Danieli 11 – CCL & CCBT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Danieli 11:1-45

1Ndipo chaka choyamba cha Dariyo Mmedi ine Mikayeli ndinabwera kumuthandiza ndi kumuteteza Gabrieli.

Mafumu a Kummwera ndi Kumpoto

2“Ndipo tsopano ndikuwuza zoona: Mafumu ena atatu adzalamulira ku Peresiya, ndipo kenaka padzadzuka mfumu yachinayi imene idzakhala yolemera kwambiri kuposa onsewo. Popeza kuti idzakhala ndi mphamvu chifukwa cha chuma chake, idzadzutsa onse kuti alimbane ndi ufumu wa Grisi. 3Kenaka mfumu yamphamvu idzafika imene idzalamulira ndi ufumu waukulu ndi kuchita zimene ifuna. 4Koma ufumu wake ukadzafika pachimake, udzawonongedwa ndi kugawidwa mʼzigawo zinayi. Ufumuwo sudzaperekedwa kwa zidzukulu zake, ndipo olowa mʼmalo mwake sadzakhala ndi mphamvu monga anali nazo, chifukwa ufumu wake udzazulidwa ndi kuperekedwa kwa ena.

5“Mfumu ya kummwera idzakhala yamphamvu, koma mmodzi mwa akalonga ake adzakhala ndi mphamvu kuposa iyo; adzalamulira ufumu wake waukulu kwambiri. 6Patapita zaka zingapo, mfumu ya kummwera ndi mfumu ya kumpoto adzachita pangano. Mwana wamkazi wa mfumu ya kummwera adzapita nakakwatiwa ndi mfumu ya kumpoto pokhazikitsa pangano la mtendere, koma ulamuliro wake pamodzi ndi wa mwana wake sudzakhalitsa. Mʼmasiku amenewo iye, mwamuna wake, mwana wake ndi atumiki ake, onse adzaperekedwa kwa adani.

7“Mmodzi wochokera ku banja la mkaziyo adzadzuka nadzalamulira mʼmalo mwake. Iye adzamenyana ndi ankhondo a mfumu ya kumpoto ndi kulowa mʼmalo ake otetezedwa; adzachita nawo nkhondo ndi kupambana. 8Iye adzalandanso milungu yawo, mafano awo achitsulo, ndi ziwiya zawo zamtengowapatali zasiliva ndi golide ndi kubwerera nazo ku Igupto. Adzaleka osayithira nkhondo mfumu ya kumpoto kwa zaka zingapo. 9Kenaka mfumu ya kumpoto idzathira nkhondo dziko la mfumu ya kummwera koma idzalephera ndi kubwerera kwawo. 10Ana ake adzakonzekera nkhondo ndi kusonkhanitsa gulu lankhondo lalikulu, limene lidzathira nkhondo mfumu yakummwera ngati chigumula mpaka kumalo ake otetezedwa.

11“Kenaka mfumu yakummwera idzatuluka mokwiya ndi kumenya nkhondo ndi mfumu yakumpoto, imene idzasonkhanitsa gulu lalikulu la nkhondo, koma idzayigonjetsa. 12Gulu la nkhondoli likadzagwidwa, mfumu yakummwera idzayamba kudzikuza ndipo idzapha anthu miyandamiyanda, koma kupambanaku sikudzapitirira. 13Popeza mfumu ya kumpoto idzasonkhanitsa gulu lina lankhondo, lochulukirapo kuposa loyamba; ndipo patapita zaka zingapo idzabwera ndi chigulu chachikulu cha nkhondo chokonzekeratu ndi zida.

