Danieli 5 – CCL & PCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Danieli 5:1-31

Malemba pa Khoma

1Tsiku lina mfumu Belisazara anakonza phwando lalikulu la akalonga ake 1,000 ndipo anamwa vinyo pamodzi ndi iwo. 2Pamene Belisazara ankamwa vinyo, analamula kuti ziwiya zagolide ndi zasiliva zimene Nebukadinezara abambo ake anakatenga mʼNyumba ya Mulungu ku Yerusalemu zikatengedwe kuti mfumu ndi akalonga ake, akazi ake ndi azikazi amweremo. 3Choncho anabweretsa ziwiya zagolide zimene anazitenga mʼNyumba ya Mulungu; ndipo mfumu ndi akalonga ake, akazi ake ndi azikazi ake anamweramo. 4Akumwa vinyo, anatamanda milungu yagolide ndi siliva, yamkuwa, chitsulo, yamtengo ndi mwala.

5Mwadzidzidzi zala za dzanja la munthu zinaonekera ndi kulemba pa khoma, pafupi ndi choyikapo nyale mʼnyumba yaufumu. Mfumu inapenyetsetsa dzanjalo pamene limalemba. 6Nkhope yake inasandulika ndipo inachita mantha, nkhongono zii, mawondo gwedegwede.

7Mfumu inafuwula kuyitana owombeza, alawuli ndi amawula kuti abwere. Ndipo anawawuza anthu anzeru a ku Babuloni kuti, “Aliyense amene awerenge malembawa ndi kundiwuza tanthauzo lake adzavekedwa chovala cha pepo ndi mkanda wa golide udzavekedwa mʼkhosi mwake, ndipo adzakhala wolamulira wachitatu mu ufumuwu.”

8Pamenepo anzeru onse a mfumu anabwera, koma sanakwanitse kuwerenga malembawo kapena kumutanthauzira mfumu. 9Choncho mfumu Belisazara anachita mantha koposa ndipo nkhope yake inapitirira kusinthika. Akalonga ake anathedwa nzeru.

10Mfumukazi, pakumva mawu a mfumu ndi akalonga ake, analowa mʼchipinda cha phwando ndipo anati, “Mfumu mukhale ndi moyo wautali! Musavutike! Nkhope yanu isasinthike! 11Pali munthu wina mu ufumu wanu uno amene mwa iye muli mzimu wa milungu yoyera. Pa nthawi ya ulamuliro wa abambo anu iye anapezeka kuti ali ndi chidziwitso, luntha ndi nzeru zonga za milungu. Mfumu Nebukadinezara, abambo anu, Ine ndikukuwuzani anamusankha iye kukhala mkulu wa amatsenga, owombeza, alawuli ndi amawula. 12Munthu ameneyu dzina lake ndi Danieli, koma mfumu inamutcha Belitesezara ndipo ali ndi nzeru zapadera, ndi wodziwa ndi kuzindikira zinthu, ndiponso luso lakutanthauzira maloto, kufotokozera miyambi ndi kuthetsa mavuto osautsa. Muyitaneni Danieli, ndipo adzakuwuzani chomwe mawuwa akutanthauza.”

13Choncho anabwera naye Danieli pamaso pa mfumu ndipo inati kwa iye, “Kodi ndiwe Danieli, mmodzi mwa akapolo omwe abambo anga mfumu anabwera nawo kuchoka ku Yuda? 14Ndamva kuti mzimu wa milungu uli mwa iwe ndi kuti uli ndi chidziwitso, luntha ndi nzeru zapadera. 15Anzeru ndi owombeza anabwera pamaso panga kuti awerenge zolembedwazi ndi kundiwuza tanthauzo lake koma sanakwanitse kundifotokozera. 16Tsopano ndamva kuti iwe ukhoza kupereka matanthauzo ndi kuthetsa mavuto. Ngati ungawerenge zolembedwazi ndi kundiwuza tanthauzo lake, udzavekedwa chovala cha pepo ndi kuyikidwa mkanda wa golide mʼkhosi mwako, ndipo udzakhala wolamulira wachitatu mu ufumu uno.”

17Pamenepo Danieli anayankha mfumu kuti, “Inu musunge mphatso zanuzo kwa inu nokha ndipo mupereke mphothoyo kwa wina aliyense. Komabe ine ndi kuwerengerani malembawa mfumu; ndikukuwuzani tanthauzo lake.

