Deuteronomo 1 – CCL & CCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Deuteronomo 1:1-46

Mose Akumbutsa Aisraeli za ku Horebu

1Awa ndi mawu amene Mose anayankhula kwa Aisraeli onse mʼchipululu kummawa kwa Yorodani, ku Araba moyangʼanana ndi Sufi, pakati pa Parani ndi Tofeli, Labani, Heziroti ndi Dizahabu. 2(Kuyenda kuchokera ku Horebu kukafika ku Kadesi Barinea kudzera njira ya ku Phiri la Seiri ndi ulendo wa masiku khumi ndi limodzi).

3Mʼchaka cha makumi anayi, pa tsiku loyamba la mwezi 11, Mose anafotokozera Aisraeli zonse zimene Yehova anamulamula zokhudza iwowo. 4Apa nʼkuti atagonjetsa Sihoni mfumu ya Aamori, amene amalamulira ku Hesiboni, ndipo pa Ederi anagonjetsa Ogi mfumu ya ku Basani, amene amalamulira mu Asiteroti.

5Chakummawa kwa Yorodani mʼchigawo cha Mowabu, Mose anayamba kufotokozera lamulo ili kunena kuti:

6Ku Horebu, Yehova Mulungu wathu anati kwa ife, “Mwakhalitsa pa phiri lino. 7Sasulani msasa ndipo pitani ku dziko la mapiri la Aamori. Pitani kwa anthu onse oyandikana nawo ku Araba, ku mapiri, mʼmbali mwa mapiri a ku madzulo, ku Negevi ndiponso mʼmbali mwa nyanja, ku dziko la Akanaani ndi ku Lebanoni mpaka ku mtsinje waukulu wa Yufurate. 8Taonani, Ine ndakupatsani dziko ili. Lowani ndi kulilanda dziko limene Yehova analumbira kuti adzapereka kwa makolo anu, Abrahamu, Isake ndi Yakobo komanso kwa zidzukulu zawo.”

Kukhazikitsa Atsogoleri

9Pa nthawi imeneyi ine ndinati kwa inu, “Inu ndinu katundu olemera kwambiri woti sindingathe kumunyamula ndekha. 10Yehova Mulungu wanu wakuchulukitsani kotero kuti lero lino ndinu ochuluka ngati nyenyezi za kumwamba. 11Yehova Mulungu wa makolo anu wachulukitsa chiwerengero chanu ndipo wakudalitsani monga momwe analonjezera! 12Koma nanga ndekha ndidzasenza bwanji zovuta ndi zipsinjo zanu komanso milandu yanu? 13Sankhani amuna ena anzeru, ozindikira ndi amene mumawalemekeza kuchokera ku mtundu uliwonse wa mitundu yanu, ndipo ndidzawayika kuti akulamulireni.”

14Inu munandiyankha kuti, “Maganizo amenewa ndi abwino kuwachita.”

15Choncho ndinatenga anthu otsogolera mafuko anu, anzeru ndi omwe mumawalemekeza, ndipo ndinawayika kuti azikulamulirani mʼmagulu a 1,000, ena 100, ena makumi asanu ndi ena khumi, kuti akhalenso ngati akapitawo a mafuko. 16Ndipo pa nthawi imeneyo ndinawawuza olamula anu kuti, “Muzimva milandu ya pakati pa abale anu ndi kuweruza mosakondera, kaya mlanduwo uli pakati pa Aisraeli okhaokha kapena mmodzi wa iwo ndi mlendo. 17Osamayangʼana nkhope poweruza koma muzimvetsera aangʼono ndi aakulu omwe chimodzimodzi. Musamaope munthu aliyense, pakuti chiweruzo ndi cha Mulungu. Muzindibweretsera mlandu uliwonse wovuta ndipo ndidzaumva.” 18Ndipo nthawi imeneyo ndinakuwuzani chilichonse chimene munayenera kuchita.

Atumizidwa Kukazonda Dziko

19Tsono monga Yehova Mulungu wathu anatilamulira, tinanyamuka kuchoka ku Horebu ndi kupita cha ku dziko lamapiri la Aamori kudzera ku chipululu chachikulu ndi choopsa chija munachionachi, kotero kuti tinakafika ku Kadesi Barinea. 20Ndipo ndinati kwa inu, “Mwafika ku dziko la mapiri la Aamori, limene Yehova Mulungu wathu akutipatsa. 21Taonani, Yehova Mulungu wanu wakupatsani dzikoli. Pitani ndi kulitenga monga Yehova, Mulungu wa makolo anu anakuwuzirani. Musaope kapenanso kugwa mphwayi.”

22Tsono nonse munabwera kwa ine ndi kuti, “Tiyeni titumize anthu ayambe apita kuti akazonde dzikolo ndi kutibweretsera mawu pa za njira yomwe tidzere ndi za mizinda imene tikafikireko.”

