Danieli 3 – CCL & NIV

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Danieli 3:1-30

Fano la Golide ndi Ngʼanjo ya Moto

1Mfumu Nebukadinezara anapangitsa fano la golide lotalika mamita 27 ndi mulifupi mwake mamita atatu, ndipo analiyimika mʼchigwa cha Dura mʼchigawo cha Babuloni. 2Kenaka iye anayitanitsa akalonga, abwanamkubwa, nduna, aphungu, asungichuma, oweruza milandu, anyakwawa ndi akulu ena onse a madera a dzikolo, kuti abwere ku mwambo wotsekula fano limene analiyimika lija. 3Choncho akalonga, abwanamkubwa, nduna, aphungu, asungichuma, oweruza milandu, anyakwawa, ndi akulu ena onse a madera a dzikolo, anasonkhana kudzachita mwambo wotsekulira fano limene mfumu Nebukadinezara analiyimika, ndipo mlaliki anayimirira pamaso pa fanolo nati:

4“Inu anthu a mitundu yonse ndi a ziyankhulo zonse, mukulamulidwa kuti muchite izi: mitundu ya anthu ndi a chiyankhulo chilichonse 5mukadzamva kulira kwa lipenga, chitoliro, zeze, sansi, chisakasa, mngoli ndi nyimbo za mtundu uliwonse, muyenera kulambira ndi kupembedza fano la golide limene mfumu Nebukadinezara analiyimika. 6Aliyense amene sadzalambira ndi kupembedza adzaponyedwa nthawi yomweyo mʼngʼanjo ya moto.”

7Choncho anthu onse aja atangomva kulira kwa lipenga, chitoliro, zeze, sansi, chisakasa, mngoli ndi nyimbo za mtundu uliwonse, analambira ndi kupembedza fano la golide limene mfumu Nebukadinezara analiyimika.

8Pa nthawi imeneyi alawuli ena anafika ndi kuwanenera zoyipa Ayuda. 9Iwo anati kwa mfumu Nebukadinezara, “Inu mfumu mukhale ndi moyo wautali! 10Inu mfumu, mwakhazikitsa lamulo kuti aliyense akamva kulira kwa lipenga, chitoliro, zeze, sansi, chisakasa, mngoli ndi nyimbo za mtundu uliwonse, ayenera kulambira ndi kupembedza fano la golide, 11ndi kuti aliyense osalambira ndi kupembedza adzaponyedwa mʼngʼanjo ya moto. 12Koma alipo Ayuda ena Sadirake, Mesaki ndi Abedinego amene munawayika kuti ayangʼanire ntchito ya dera la ku Babuloni. Anthu amenewa sakumvera inu mfumu. Iwo sakutumikira milungu yanu kapena kulambira fano la golide limene munaliyimikalo.”

13Tsono Nebukadinezara anakwiya ndi kupsa mtima kwambiri, ndipo anayitanitsa Sadirake, Mesaki ndi Abedenego. Choncho amuna awa anabwera pamaso pa mfumu, 14ndipo Nebukadinezara anawafunsa kuti, “Kodi ndi zoona, Sadirake, Mesaki ndi Abedenego, kuti simukutumikira milungu yanga kapena kupembedza fano la golide ndinaliyikalo? 15Tsopano ngati muli okonzeka kulambira ndi kupembedza fano ndinalipanga, mukangomva kulira kwa lipenga chitoliro, zeze, sansi, chisakasa, mngoli ndi nyimbo za mtundu uliwonse, muchita bwino. Koma ngati simulipembedza, mudzaponyedwa mʼnganjo ya moto. Nanga ndi mulungu uti amene adzatha kukupulumutsani mʼmanja anga?”

16Sadirake, Mesaki ndi Abedenego anayankha mfumu Nebukadinezara kuti, “Sikoyenera kuti tikuyankheni pa nkhani imeneyi. 17Ngati tiponyedwa mʼngʼanjo ya moto, Mulungu amene timamutumikira akhoza kutipulumutsa ku ngʼanjo yamotoyo, ndipo adzatilanditsa mʼdzanja lanu mfumu. 18Koma ngakhale Mulungu wathu atapanda kutipulumutsa, tikufuna mudziwe inu mfumu, kuti sitidzatumikira milungu yanu kapena kupembedza fano la golide limene munaliyimika.”

