Danieli 9 – CCL & CARS

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Danieli 9:1-27

Pemphero la Danieli

1Mʼchaka choyamba cha Dariyo mwana wa Ahasiwero (wochokera kwa Amedi), amene anakhala mfumu ya ku Babuloni, 2ine Danieli ndinazindikira powerenga mawu a Yehova opatsidwa kwa mneneri Yeremiya, kuti Yerusalemu adzakhala bwinja kwa zaka 70. 3Choncho ndinatembenukira kwa Ambuye Mulungu ndipo ndinamudandaulira ndi kupempha posala kudya, ndi kuvala chiguduli ndi kudzola phulusa.

4Ndinapemphera kwa Yehova Mulungu wanga ndi kuvomereza kuti tinachimwa:

Ndinati, “Inu Ambuye, Mulungu wamkulu ndi woopsa, amene mumasunga pangano lanu la chikondi kwa onse amene amakukondani ndi kumvera malamulo anu, 5tachimwa ndipo tachita zolakwa ndi zoyipa. Takuwukirani posiya malangizo ndi malamulo anu. 6Sitinamvere aneneri atumiki anu, amene anayankhula mʼdzina lanu kwa mafumu athu, kwa akalonga athu, makolo athu, ndi kwa anthu onse a mʼdziko.

7“Ambuye ndinu olungama, koma lero tili ndi manyazi, ife anthu a ku Yuda, a ku Yerusalemu ndi Israeli yense, apafupi ndi akutali omwe, ku mayiko onse kumene munatipirikitsira chifukwa cha kusakhulupirika kwathu. 8Inu Yehova, ife ndi mafumu athu, akalonga athu ndi makolo athu tili ndi manyazi chifukwa takuchimwirani. 9Ambuye Mulungu wathu ndi wachifundo ndi wokhululuka, ngakhale kuti tamuwukira: 10Ife sitinamvere Yehova Mulungu wathu kapena kusunga malamulo ake amene anatipatsa kudzera mwa aneneri atumiki ake. 11Aisraeli onse anachimwira lamulo lanu motero anapatuka, nakana kukumverani.

“Choncho matemberero ndi olumbira amene alembedwa mʼmalamulo a Mose, mtumiki wa Mulungu, atigwera chifukwa takuchimwirani. 12Inu mwakwaniritsa mawu amene munayankhula otitsutsa ife ndi otsutsa otilamulira potibweretsera tsoka lalikulu. Pa dziko lapansi sipanachitikenso zinthu ngati zimene zaonekera Yerusalemu. 13Monga kunalembedwa mʼMalamulo a Mose, tsoka lililonse latifikira chikhalirecho sitinapemphe Yehova Mulungu wathu kuti atikomere mtima. Sitinasiye machimo athu, ndipo sitinasamale choonadi chanu. 14Choncho Yehova anakonza kuti atigwetsere tsoka limeneli, ndipo wachitadi popeza Yehova Mulungu wathu ndi wolungama mu chilichonse amachita; chikhalirecho ife sitinamumvere.

15“Inu Ambuye Mulungu wathu, munatulutsa anthu anu ku Igupto ndi dzanja lanu lamphamvu ndipo dzina lanu ndi lotchuka mpaka lero. Ife tachimwa, tachita zolakwa. 16Inu Ambuye, molingana ndi zochita zanu zolungama, tikukupemphani kuti muchotse mkwiyo ndi ukali wanu pa Yerusalemu mzinda wanu, phiri lanu loyera. Machimo athu ndi mphulupulu za makolo athu zachititsa kuti onse otizungulira atonze Yerusalemu ndi anthu anu.

17“Tsopano Mulungu wathu, imvani mapemphero ndi zopempha za mtumiki wanu. Kuti anthu onse akudziweni kuti ndinu Ambuye, komerani mtima malo anu opatulika amene asanduka bwinja. 18Tcherani khutu, Inu Mulungu, ndipo imvani; tsekulani maso anu ndipo onani mabwinja athu ndi mzinda umene umadziwika ndi dzina lanu. Sitikupempha chifukwa chakuti ndife olungama, koma chifukwa cha kukula kwa chifundo chanu. 19Inu Ambuye imvani mawu athu! Ambuye khululukani! Ambuye timvereni, ndipo muchitepo kanthu! Kuti anthu adziwe kuti Inu ndinu Mulungu wanga musachedwe chifukwa mzinda wanu ndi anthu anu amadziwika ndi dzina lanu.”