23Ndinaona kuti maganizo amenewa anali abwino, choncho ndinasankha anthu khumi ndi awiri, mmodzi ku fuko lililonse. 24Iwo ananyamuka napita mʼdziko la mapiri, ndipo anafika ku Chigwa cha Esikolo ndi kukazonda dzikolo. 25Pobwerera anatitengerako zipatso za mʼdzikomo ndipo anatipatsa mawu akuti, “Dziko limene Yehova Mulungu wathu akutipatsa ndi labwino.”

Awukira Yehova

26Koma inu simunafune kupitako ndipo munawukira lamulo la Yehova Mulungu wanu. 27Inu munanyinyirika mʼmatenti anu nʼkumati, “Mulungu amatida nʼchifukwa chake anatitulutsa ku Igupto kuti atipereke mʼmanja mwa Aamori kuti atiwononge. 28Tigwire mtengo wanji? Abale athu anatitayitsa mtima. Iwo akuti, ‘Anthuwo ndi amphamvu ndi aatali kuposa ife, mizindayo ndi yayikulu ndipo mipanda yake ndi yayitali yofika kumwamba. Ife tinaonanso Aanaki kumeneko.’ ”

29Ndipo ine ndinati kwa inu, “Musachite mantha kapena kuwaopa. 30Yehova Mulungu wanu, amene akukutsogolerani, adzakumenyerani nkhondo monga muja anachitira ku Igupto inu mukuona, 31ndi mʼchipululu muja. Kumeneko munaona mmene Yehova Mulungu wanu anakunyamulirani monga abambo anyamulira mwana wawo, njira yonse yomwe munayenda mpaka munafika pamalo ano.”

32Ngakhale zinali choncho, simunadalire Yehova Mulungu wanu 33amene anakutsogolerani pa ulendo wanu, ndi moto nthawi ya usiku ndi mtambo nthawi ya masana, kukufunirani malo woti mumange msasa ndi kukuonetsani njira yoti muyendemo.

34Yehova atamva zimene munanena anakwiya nalumbira kuti, 35“Palibe ndi mmodzi yemwe mwa mʼbado woyipawu amene adzaona dziko labwino limene ndinalumbira kupatsa makolo anu, 36kupatula Kalebe mwana wa Yefune. Iye adzaliona, ndipo ndidzamupatsa iye ndi adzukulu ake, dziko limene adzapondamo popeza anatsata Yehova ndi mtima wake wonse.”

37Chifukwa cha inu, Yehova anakwiyiranso ine ndipo anati, “Iwenso sudzalowa mʼdzikomo. 38Koma Yoswa mwana wa Nuni amene amakuthandiza, adzalowa mʼdzikomo. Umulimbikitse chifukwa adzatsogolera Israeli kukalandira dzikolo. 39Ndipo angʼonoangʼono amene munati adzagwidwa ukapolo, ana anu amene sanadziwe kusiyanitsa chabwino ndi choyipa, amenewo adzalowa mʼdzikolo. Ndidzalipereka kwa iwo ndipo lidzakhala lawo. 40Koma inu, tembenukani nyamukani kulowera cha ku chipululu kutsatira njira ya ku Nyanja Yofiira.”

41Ndipo inuyo munati, “Tachimwa pamaso pa Yehova. Tipita ndi kukachita nkhondo monga Yehova Mulungu wathu watilamulira.” Choncho aliyense wa inu anavala zankhondo, ndi kuganiza kuti nʼkosavuta kupita mʼdziko la mapiri lija.

42Koma Yehova anandiwuza kuti, “Awuze anthuwa kuti, ‘Musapite kukachita nkhondo chifukwa Ine sindidzakhala nanu. Mudzagonjetsedwa ndi adani anu.’ ”

43Choncho ndinakuwuzani koma simunamve. Inu munawukira lamulo la Yehova ndipo mwamwano munayenda kulowa mʼdziko la mapiri. 44Aamori amene ankakhala mʼmapiriwo anatuluka kukakumana nanu ndipo anakuthamangitsani ngati gulu la njuchi ndipo anakukanthani kuchokera ku Seiri, njira yonse mpaka ku Horima. 45Munabwererako mukulira pamaso pa Yehova, koma Iye sanalabadire kulira kwanuko ndipo sanakumvetsereni. 46Pamenepo munakhala ku Kadesi masiku ambiri kwa nthawi yayitali ndithu.

