Danieli 6 – CCL & NIV

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Danieli 6:1-28

Danieli Mʼdzenje la Mikango

1Kunamukomera Dariyo kusankha akalonga 120 kuti alamulire mu ufumu wonse, 2ndikusankha nduna zazikulu zitatu kuti ziwayangʼanire ndipo imodzi mwa ndunazo anali Danieli. Akalongawo amayangʼaniridwa ndi nduna zazikuluzo kuti zinthu za mfumu zisawonongeke. 3Tsono Danieli anadzionetsa kuti akhoza kugwira ntchito bwino kopambana nduna zinzake chifukwa anali wanzeru kwambiri. Ndiye mfumu inaganiza zomuyika kuti akhale woyangʼanira ufumu wonse. 4Chifukwa cha ichi, anzake ndi akalonga anayesa kupeza zifukwa zomutsutsira Danieli pa kayendetsedwe ka ntchito za dzikolo, koma sanapeze cholakwa chilichonse. Iwo sanapeze chinyengo mwa iye, chifukwa anali wokhulupirika ndipo sankachita chinyengo kapena kutayirira ntchito. 5Pomaliza, anthu awa ananena kuti, “Sitidzapeza cholakwa chilichonse chomutsutsira Danieli kupatula chokhacho chimene chikhudza chipembedzo cha Mulungu wake.”

6Choncho akalonga ndi nduna pamodzi anapita kwa mfumu ndipo anati: “Inu mfumu Dariyo, mukhale ndi moyo wautali! 7Nduna zoyendetsa ufumu wanu, aphungu, akalonga ndi abwanamkubwa tonse tagwirizana kuti inu mfumu mukhazikitse lamulo ndi kulisindikiza kuti aliyense amene apemphera kwa mulungu wina kapena kwa munthu kupatula kwa inu mfumu, pa masiku makumi atatu otsatirawa, adzaponyedwa mʼdzenje la mikango. 8Tsopano inu mfumu khazikitsani lamulo limeneli ndipo musindikizepo dzina lanu kuti lisasinthike monga mwa malamulo a Amedi ndi Aperezi, amene sasinthidwa.” 9Choncho mfumu Dariyo anasindikizapo dzina lake pa lamuloli.

10Danieli atamva kuti lamulo lasindikizidwa, anapita ku nyumba kwake nalowa mʼchipinda chapamwamba chimene mazenera ake anali otsekula kuloza ku Yerusalemu. Katatu pa tsiku iye ankagwada pansi pa mawondo ndipo amapemphera, kuyamika Mulungu wake, monga momwe ankachitira kale. 11Ndipo anthu awa anapita pamodzi ndi kukapeza Danieli akupemphera ndi kupempha Mulungu wake kuti amuthandize. 12Kotero iwo anapita kwa mfumu ndipo anayankhula naye za lamulo lake kuti, “Kodi simunasindikize lamulo lakuti pa masiku makumi atatu otsatirawa aliyense amene apemphera kwa mulungu wina aliyense kapena kwa munthu kupatula kwa inu mfumu, adzaponyedwa mʼdzenje la mikango?”

Mfumu inayankha kuti, “Lamulo lilipobe monga mwa malamulo a Amedi ndi Aperezi, amene sangathe kusinthika.”

13Kenaka iwo anati kwa mfumu, “Danieli, amene ndi mmodzi mwa akapolo ochokera ku Yuda, sakulabadira inu mfumu, kapena lamulo limene munasindikizapo dzina lanu lija. Iye akupempherabe katatu pa tsiku.” 14Mfumu itamva izi, inavutika kwambiri mu mtima mwake. Iyo inayesa kupeza njira yopulumutsira Danieli. Iyo inachita chotheka chilichonse kufikira kulowa kwa dzuwa kuti imupulumutse.

15Ndipo anthuwo anapita pamodzi kwa mfumu ndipo anati kwa iye, “Kumbukirani, inu mfumu kuti monga mwa lamulo la Amedi ndi Aperezi, palibe chimene mfumu inalamulira kapena kukhazikitsa chimasinthidwa.”

16Choncho mfumu inalamula, ndipo anabwera naye Danieli ndi kukamuponya mʼdzenje la mikango. Mfumu inati kwa Danieli, “Mulungu wako amene umutumikira nthawi zonse, akupulumutse!”

17Anatenga mwala natseka pa khoma pa dzenje la mikango, ndipo mfumu inadindapo chizindikiro chake ndi cha nduna zake kuti wina asasinthepo kanthu pa za Danieli. 18Kenaka mfumu inabwerera ku nyumba yake ndipo inakhala usiku wonse osadya kanthu, osalola chosangalatsa chilichonse. Ndipo sinagone tulo.

19Mʼbandakucha, mfumu inanyamuka ndi kufulumira kupita ku dzenje la mikango lija. 20Itayandikira pa dzenjelo, inayitana Danieli moonetsa nkhawa, “Danieli, mtumiki wa Mulungu wa moyo! Kodi Mulungu wako, amene umutumikira nthawi zonse, wakulanditsa ku mikango?”

21Danieli anayankha kuti, “Inu mfumu mukhale ndi moyo wautali! 22Mulungu wanga anatumiza mngelo wake, ndipo anatseka pakamwa pa mikango. Iyo sinandivulaze chifukwa Mulungu anaona kuti ndine wosalakwa ndi kutinso sindinakulakwireni inu mfumu.”

