Danieli 12 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Danieli 12:1-13

Nthawi Yotsiriza

1“Pa nthawi imeneyo Mikayeli, mngelo wamkulu amene amateteza anthu a mtundu wako, adzabwera. Imeneyi idzakhala nthawi ya mavuto aakulu omwe sanaonekepo kuyambira pachiyambi cha mitundu ya anthu mpaka nthawi ikudzayo. Komatu pa nthawiyi anthu a mtundu wako, aliyense amene dzina lake lidzapezeke lolembedwa mʼbuku adzapulumutsidwa. 2Ambiri mwa amene akugona mʼnthaka adzadzuka: ena adzapita ku moyo wosatha, ena ku malo amanyazi ndi chilango chosatha. 3Amene ali anzeru mʼnjira ya chilungamo adzawala ngati kuwala kwa mlengalenga, ndipo amene alondolera ambiri ku njira yolungama, adzawala ngati nyenyezi ku nthawi zosatha. 4Koma iweyo, Danieli, sungitsa mawuwa, umate bukuli kufikira nthawi ya chimaliziro. Anthu ambiri adzapita uku ndi uko ndipo nzeru zidzanka zikukulirakulira.”

5Kenaka ine Danieli poyangʼana ndinaona anthu ena awiri atayima, wina tsidya lino la mtsinje, wina tsidya linalo. 6Mmodzi mwa awiriwo anafunsa munthu wovala chovala chosalala amene anali mʼmbali mwa madzi a mu mtsinje uja kuti, “Kodi padzapita nthawi yayitali bwanji kuti zodabwitsazi zidzakwaniritsidwe?”

7Munthu wovala chovala chosalala, amene anali mʼmbali mwa madzi a mu mtsinje uja, anakweza dzanja lake lamanja ndi lamanzere kumwamba, ndipo ndinamumva akulumbira mʼdzina la Wamoyo ku nthawi zonse uja kuti, “Zidzachitika patapita zaka zitatu ndi theka. Zinthu zonsezi zidzachitika akadzatha masautso amene agwera anthu olungama.”

8Ndinamva, koma sindinamvetsetse. Choncho ndinafunsa kuti, “Mbuye wanga, nanga matsiriziro a zonsezi adzakhala chiyani?”

9Ndipo anandiyankha kuti, “Pita iwe Danieli, pakuti mawuwa ndi osungidwa ndi omatidwa kufikira nthawi ya chimaliziro. 10Anthu ambiri adzayeretsedwa nakhala olungama wopanda chodetsa, koma oyipa adzakhala chiyipire. Palibe mmodzi wa anthu oyipa amene adzamvetsetsa koma okhawo amene ali anzeru adzamvetsetsa.

11“Kuyambira pamene nsembe ya tsiku ndi tsiku idzathetsedwa ndi kukhazikitsa kwa chonyansa chobweretsa chisokonezo chija, padzapita masiku 1,290. 12Wodala munthu amene adikirabe nadzafika pa mapeto a masiku 1,335.

13“Koma iweyo Danieli, pitiriza ndipo ulimbikire mpaka matsiriziro. Kenaka udzamwalira. Koma mʼmasiku otsiriza udzauka kuti ulandire gawo lako.”