18“Inu mfumu, Mulungu Wammwambamwamba anapatsa abambo anu Nebukadinezara mphamvu ndi ukulu ndi ulemerero ndi ufumu. 19Chifukwa cha udindo waukulu umene anapatsidwanso, anthu onse ndi mitundu ndi anthu aziyankhulo zosiyanasiyana ankanjenjemera ndikumuopa iye. Amene mfumu inafuna anawaphadi; amene inafuna kuwasunga, inawasunga; amene inafuna kuwakweza, inawakweza; ndipo amene inafuna kuwatsitsa, inawatsitsa. 20Koma pamene inayamba kudzitama ndi kuwumitsa mtima wake ndi kuyamba kunyada, inachotsedwa pa mpando wake waufumu ndi kulandidwa ulemerero wake. 21Iyo inachotsedwa pakati pa anthu ndi kupatsidwa mtima ngati wa nyama; inakhala pamodzi ndi abulu akutchire ndi kudya udzu ngati ngʼombe; ndipo thupi lake linanyowa ndi mame akumwamba, mpaka pamene anavomereza kuti Mulungu Wammwambamwamba ndiye wolamulira maufumu a anthu ndipo amawupereka kwa aliyense amene Iye wafuna.

22“Koma inu mwana wake, Belisazara, simunadzichepetse, ngakhale kuti mumadziwa zonsezi. 23Mʼmalo mwake, mwadzikweza nokha kutsutsana ndi Ambuye wakumwamba. Inu mwatenga ziwiya za mʼNyumba mwake, ndipo inu ndi akalonga anu, akazi anu ndi azikazi anu mwamwera vinyo mu zimenezi. Inu munatamanda milungu yasiliva ndi golide, yamkuwa, chitsulo, mtengo ndi mwala, imene singaone kapena kumva kapena kuzindikira. Koma simunamupatse ulemu Mulungu amene asunga mʼmanja mwake moyo wanu ndi njira zanu zonse. 24Choncho Iye watumiza dzanja limene lalemba mawu amenewa.

25“Mawu amene analembedwa ndi awa:

MENE, MENE, TEKELI, PARASINI.

26“Zimene mawuwa akutanthauza ndi izi:

Mene: Mulungu wawerenga masiku a ufumu wanu ndipo wauthetsa.

27Tekeli: Inu mwayesedwa pa sikelo ndipo mwapezeka kuti mukuperewera.

28Parasini: Ufumu wanu wagawidwa ndi kupatsidwa kwa Amedi ndi Aperezi.”

29Mwa lamulo la Belisazara, Danieli anavekedwa chovala cha pepo, mkanda wagolide unayikidwa mʼkhosi mwake, ndipo analengeza kuti anali wachitatu mu ulamuliro mu ufumuwo.

30Usiku womwewo Belisazara, mfumu ya anthu a ku Babuloni, inaphedwa, 31ndipo Dariyo Mmedi analanda ufumuwo ali ndi zaka 62.

Persian Contemporary Bible

دانيال 5:1-31

ضيافت بلشصر

1يک شب بلشصر پادشاه ضيافت بزرگی ترتيب داد و هزار نفر از بزرگان مملكت را به باده‌نوشی دعوت كرد. 2‏-4وقتی بلشصر سرگرم شرابخواری بود، دستور داد كه جامهای طلا و نقره را كه جدش نبوكدنصر از خانهٔ خدا در اورشليم به بابل آورده بود، بياورند. وقتی آنها را آوردند، پادشاه و بزرگان و زنان و كنيزان پادشاه در آنها شراب نوشيدند و بتهای خود را كه از طلا و نقره، مفرغ و آهن، چوب و سنگ ساخته شده بود، پرستش كردند.

5اما در حالی كه غرق عيش و نوش بودند، ناگهان انگشتهای دست انسانی بيرون آمده شروع كرد به نوشتن روی ديواری كه در مقابل چراغدان بود. پادشاه با چشمان خود ديد كه آن انگشتها می‌نوشتند 6و از ترس رنگش پريد و چنان وحشتزده شد كه زانوهايش به هم می‌خورد و نمی‌توانست روی پاهايش بايستد. 7سپس، فرياد زد: «جادوگران، طالع‌بينان و منجمان را بياوريد! هر كه بتواند نوشتهٔ روی ديوار را بخواند و معنی‌اش را به من بگويد، لباس ارغوانی سلطنتی را به او می‌پوشانم، طوق طلا را به گردنش می‌اندازم و او شخص سوم مملكت خواهد شد.» 8اما وقتی حكيمان آمدند، هيچكدام نتوانستند نوشتهٔ روی ديوار را بخوانند و معنی‌اش را بگويند.