23Mfumu inali ndi chimwemwe chopambana ndipo inalamulira kuti amutulutse Danieli mʼdzenjemo. Ndipo atamutulutsa Danieli mʼdzenjemo, sanapezeke ndi chilonda chilichonse pa thupi lake, chifukwa iye anadalira Mulungu wake.

24Mwa lamulo la mfumu, anthu onse amene ananeneza Danieli aja anagwidwa ndi kukaponyedwa mʼdzenje la mikango, pamodzi ndi akazi awo ndi ana awo. Ndipo asanafike pansi pa dzenjelo, mikango inawawakha ndi mphamvu ndi kuteketa mafupa awo onse.

25Kenaka mfumu Dariyo inalembera anthu a mitundu yonse, ndi anthu a ziyankhulo zosiyanasiyana a mʼdziko lonse kuti,

“Mtendere uchuluke pakati panu!

26“Ndikukhazikitsa lamulo kuti paliponse mʼdziko langa anthu ayenera kuopa ndi kuchitira ulemu Mulungu wa Danieli.

“Popeza Iye ndi Mulungu wamoyo

ndi wamuyaya;

ufumu wake sudzawonongeka,

ulamuliro wake sudzatha.

27Iye amalanditsa ndipo amapulumutsa,

amachita zizindikiro ndi zozizwitsa

kumwamba ndi pa dziko lapansi.

Iye walanditsa Danieli

ku mphamvu ya mikango.”

28Choncho Danieli anapeza ufulu pa nthawi ya ulamuliro wa Dariyo ndi ulamuliro wa Koresi wa ku Perisiya.

New International Version

Daniel 6:1-28

Daniel in the Den of Lions

In Aramaic texts 6:1-28 is numbered 6:2-29. 1It pleased Darius to appoint 120 satraps to rule throughout the kingdom, 2with three administrators over them, one of whom was Daniel. The satraps were made accountable to them so that the king might not suffer loss. 3Now Daniel so distinguished himself among the administrators and the satraps by his exceptional qualities that the king planned to set him over the whole kingdom. 4At this, the administrators and the satraps tried to find grounds for charges against Daniel in his conduct of government affairs, but they were unable to do so. They could find no corruption in him, because he was trustworthy and neither corrupt nor negligent. 5Finally these men said, “We will never find any basis for charges against this man Daniel unless it has something to do with the law of his God.”

6So these administrators and satraps went as a group to the king and said: “May King Darius live forever! 7The royal administrators, prefects, satraps, advisers and governors have all agreed that the king should issue an edict and enforce the decree that anyone who prays to any god or human being during the next thirty days, except to you, Your Majesty, shall be thrown into the lions’ den. 8Now, Your Majesty, issue the decree and put it in writing so that it cannot be altered—in accordance with the law of the Medes and Persians, which cannot be repealed.” 9So King Darius put the decree in writing.

10Now when Daniel learned that the decree had been published, he went home to his upstairs room where the windows opened toward Jerusalem. Three times a day he got down on his knees and prayed, giving thanks to his God, just as he had done before. 11Then these men went as a group and found Daniel praying and asking God for help. 12So they went to the king and spoke to him about his royal decree: “Did you not publish a decree that during the next thirty days anyone who prays to any god or human being except to you, Your Majesty, would be thrown into the lions’ den?”

The king answered, “The decree stands—in accordance with the law of the Medes and Persians, which cannot be repealed.”

13Then they said to the king, “Daniel, who is one of the exiles from Judah, pays no attention to you, Your Majesty, or to the decree you put in writing. He still prays three times a day.” 14When the king heard this, he was greatly distressed; he was determined to rescue Daniel and made every effort until sundown to save him.

15Then the men went as a group to King Darius and said to him, “Remember, Your Majesty, that according to the law of the Medes and Persians no decree or edict that the king issues can be changed.”

16So the king gave the order, and they brought Daniel and threw him into the lions’ den. The king said to Daniel, “May your God, whom you serve continually, rescue you!”

17A stone was brought and placed over the mouth of the den, and the king sealed it with his own signet ring and with the rings of his nobles, so that Daniel’s situation might not be changed. 18Then the king returned to his palace and spent the night without eating and without any entertainment being brought to him. And he could not sleep.

19At the first light of dawn, the king got up and hurried to the lions’ den. 20When he came near the den, he called to Daniel in an anguished voice, “Daniel, servant of the living God, has your God, whom you serve continually, been able to rescue you from the lions?”

21Daniel answered, “May the king live forever! 22My God sent his angel, and he shut the mouths of the lions. They have not hurt me, because I was found innocent in his sight. Nor have I ever done any wrong before you, Your Majesty.”

23The king was overjoyed and gave orders to lift Daniel out of the den. And when Daniel was lifted from the den, no wound was found on him, because he had trusted in his God.

24At the king’s command, the men who had falsely accused Daniel were brought in and thrown into the lions’ den, along with their wives and children. And before they reached the floor of the den, the lions overpowered them and crushed all their bones.

25Then King Darius wrote to all the nations and peoples of every language in all the earth:

“May you prosper greatly!

26“I issue a decree that in every part of my kingdom people must fear and reverence the God of Daniel.

“For he is the living God

and he endures forever;

his kingdom will not be destroyed,

his dominion will never end.

27He rescues and he saves;

he performs signs and wonders

in the heavens and on the earth.

He has rescued Daniel

from the power of the lions.”

28So Daniel prospered during the reign of Darius and the reign of Cyrus6:28 Or Darius, that is, the reign of Cyrus the Persian.