14“Nthawi imeneyo ambiri adzawukira mfumu ya kummwera. Anthu achisokonezo pakati panu nawonso adzawukira pokwaniritsa masomphenya, koma sadzapambana. 15Kenaka mfumu ya kumpoto idzafika ndikuzinga mzinda powunda nthumbira za nkhondo ndipo idzagonjetsa mzinda wotetezedwa. Gulu lankhondo la kummwera lidzasowa mphamvu; ngakhale akatswiri awo ankhondo sadzakhala ndi mphamvu zogonjetsera ankhondo a kumpoto. 16Mfumu ya kumpoto idzachita zofuna zake; palibe aliyense adzayigonjetse. Idzakhazikitsa ulamuliro wake mu Dziko Lokongola. Zonse zidzakhala mu ulamuliro wa mfumu yakumpoto ija. 17Idzafika ndi mphamvu za ufumu wake wonse ndipo idzayesa kuchita pangano la mtendere ndi mfumu ya kummwera. Ndipo idzamupatsa mwana wake wamkazi kuti amukwatire ndi cholinga cholanda ufumu, koma zolinga zake sizidzatheka kapena kumuthandiza. 18Kenaka idzatembenukira ku mayiko a mʼmbali mwa nyanja ndi kulanda mizinda yambiri, koma mtsogoleri wina wa nkhondo adzathetsa kudzikuza kwakeko ndipo adzabwezera chipongwecho kwa iye. 19Zikadzatha izi, mfumu idzabwerera ku malo otetezedwa a dziko la kwawo koma idzapunthwa ndi kugwa osapezekanso.

20“Mfumu imene idzatenga malo ake idzatumiza wokhometsa msonkho kuti chuma cha ufumu wake chichuluke. Komabe mʼzaka zochepa mfumuyo idzawonongedwa osati mu mkwiyo kapena ku nkhondo.

21“Mʼmalo mwake mudzalowa munthu wonyozeka amene si wa banja laufumu. Iye adzabwera pamene anthu akuganiza kuti ali pa mtendere, ndipo adzalanda ufumuwo mwa chinyengo. 22Kenaka adzagonetsa gulu lalikulu lankhondo kuphatikizapo Mkulu wa Ansembe wapangano. 23Atatha kuchita naye pangano, iye adzachita monyenga, ndipo ngakhale adzakhale ndi anthu ochepa adzakhalabe ndi mphamvu. 24Mwadzidzidzi, iye adzazithira nkhondo zigawo zolemera kwambiri ndipo adzachita zimene makolo ake ngakhale agogo ake sanachitepo. Iye adzagawira zolanda, zofunkha ndi chuma kwa omutsatira. Adzachita chiwembu cholanda mizinda yotetezedwa koma kwa kanthawi kochepa.

25“Mfumu ya kumpoto idzalimba mtima, ndipo idzasonkhanitsa gulu lalikulu la ankhondo kuti lithire nkhondo mfumu yakummwera. Mfumu yakummwera ndi gulu lake lankhondo lalikulu ndi lamphamvu idzathirana nkhondo ndi mfumu yakumpoto koma sidzapambana chifukwa cha ziwembu zimene adzamukonzera. 26Amene amadya chakudya ndi mfumu adzamuukira; gulu lake lankhondo lidzagonjetsedwa, ndipo ambiri adzafera ku nkhondo. 27Mafumu awiriwa mitima yawo idzalinga ku zoyipa. Azidzanamizana ali pa tebulo limodzi, koma zolinga zawo sizidzatheka chifukwa nthawi idzakhala isanakwane. 28Mfumu ya kumpoto idzabwerera ku dziko la kwawo ndi chuma chambiri, koma mtima wake udzafunitsitsa pangano lopatulika. Idzawononga panganolo ndipo kenaka idzabwerera ku dziko lake.

29“Patapita nthawi mfumu ya kumpoto idzabwereranso kummwera koma sidzapambana monga inachitira kale. 30Sitima zapamadzi zochokera ku mayiko a ku madzulo zidzalimbana naye, ndipo adzataya mtima. Kenaka idzabwerera mopsa mtima ndi kudzalimbana ndi chipembedzo cha anthu opatulika. Idzabwerera ndi kuchitira chifundo amene sadzasunga pangano loyera.

31“Ankhondo ake adzayipitsa linga la Nyumba ya Mulungu ndipo adzathetsa nsembe za tsiku ndi tsiku. Kenaka adzakhazikitsa chonyansa chimene chabweretsa chiwonongeko. 32Ndi mawu oshashalika mfumuyo idzakopa amene anaphwanya pangano, koma anthu amene amadziwa Mulungu wawo adzalimbika ndipo adzayikana mfumuyo kwathunthu.