19Pamenepo Nebukadinezara anapsa mtima ndi Sadirake, Mesaki ndi Abedenego, ndipo anayipidwa nawo. Iye analamulira kuti ngʼanjo ayitenthetse kasanu ndi kawiri kuposa nthawi zonse, 20ndipo analamula ena mwa asilikali amphamvu kwambiri mʼgulu lake lankhondo kuti amange Sadirake, Mesaki ndi Abedenego ndi kuwaponya mʼngʼanjo ya moto. 21Choncho amuna awa, atavala mikanjo yawo, mabuluku, nduwira ndi zovala zina zonse, anamangidwa ndi kuponyedwa mʼngʼanjo ya moto. 22Tsono popeza lamulo la mfumu linali lofulumiza, ngʼanjo inatenthetsedwa kowirikiza mwakuti malawi ake anapha asilikali amene ananyamula Sadirake, Mesaki ndi Abedenego, 23ndipo anyamata atatuwa, ali chimangidwire, anagwera mʼngʼanjo ya moto.

24Kenaka mfumu Nebukadinezara anadabwa ndipo anafunsa nduna zake kuti, “Kodi sanali amuna atatu amene anamangidwa ndi kuponyedwa mʼmoto?”

Iwo anayankha kuti, “Ndi zoonadi, mfumu.”

25Iye anati, “Taonani! Ndikuona amuna anayi akuyendayenda mʼmoto, osamangidwa ndi osapwetekedwa ndipo wachinayi akuoneka ngati mwana wa milungu.”

26Pamenepo Nebukadinezara anayandikira pa khomo langʼanjo ya moto ndi kufuwula kuti, “Sadirake, Mesaki ndi Abedenego, atumiki a Mulungu Wammwambamwamba, tulukani! Bwerani kuno!”

Ndipo Sadirake, Mesaki ndi Abedenego anatuluka mʼmoto, 27ndipo akalonga, akazembe, abwanamkubwa ndi nduna zamfumu anasonkhana mowazungulira. Anaona kuti moto sunatenthe matupi awo ngakhale tsitsi kumutu kwawo silinapse; zovala zawo sizinapse, ndipo sankamveka fungo la moto.

28Kenaka Nebukadinezara anati, “Atamandike Mulungu wa Sadirake, Mesaki ndi Abedenego, amene anatumiza mngelo wake ndi kupulumutsa atumiki ake! Iwo anakhulupirira Iye ndi kunyozera lamulo la mfumu ndipo anali okonzeka kutaya moyo wawo koposa kutumikira kapena kupembedza mulungu wina aliyense wosakhala Mulungu wawo. 29Tsono ndikulamula kuti anthu a mitundu ina kaya chiyankhulo china chili chonse amene anganyoze Mulungu wa Sadirake, Mesaki ndi Abedenego adulidwe nthulinthuli ndipo nyumba zawo ndidzagwetsa ndi kusandutsa bwinja, popeza palibe Mulungu amene akhoza kupulumutsa mʼnjira yotere.”

30Ndipo mfumu Nebukadinezara anakweza pa ntchito Sadirake, Mesaki ndi Abedenego mʼchigawo cha Babuloni.

New International Version

Daniel 3:1-30

The Image of Gold and the Blazing Furnace

1King Nebuchadnezzar made an image of gold, sixty cubits high and six cubits wide,3:1 That is, about 90 feet high and 9 feet wide or about 27 meters high and 2.7 meters wide and set it up on the plain of Dura in the province of Babylon. 2He then summoned the satraps, prefects, governors, advisers, treasurers, judges, magistrates and all the other provincial officials to come to the dedication of the image he had set up. 3So the satraps, prefects, governors, advisers, treasurers, judges, magistrates and all the other provincial officials assembled for the dedication of the image that King Nebuchadnezzar had set up, and they stood before it.