Zaka 70

20Ndikuyankhula ndi kupemphera, kuvomereza machimo anga ndi machimo a anthu anga Aisraeli ndi kupempherera phiri lake loyera kwa Yehova Mulungu wanga, 21Gabrieli, munthu uja amene ndinamuona mʼmasomphenya poyambirira, anabwera kwa ine mowuluka. Iyi inali nthawi ya nsembe ya madzulo. 22Anandilangiza kuti, “Danieli ndabwera tsopano kuti ndikupatse nzeru kuti uzitha kumvetsa zinthu. 23Utangoyamba kupemphera, Mulungu anayankha. Tsono ine ndabwera kudzakuwuza yankholo, popeza ndiwe wokondedwa kwambiri. Choncho mvetsetsa pamene ndikufotokoza za zinthu zimene unaziona mʼmasomphenya.

24“Zaka 490 zinayikidwa kuti anthu a mtundu wako ndi mzinda wanu woyera aleke zoyipa, asiye tchimo. Iwo adzapereka dipo kupepesera zolakwa zawo. Zikadzatero anthu adzaonetsa moyo wachilungamo nthawi zonse. Izi zidzatsimikiza zimene unaziona mʼmasomphenya zija ndi zimene ananenera aneneri. Malo opatulika adzakhazikitsidwa.

25“Tsono udziwe ndipo uzindikire izi kuti kuyambira pamene lamulo linaperekedwa kuti Yerusalemu akonzedwenso mpaka pamene mfumu Yodzozedwa idzafike padzapita zaka 49. Pa zaka 434 mzinda wa Yerusalemu udzamangidwanso, ndipo mabwalo ndi ngalande zake zidzatetezedwa. Koma nthawiyi idzakhala ya masautso. 26Patatha zaka 434, Wodzozedwayo adzaphedwa ndipo sadzakhala ndi aliyense. Anthu a wolamulira amene adzabwere adzawononga mzinda ndi Nyumba ya Mulungu. Kutha kwake kudzafika ngati chigumula. Komabe nkhondo idzapitirira mpaka chiwonongeko chimene Mulungu ananeneratu chitachitika. 27Adzachita pangano lolimba ndi anthu ambiri kwa zaka zisanu ndi ziwiri. Koma pakatinʼpakati pa sabata limodzilo iye adzaletsa kupereka nsembe ndi chopereka. Chonyansa chosakaza chija adzachiyika mʼNyumba ya Mulungu, ndipo chidzakhalapobe mpaka wochita zimenezi atalangidwa ndi chiwonongeko chimene Mulungu ananeneratu.”

Священное Писание

Даниял 9:1-27

Молитва Данияла

1В первый год Дария, сына Ксеркса9:1 Букв.: «Ахашвероша» – еврейский вариант персидского имени Ксеркс. Личность этого человека, отличающегося от царя Ксеркса книги Есфирь, точно не установлена., родом мидянина, который был сделан правителем Вавилонского царства, – 2в первом году его правления (в 539 г. до н. э.) я, Даниял, понял из Писания, по слову Вечного9:2 Вечный – на языке оригинала: «Яхве». Под этим именем Всевышний открылся Мусе и народу Исраила (см. Исх. 3:13-15). См. пояснительный словарь. к пророку Иеремии, что запустение Иерусалима продлится семьдесят лет9:2 См. Иер. 25:11-12; 29:10.. 3Тогда я обратился к Владыке Всевышнему с молитвой и прошением, в посте, одетый в рубище, с головой, посыпанной пеплом.

4Я молился Вечному, моему Богу, и каялся:

– Владыка, Бог великий и грозный, верный соглашению любви со всеми, кто любит Тебя и исполняет Твои повеления, 5мы согрешили и сделали зло. Мы были нечестивы и мятежны; мы отвернулись от Твоих повелений и законов. 6Мы не слушали Твоих рабов пророков, говоривших от Твоего имени нашим царям, вождям, предкам и всему народу страны.

7Владыка, Ты праведен, а мы сегодня покрыты стыдом – народ Иудеи, жители Иерусалима и весь Исраил, те, кто близко, и те, кто далеко, во всех странах, куда Ты рассеял нас из-за нашей неверности Тебе. 8Вечный, мы и наши цари, вожди и предки покрыты стыдом из-за того, что согрешили против Тебя. 9Владыка, наш Бог, Ты милостив и готов прощать, пусть мы и восставали против Тебя; 10мы не слушали Тебя, Вечный, наш Бог, и не соблюдали законы, которые Ты дал нам через Своих рабов пророков. 11Весь Исраил нарушил Твой Закон и отвернулся, отказываясь слушаться Тебя.

