما و خدای شماست، خدايی كه معجزات عظيمی برای شما انجام داد و خود شاهد آنها بوده‌ايد. 22وقتی كه اجداد شما به مصر رفتند فقط هفتاد نفر بودند، ولی اكنون خداوند، خدايتان شما را به اندازهٔ ستارگان آسمان افزايش داده است!