4Then the herald loudly proclaimed, “Nations and peoples of every language, this is what you are commanded to do: 5As soon as you hear the sound of the horn, flute, zither, lyre, harp, pipe and all kinds of music, you must fall down and worship the image of gold that King Nebuchadnezzar has set up. 6Whoever does not fall down and worship will immediately be thrown into a blazing furnace.”

7Therefore, as soon as they heard the sound of the horn, flute, zither, lyre, harp and all kinds of music, all the nations and peoples of every language fell down and worshiped the image of gold that King Nebuchadnezzar had set up.

8At this time some astrologers3:8 Or Chaldeans came forward and denounced the Jews. 9They said to King Nebuchadnezzar, “May the king live forever! 10Your Majesty has issued a decree that everyone who hears the sound of the horn, flute, zither, lyre, harp, pipe and all kinds of music must fall down and worship the image of gold, 11and that whoever does not fall down and worship will be thrown into a blazing furnace. 12But there are some Jews whom you have set over the affairs of the province of Babylon—Shadrach, Meshach and Abednego—who pay no attention to you, Your Majesty. They neither serve your gods nor worship the image of gold you have set up.”

13Furious with rage, Nebuchadnezzar summoned Shadrach, Meshach and Abednego. So these men were brought before the king, 14and Nebuchadnezzar said to them, “Is it true, Shadrach, Meshach and Abednego, that you do not serve my gods or worship the image of gold I have set up? 15Now when you hear the sound of the horn, flute, zither, lyre, harp, pipe and all kinds of music, if you are ready to fall down and worship the image I made, very good. But if you do not worship it, you will be thrown immediately into a blazing furnace. Then what god will be able to rescue you from my hand?”

16Shadrach, Meshach and Abednego replied to him, “King Nebuchadnezzar, we do not need to defend ourselves before you in this matter. 17If we are thrown into the blazing furnace, the God we serve is able to deliver us from it, and he will deliver us3:17 Or If the God we serve is able to deliver us, then he will deliver us from the blazing furnace and from Your Majesty’s hand. 18But even if he does not, we want you to know, Your Majesty, that we will not serve your gods or worship the image of gold you have set up.”

19Then Nebuchadnezzar was furious with Shadrach, Meshach and Abednego, and his attitude toward them changed. He ordered the furnace heated seven times hotter than usual 20and commanded some of the strongest soldiers in his army to tie up Shadrach, Meshach and Abednego and throw them into the blazing furnace. 21So these men, wearing their robes, trousers, turbans and other clothes, were bound and thrown into the blazing furnace. 22The king’s command was so urgent and the furnace so hot that the flames of the fire killed the soldiers who took up Shadrach, Meshach and Abednego, 23and these three men, firmly tied, fell into the blazing furnace.

24Then King Nebuchadnezzar leaped to his feet in amazement and asked his advisers, “Weren’t there three men that we tied up and threw into the fire?”

They replied, “Certainly, Your Majesty.”

25He said, “Look! I see four men walking around in the fire, unbound and unharmed, and the fourth looks like a son of the gods.”

26Nebuchadnezzar then approached the opening of the blazing furnace and shouted, “Shadrach, Meshach and Abednego, servants of the Most High God, come out! Come here!”

So Shadrach, Meshach and Abednego came out of the fire, 27and the satraps, prefects, governors and royal advisers crowded around them. They saw that the fire had not harmed their bodies, nor was a hair of their heads singed; their robes were not scorched, and there was no smell of fire on them.

28Then Nebuchadnezzar said, “Praise be to the God of Shadrach, Meshach and Abednego, who has sent his angel and rescued his servants! They trusted in him and defied the king’s command and were willing to give up their lives rather than serve or worship any god except their own God. 29Therefore I decree that the people of any nation or language who say anything against the God of Shadrach, Meshach and Abednego be cut into pieces and their houses be turned into piles of rubble, for no other god can save in this way.”

30Then the king promoted Shadrach, Meshach and Abednego in the province of Babylon.