33“Amene ndi anzeru adzalangiza ambiri. Koma patapita kanthawi adzaphedwa ndi lupanga kapena kutenthedwa, kapena kugwidwa kapena kulandidwa katundu. 34Pa nthawi yozunzikayi ena adzawathandiza pangʼono, koma ambiri othandizawo adzakhala achinyengo. 35Ena mwa anzeruwo adzaphedwa ndi cholinga chakuti ayengedwe, otsala mwa iwo ayeretsedwe ndi kukhala wopanda banga kufikira nthawi yomaliza, popeza idzafika ndithu nthawi imene Mulungu wayika.

Mfumu Yodzikweza

36“Mfumu ya kumpoto idzachita zimene ikufuna. Idzadzikweza ndi kudziyesa yopambana mulungu aliyense ndipo idzanenera za mwano Mulungu wa milungu. Iyo idzapambana mpaka nthawi yoti Mulungu ayilange mwa mkwiyo itakwana popeza chimene chatsimikizika chiyenera kuchitika. 37Mfumuyo idzanyoza milungu ya makolo ake ndiponso mulungu wokondedwa ndi akazi, sidzachitiranso ulemu mulungu aliyense, koma idzadzikweza yokha pamwamba pa onse. 38Mʼmalo mwa onsewo, idzachitira ulemu mulungu wachitetezo; mulungu wosadziwika ndi makolo ake. Iyo idzapereka kwa mulunguyo golide ndi siliva, ndi miyala yokongola, ndiponso mphatso za pamwamba kwambiri. 39Anthu opembedza mulungu wachilendo adzakhala ngati linga lake. Idzalemekeza iwowa kwambiri, ndipo idzawayika kuti alamulire anthu ambiri. Idzawagawira dziko ngati malipiro awo.

40“Pa nthawi yomaliza mfumu yakummwera idzachita nkhondo ndi mfumu yakumpoto. Koma mfumu yakumpotoyi idzayikantha ndi magaleta ndi akavalo ndi sitima zapamadzi zambiri ngati mphepo yamkokomo. Idzalowa mʼmayiko ambiri ndikuwakokolola onse ngati madzi osefukira. 41Idzalowanso mʼDziko Lokongola ndipo anthu ambiri adzaphedwa. Koma Edomu, Mowabu ndi olamulira a Amoni adzapulumuka. 42Idzathira nkhondo mayiko ambiri ndipo ngakhale Igupto sadzapulumuka. 43Idzalanda chuma cha golide, siliva, ndi zonse za mtengowapatali za ku Igupto, ndiponso anthu a ku Libiya ndi Akusi adzagonja kwa iwo. 44Koma uthenga wochokera kummawa ndi kumpoto udzayiopsa, ndipo idzapita ndi ukali kukawononga ndi kutheratu anthu ambiri. 45Mfumuyo idzayimika matenti ake aufumu, pakati pa nyanja ndi phiri lokongola. Komabe mapeto ake mfumuyo idzaphedwa, ndipo palibe amene adzayithandize.”

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

但以理書 11:1-45

1瑪代大流士元年,我去幫助、護衛米迦勒2現在我要把真相告訴你。波斯將再有三位王興起,隨後的第四位王遠比其他王富有。他靠財富強盛後,便會煽動眾民去攻打希臘國。 3那時必有一位英勇的王興起,執掌大權,隨心所欲。 4但他興起後不久,他的國必土崩瓦解,在天下一分為四,既不歸他的後代統治,也不如他掌權時強盛。因為他的國必被連根拔除,歸給外人。

5「南方王必強盛,他的將領中將有一位比他更強盛,這人執掌王權,勢力強大。 6若干年後,南方王將與北方王聯盟。南方王的女兒將到北方王那裡締結盟約。但她必保不住自己的勢力,王權也無法長久。她和她的隨從、父親和輔佐者必遭殺害。

7「她家族中必有一人繼承王位,率軍攻打北方王,侵入他們的堡壘,擊敗他們, 8將他們的神像、鑄造的偶像及金銀寶器擄到埃及。此後數年,他不再去攻擊北方王。 9後來,北方王必侵入南方王的國土,但終必撤回本國。