Поэтому на нас излились проклятия и клятвы, записанные в Законе Мусы, раба Всевышнего, ведь мы согрешили против Тебя. 12Ты исполнил слова, сказанные против нас и против наших правителей, наведя на нас великую беду. Под всем небом никогда не случалось того, что случилось с Иерусалимом. 13Как и написано в Законе Мусы, эта беда пришла к нам, но мы всё-таки не искали Твоей милости, Вечный, наш Бог, не оставили грехов и не размышляли о Твоей истине. 14Ты не поколебался навести на нас эту беду, потому что Ты, Вечный, наш Бог, праведен во всём, что делаешь; и всё-таки мы не слушались Тебя.

15И ныне, Владыка, Бог наш, выведший Свой народ из Египта могучей рукой и сделавший Себе имя, которое славно и сегодня, мы согрешили, мы сделали зло. 16Владыка, ради всей праведности Твоей, молю, отврати Свой гнев и негодование от Иерусалима, Твоего города, Твоей святой горы. Из-за наших грехов и беззаконий наших отцов Иерусалим и Твой народ в презрении у всех, кто его окружает.

17И ныне, Бог наш, услышь молитвы и прошения Твоего раба. Ради Себя Самого, Владыка, взгляни с благоволением на Твоё опустошённое святилище. 18Услышь, Бог мой, и внемли; открой глаза и погляди на запустение города, в котором Ты пребываешь. Мы просим Тебя не ради нашей праведности, но ради Твоей великой милости. 19Владыка, услышь! Владыка, прости! Владыка, внемли и соверши! Ради Самого Себя, Бог мой, не медли, ведь над Твоим городом и Твоим народом провозглашено Твоё имя.

Объяснение тайны о семидесяти семилетиях

20Когда я говорил и молился, признавая свой грех и грех моего народа Исраила, и молил Вечного, моего Бога, о Его святой храмовой горе – 21когда я ещё молился, ангел Джабраил, которого я видел в предыдущем видении, явился ко мне, быстро прилетев во время вечерней жертвы9:21 То есть примерно в три часа пополудни (см. Исх. 29:38-41; Чис. 28:3-8).. 22Он объяснил мне:

– Даниял, я пришёл сейчас, чтобы дать тебе мудрость и понимание. 23Едва лишь ты начал молиться, был дан ответ, который я и пришёл возвестить, потому что ты любим Всевышним. Итак, вникни в эту весть и пойми видение.

24Семьдесят семилетий9:24 То есть 490 лет. Семилетие – букв.: «седмица». Здесь и далее в этой главе имеется в виду период в 7 лет (ср. 10:2-3, где имеется в виду неделя). установлены для твоего народа и святого города Иерусалима, чтобы прекратить преступления, положить конец грехам, искупить беззакония, привести вечную праведность, запечатать и видение, и пророка и помазать Святая Святых9:24 Святая Святых – внутренняя комната в храме. Другой перевод: «Самого Святого»..

25Знай и пойми: от повеления восстановить и отстроить Иерусалим до прихода Правителя-Помазанника9:25 Помазанник («Машиах» (евр.), «Масих» (араб.), «Христос» (греч.)) – здесь пророчество об Исе Масихе, праведном Царе, Освободителе и Спасителе. пройдёт семь семилетий и шестьдесят два семилетия. Город будет отстроен с улицами и со рвом, но в трудные времена. 26После шестидесяти двух семилетий Помазанник будет предан смерти, и у Него ничего не останется9:26 Или: «у Него не будет никого»; или: «хотя не будет на Нём вины»; или: «Его не будет».. Народ вождя, который придёт, разрушит город и святилище. Конец вождя9:26 Или: «города». придёт подобно наводнению, и до конца предустановлены война и опустошения. 27Он заключит прочный союз со многими на семь лет, а в середине семилетия прекратит жертву и приношение. На крыле святилища будет осквернение, что ведёт к опустошению9:27 Это пророчество, о котором упоминал Сам Иса Масих (см. Мат. 24:15; Мк. 13:14), частично исполнилось в 70 г., когда храм был разрушен римлянами, но полностью оно сбудется в конце времён (см. 2 Фес. 2:3-4; Отк. 11:2). См. также 11:31 со сноской и 12:11., пока предопределённый конец не постигнет опустошителя.