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

申命记 1:1-46

前言

1以下是摩西以色列人说的话。当时以色列人在约旦河东的旷野、疏弗对面的亚拉巴,即巴兰陀弗拉班哈洗录底撒哈之间。 2何烈山取道西珥山到加低斯·巴尼亚,需十一天。 3在离开埃及后第四十年的十一月一日,摩西把耶和华的一切吩咐告诉了以色列人。 4那时,他已经打败了希实本亚摩利西宏以及盘踞在以得来亚斯她录巴珊5摩西约旦河东的摩押讲解律法,说: 6“我们的上帝耶和华在何烈山对我们说,‘你们在这里已经住了多日, 7现在该启程前往亚摩利人的山区、亚拉巴地区、山地、丘陵、南地、沿海一带、迦南黎巴嫩,直到幼发拉底河。 8看啊,我把那片土地赐给你们了,你们去占领吧,那是耶和华起誓赐给你们祖先亚伯拉罕以撒雅各和他们后裔的地方。’

摩西设立首领

9“那时,我对你们说,‘我无法独自承担管理你们的重任, 10因为你们的上帝耶和华使你们人丁兴旺,以致今天人数多如天上的星星。 11愿你们祖先的上帝耶和华使你们人数更增千倍,照祂的应许赐福给你们。 12但我怎能独自担当解决你们问题和争端的重任呢? 13你们要从各支派中选出有智慧、有见识、受尊重的人,我要立他们做你们的首领。’ 14你们都同意这样的做法。 15于是,我把各支派中有智慧和受敬重的人立为你们的首领,即千夫长、百夫长、五十夫长、十夫长和其他官长,治理你们。 16我吩咐这些官员要聆听案件,公正地审理同胞之间或与外族人之间的诉讼, 17不可偏私,不分贵贱,不惧情面,因为判决来自上帝。如果案件太难,可以交给我处理。 18那时,我把一切当行之事都告诉了你们。

派人打探迦南

19“我们照我们上帝耶和华的吩咐,从何烈山出发,走过你们所见的那大而可怕的旷野,前往亚摩利山区,来到加低斯·巴尼亚20我对你们说,‘我们的上帝耶和华赐给我们的亚摩利山区到了。 21看啊,你们祖先的上帝耶和华已把那片土地赐给你们,你们要照着祂的应许去占领那里,不要惧怕,不要气馁。’ 22你们来对我说,‘我们要先派人去打探那地方,回来好告诉我们当走哪条路,当占哪些城。’ 23我同意你们的建议,便从你们当中选出十二人,每支派选一人。 24他们前往山区,到了以实各谷,打探那地方。 25他们带回来一些那里的果子,禀告说,‘我们的上帝耶和华赐给我们的地方很好。’

26“但你们却违背你们上帝耶和华的命令,不肯上去。 27你们在帐篷中埋怨说,‘耶和华憎恨我们,所以才领我们离开埃及,要把我们交在亚摩利人手里,让他们消灭我们。 28我们怎能上去呢?那些弟兄的报告令我们胆战心惊,他们说那里的人比我们高大,城邑雄伟,城墙高达云霄,还有亚衲人在那里。’ 29我对你们说,‘不要惊慌,不要怕他们。 30你们的上帝耶和华必带领你们,为你们争战,正如祂当着你们的面在埃及所行的一样。 31你们在旷野曾目睹你们的上帝耶和华像父亲抱儿子一样,一路把你们抱到这地方。’ 32-33祂为你们开路,为你们找安营的地方,夜间用火柱、白天用云柱为你们引路。尽管如此,你们还是不信靠你们的上帝耶和华。

惩罚叛逆

34“你们的埋怨惹耶和华发怒,祂起誓说, 35‘这邪恶的一代没有一人能看见我起誓要赐给他们祖先的佳美之地, 36只有耶孚尼的儿子迦勒能看见,我必把他所踏之地赐给他和他的后代,因为他全心全意地跟从我。’ 37因为你们的缘故,耶和华也向我发怒,说,‘你也不能进入那片土地, 38但你的助手——的儿子约书亚可以进入。你要鼓励他,因为他将带领以色列承受那片土地。 39你们说你们的子女会被掳去,但这些还不知善恶的孩子都将进入那片土地,我要把那里赐给他们,他们将占领那里。 40而你们要掉头,沿红海的路回到旷野。’

41“于是,你们对我说,‘我们得罪了耶和华,现在我们愿意遵从我们的上帝耶和华的吩咐,上去作战。’你们便各自拿起兵器,以为可以轻易攻占山区。 42但耶和华让我告诉你们,‘不要上去作战,以免被敌人击败,因为耶和华不会与你们同在。’ 43我把耶和华的话转告了你们,但你们不听,违背耶和华的命令,擅自前往山区。 44住在山区的亚摩利人蜂拥出击,打败了你们,从西珥追杀你们,一直追到何珥玛45你们回来在耶和华面前哭泣,但耶和华不理会你们的哭声。 46因此,你们在加低斯住了很久。