10「北方王的兒子們必發動戰爭,召集大軍,如洪水席捲而來,直打到南方王的堡壘。 11南方王必大怒,出來迎戰北方王的大軍,並擊敗他們。 12南方王獲勝後必心高氣傲,殺戮成千上萬的人,但他的勝利不能持久。 13因為數年後,北方王必召集更龐大的軍隊,帶著大量裝備捲土重來。

14「那時,許多人必起來反抗南方王。你同胞中的殘暴之徒也必反叛,從而使異象應驗,但他們必失敗。 15北方王必修築高臺攻取南方王的堅城,南方的軍兵必無力抵擋,就是精兵也抵擋不住。 16北方王必為所欲為,所向無敵。他必侵佔佳美之地,手握毀滅之權。 17他決意傾全國之力而來,與南方王建立聯盟,並將自己的女兒嫁給南方王,旨在推翻他的國。但北方王的計劃必然失敗,毫無收益。

18「後來,他將轉而攻打沿海地區,征服許多地方。但一位將領必制止他的囂張氣焰,使他自取其辱。 19他將返回本國的堡壘,從此一蹶不振,銷聲匿跡。 20繼承他王位的人將派稅吏橫徵暴斂,以維持王國的榮耀。但不久他必滅亡,並非死於民怨,也非死於戰爭。

21「接著繼位的是一個卑鄙的人。他無權繼位,卻乘人不備用奸計奪取王位。 22他橫掃千軍,擊潰他們,包括盟國的王。 23他與人結盟後,必行欺詐,藉不多的人掌握大權。 24他必乘人不備入侵最富庶的地區,行他祖先從未行過的事,將擄掠的財物分給部下,並策劃攻打堡壘,但這都是短暫的。 25他集中力量,鼓起勇氣,率領大軍進攻南方王。南方王也率領強大的軍隊迎戰,卻敵不過他,因為有人暗算南方王。 26南方王必遭親信暗算,全軍潰敗,許多人被殺。 27兩個王心懷叵測,同席而坐,爾虞我詐,但都不成功,因為結局必在所定的時間到來。 28北方王必帶著大量財物回國,但他決意反對聖約,在回國的路上任意妄為。

29「到了所定的時間,他必再次攻打南方,但結果與上次不同, 30因為基提的戰船必來攻擊他,使他喪膽而回。他必向聖約之民發洩憤怒,任意妄為,支持背棄聖約的人。 31他的軍隊必褻瀆聖地,褻瀆那堡壘,廢除日常獻的祭,設立帶來毀滅的可憎之物。 32他必花言巧語籠絡違背聖約的人,但認識上帝的人必奮起反抗。 33那些智者必教導許多民眾,但他們將在一段時間內被刀劍殺戮,或被燒死,或被擄去,或被搶掠。 34他們敗亡時必得不到多少援助,許多人並非真心實意地加入他們的行列。 35有些智者將被害,但這是為了熬煉、淨化他們,使他們潔白無瑕,一直到末了。因為結局必在所定的時間到來。

36「北方王必任意妄為,自高自大,自以為超越一切神明,肆意詆譭萬神之神。他必亨通,一直到上帝發烈怒的日子結束。因為所定的必然成就。 37他不尊崇他祖先的神明,也不尊崇婦女們愛慕的神明或其他任何神明,因為他自認為超越一切。 38他反倒祭拜他祖先不認識的堡壘之神,向它獻上金銀寶石及貴重的禮物。 39他必靠外族神明的幫助攻打堅固的堡壘,將尊榮賜給順從他的人,派他們治理民眾,分給他們土地作獎賞。

40「到了末後,南方王必與北方王交戰。北方王必率領戰車、騎兵和大批戰船攻擊他,又如洪水般橫掃列國。 41他必侵入佳美之地,殺死成千上萬的人,只有以東摩押亞捫人的首領得以逃脫。 42他必攻擊列國,埃及也無法倖免。 43他必掌管埃及的金銀財寶,利比亞人和古實人必歸順他。 44但從東方和北方傳來的消息必令他震驚,他必大怒,出兵殺戮、毀滅許多人。 45他必在海和榮美的聖山之間搭起他宮殿般的帳幕。但他必滅亡,無人相助。