Danieli 10 – CCL & CCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Danieli 10:1-21

Masomphenya a Danieli a Munthu

1Chaka chachitatu cha Koresi mfumu ya Aperezi, Danieli amene ankatchedwa Belitesezara analandira mawu a vumbulutso. Uthenga wake unali woona ndipo anawumvetsa movutikira. Uthengawu anawumva kudzera mʼmasomphenya.

2Pa nthawi imeneyi, ine Danieli ndinalira kwa masabata atatu. 3Sindinadye chakudya chokoma; nyama ndi vinyo sizinakhudze milomo yanga ndi pangʼono pomwe; ndipo sindinadzole mafuta aliwonse mpaka patatha masabata atatu.

4Pa tsiku la 24 la mwezi woyamba, nditayima mʼmbali mwa mtsinje waukulu wa Tigirisi, 5ndinakweza maso ndipo ndinaona kuti pafupi ndi ine panali munthu wochokera ku Ufazi atavala zovala zosalala ndi lamba wa golide woyengeka bwino mʼchiwuno mwake. 6Thupi lake linali ngati mwala wonyezimira, nkhope yake ngati chiphaliwali, maso ake ngati muni wowala, manja ndi miyendo yake ngati mkuwa wowala, ndipo mawu ake ngati liwu la chikhamu cha anthu.

7Ine Danieli ndinali ndekha pamene ndinaona masomphenyawa; anthu amene anali ndi ine sanawaone, koma anadzazidwa ndi mantha kotero kuti anathawa ndi kukabisala. 8Choncho ndinatsala ndekha, ndikuonetsetsa masomphenya a ulemererowa. Ndiye nkhope yanga inasinthika, ndinalefuka, ndipo ndinalibenso mphamvu. 9Kenaka ndinamva iye akuyankhula, ndipo pamene ndinkamvetsera, ndinagwa chafufumimba ndi kugona tulo tofa nato.

10Dzanja linandikhudza ndi kundinyamula ndipo ndinachita ngati kuwerama pa mawondo manja atagwira pansi. 11Iye anati, “Danieli, iwe wokondedwa kwambiri, imirira ndipo uganizire mosamala mawu ndiyankhule kwa iwe, popeza tsopano ndatumidwa kwa iwe.” Atanena izi kwa ine ndinayimirira monjenjemera.

12Ndipo iye anapitiriza nati, “Usachite mantha Danieli. Kuyambira tsiku loyamba pamene unatsimikiza mtima kuti umvetse zinthuzi ndi kudzichepetsa pamaso pa Mulungu wako, pempho lako linamveka ndipo ndabwera kudzayankha mapemphero akowo. 13Koma mtsogoleri wa ufumu wa Peresiya ananditchingira pa masiku 21, kenaka Mikayeli, mmodzi mwa angelo akuluakulu anadza kudzandithandiza chifukwa ndinakhala komweko ndi mafumu a ku Peresiya. 14Tsopano ndafika kuti ndidzakufotokozere zimene zidzachitika kwa anthu a mtundu wako kutsogolo. Ndipo pali masomphenya enanso okhudza nthawi imene ikudza.”

15Pa nthawi yomwe ankanena izi kwa ine, ndinazolika nkhope yanga pansi kusowa chonena. 16Kenaka wina wa maonekedwe ngati munthu anakhudza milomo yanga, ndipo ndinatsekula pakamwa panga ndi kuyamba kuyankhula. Ndinati kwa amene anayima patsogolo panga, “Ine ndasweka mtima chifukwa cha masomphenyawa mbuye wanga, ndipo ndalefuka. 17Kodi ine mtumiki wamba wa mbuye wanga ndingathe bwanji kuyankhula ndi inu mbuye wanga? Mphamvu zanga zatha, ndipo ndikulephera kupuma.”

18Kenaka wooneka ngati munthu uja anandikhudzanso ndipo anandipatsa mphamvu. 19Iye anati, “Usachite mantha, munthu wokondedwa kwambiriwe. Mtendere ukhale ndi Iwe ndipo ukhale wolimba.”

Atayankhula nane, ndinalimbikitsidwa ndipo ndinati, “Yankhulani Mbuye wanga, popeza mwandipatsa mphamvu.”

20Ndipo iye anati, “Kodi ukudziwa chifukwa chimene ndabwerera kwa iwe? Ndiyamba ndabwerera kukamenyana ndi mtsogoleri wa ufumu wa Peresiya, ndipo ndikakanthana naye, kenaka mtsogoleri wa ufumu wa Grisi adzabwera. 21Koma ndikuwuza zimene zalembedwa mʼbuku la zoona koma palibe wondithandiza kulimbana nawo kupatula Mikayeli, kalonga wako.”

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

但以理书 10:1-21

底格里斯河边的异象

1波斯塞鲁士执政第三年,但以理,又名伯提沙撒,得到启示。这启示是真实的,是关于一场大争战的事。但以理通过异象明白了启示的意思。

2那时,我但以理悲伤了三个星期, 3期间没有吃过美味,没有尝过酒肉,没有抹过膏油。 4一月二十四日,我站在底格里斯河边, 5举目观看,见有一个人身穿细麻衣,腰束纯金的带子, 6身体如碧玉,面貌如闪电,眼睛如火炬,四肢如明亮的铜,声音如众人的呼喊。 7只有我但以理看见了这异象,跟我在一起的人都没有看见,但他们极其恐惧,纷纷逃匿, 8只剩下我一人观看这奇异的景象。我浑身无力,脸色苍白,精疲力尽。 9接着,我听见他说话的声音,一听见他的声音,我便俯伏在地上昏睡过去。 10忽然有一只手轻拍我,扶我用膝和手掌支撑起身体。 11他对我说:“倍受眷爱的但以理啊,要留心听我说,站起来吧,因为我是奉命到你这里来的。”他说完这话,我便战战兢兢地站起来。 12他说:“但以理啊,不要怕,从你在上帝面前谦卑地恳求明白这异象的第一天,你的祷告已蒙垂听。我是来答复你的。 13波斯国的守护神拦阻我二十一日。由于我滞留在波斯诸王那里,天使长米迦勒便来帮助我。 14我来是要使你明白将来你同胞的遭遇,因为这异象是关于将来的事。” 15他对我说话时,我低着头,说不出话。 16后来,有一位样子像人的用手摸我的嘴唇,我便开口对站在我面前的说:“我主啊,因为这异象,我痛苦不堪,毫无气力。 17仆人我怎能跟我主说话?我现在浑身无力,没有气息。”

18于是,那位样子像人的再次摸我,使我有力量。 19他对我说:“倍受眷爱的人啊,不要怕,愿你平安!要刚强勇敢。”我听到他的话,便有了力量,于是对他说:“我主啊,请说,因为你使我有了力量。” 20他说:“你知道我为什么要到你这里来吗?现在我要回去与波斯的守护神争战。我离开后,希腊的守护神就会来。 21除了你们的守护天使米迦勒以外,谁也不能帮助我抵挡他们。我来是要把记录在真理书上的事告诉你。