9ترس و وحشت پادشاه بيشتر شد! بزرگان نيز به وحشت افتاده بودند. 10اما وقتی ملكهٔ مادر از جريان باخبر شد، با شتاب خود را به تالار ضيافت رساند و به بلشصر گفت: «پادشاه تا به ابد زنده بماند! ترسان و مضطرب نباش. 11در مملكت تو مردی وجود دارد كه روح خدايان مقدس در اوست. در زمان جدت، نبوكدنصر، او نشان داد كه از بصيرت و دانايی و حكمت خدايی برخوردار است و جدت او را به رياست منجمان و جادوگران و طالع‌بينان و رمالان منصوب كرد. 12اين شخص دانيال است كه پادشاه او را بلطشصر ناميده بود. او را احضار كن، زيرا او مرد حكيم و دانايی است و می‌تواند خوابها را تعبير كند، اسرار را كشف نمايد و مسايل دشوار را حل كند. او معنی نوشتهٔ روی ديوار را به تو خواهد گفت.»

13پس دانيال را به حضور پادشاه آوردند. پادشاه از او پرسيد: «آيا تو همان دانيال از اسرای يهودی هستی كه نبوكدنصر پادشاه از سرزمين يهودا به اينجا آورد؟ 14شنيده‌ام روح خدايان در توست و شخصی هستی پر از حكمت و بصيرت و دانايی. 15حكيمان و منجمان من سعی كردند آن نوشتهٔ روی ديوار را بخوانند و معنی‌اش را به من بگويند، ولی نتوانستند. 16دربارهٔ تو شنيده‌ام كه می‌توانی اسرار را كشف نمايی و مسايل مشكل را حل كنی. اگر بتوانی اين نوشته را بخوانی و معنی آن را به من بگويی، به تو لباس ارغوانی سلطنتی را می‌پوشانم، طوق طلا را به گردنت می‌اندازم و تو را شخص سوم مملكت می‌گردانم.»

17دانيال جواب داد: «اين انعام‌ها را برای خود نگاه دار يا به شخص ديگری بده؛ ولی من آن نوشته را خواهم خواند و معنی‌اش را به تو خواهم گفت. 18ای پادشاه، خدای متعال به جدت نبوكدنصر، سلطنت و عظمت و افتخار بخشيد. 19چنان عظمتی به او داد كه مردم از هر قوم و نژاد و زبان از او می‌ترسيدند. هر كه را می‌خواست می‌كشت و هر كه را می‌خواست زنده نگاه می‌داشت؛ هر كه را می‌خواست سرافراز می‌گرداند و هر كه را می‌خواست پست می‌ساخت. 20اما او مستبد و متكبر و مغرور شد، پس خدا او را از سلطنت بركنار كرد و شكوه و جلالش را از او گرفت. 21از ميان انسانها رانده شد و عقل انسانی او به عقل حيوانی تبديل گشت. با گورخران به سر می‌برد و مثل گاو علف می‌خورد و بدنش از شبنم آسمان تر می‌شد تا سرانجام فهميد كه دنيا در تسلط خدای متعال است و او حكومت بر ممالک دنيا را به هر كه اراده كند، می‌بخشد.

22«اما تو ای بلشصر كه بر تخت نبوكدنصر نشسته‌ای، با اينكه اين چيزها را می‌دانستی، ولی فروتن نشدی. 23تو به خداوند آسمانها بی‌حرمتی كردی و جامهای خانهٔ او را به اينجا آورده، با بزرگان و زنان و كنيزانت در آنها شراب نوشيدی و بتهای خود را كه از طلا و نقره، مفرغ و آهن، چوب و سنگ ساخته شده‌اند كه نه می‌بينند و نه می‌شنوند و نه چيزی می‌فهمند، پرستش كردی؛ ولی آن خدا را كه زندگی و سرنوشتت در دست اوست تمجيد ننمودی. 24‏-25پس خدا آن دست را فرستاد تا اين پيام را بنويسد: منا، منا، ثقيل، فرسين. 26معنی اين نوشته چنين است: منا يعنی ”شمرده شده“. خدا روزهای سلطنت تو را شمرده است و دورهٔ آن به سر رسيده است. 27ثقيل يعنی ”وزن شده“. خدا تو را در ترازوی خود وزن كرده و تو را ناقص يافته است. 28فرسين يعنی ”تقسيم شده“. مملكت تو تقسيم می‌شود و به مادها و پارس‌ها داده خواهد شد.»

29پس به فرمان بلشصر، لباس ارغوانی سلطنتی را به دانيال پوشانيدند، طوق طلا را به گردنش انداختند و اعلان كردند كه شخص سوم مملكت است.

30همان شب بلشصر، پادشاه بابل كشته شد 31و داريوش مادی كه در آن وقت شصت و دو ساله بود بر تخت سلطنت نشست.