Chivumbulutso 7 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Chivumbulutso 7:1-17

Anthu 144,000

1Zitatha izi ndinaona angelo anayi atayima pa mbali zinayi za dziko lapansi, atagwira mphepo zinayi za dziko lapansi kuletsa kuti mphepo iliyonse isawombe pa dziko kapena pa nyanja kapena pa mtengo uliwonse. 2Kenaka ndinaona mngelo wina akuchokera kummawa, ali ndi chidindo cha Mulungu wamoyo. Iye anafuwulira angelo anayi aja amene anapatsidwa mphamvu yowononga dziko ndi nyanja kuti, 3“Musawononge dziko, nyanja ndi mitengo kufikira titalemba chizindikiro pa mphumi za atumiki a Mulungu wathu.” 4Choncho ndinamva chiwerengero cha amene ankayenera kulembedwa chizindikiro aja. Analipo okwanira 144,000 kuchokera ku mafuko onse a Israeli.

5Ochokera fuko la Yuda analipo 12,000 amene analembedwa chizindikiro.

Ochokera fuko la Rubeni analipo 12,000;

ochokera fuko la Gadi analipo 12,000;

6ochokera fuko la Aseri analipo 12,000;

ochokera fuko la Nafutali analipo 12,000;

ochokera fuko la Manase analipo 12,000;

7ochokera fuko la Simeoni analipo 12,000;

ochokera fuko la Levi analipo 12,000;

ochokera fuko la Isakara analipo 12,000;

8ochokera fuko la Zebuloni analipo 12,000;

ochokera fuko la Yosefe analipo 12,000;

ochokera fuko la Benjamini analipo 12,000.

Gulu Lalikulu la Anthu Ovala Zoyera

9Zitatha izi ndinayangʼana patsogolo panga ndipo ndinaona gulu lalikulu la anthu loti munthu sangathe kuliwerenga lochokera dziko lililonse, fuko lililonse, mtundu wa anthu uliwonse ndi chiyankhulo chilichonse, atayima patsogolo pa mpando waufumu, pamaso pa Mwana Wankhosa. Iwo anali atavala mikanjo yoyera ndi kunyamula nthambi za kanjedza mʼmanja mwawo. 10Ndipo ankafuwula mokweza kuti:

“Chipulumutso chimachokera kwa Mulungu wathu,

wokhala pa mpando waufumu

ndi kwa Mwana Wankhosa.”

11“Angelo onse anayimirira kuzungulira mpando waufumu uja, kuzunguliranso akuluakulu aja ndi zamoyo zinayi zija. Angelo aja anadzigwetsa pansi chafufumimba patsogolo pa mpando waufumu napembedza Mulungu. 12Iwo anati,

“Ameni!

Matamando ndi ulemerero,

nzeru, mayamiko, ulemu,

ulamuliro ndi mphamvu

zikhale kwa Mulungu wathu kunthawi zanthawi,

Ameni!”

13Pamenepo mmodzi wa akuluakulu aja anandifunsa kuti, “Kodi avala mikanjo yoyerawa ndani ndipo akuchokera kuti?”

14Ine ndinayankha kuti, “Mbuye wanga mukudziwa ndinu.”

Tsono iye anandiwuza kuti, “Amenewa ndi amene anatuluka mʼmazunzo aakulu aja. Anachapa mikanjo yawo naziyeretsa mʼmagazi a Mwana Wankhosa. 15Nʼchifukwa chake,

“iwowa ali patsogolo pa mpando waufumu wa Mulungu

ndipo akutumikira usana ndi usiku mʼNyumba ya Mulungu;

ndipo Iye wokhala pa mpando waufumu

adzawaphimba ndi tenti yake.

16‘Iwowa sadzamvanso njala,

sadzamvanso ludzu,

dzuwa kapena kutentha kulikonse

sikudzawawotcha.’

17Pakuti Mwana Wankhosa amene ali pakati pa mpando waufumu

adzakhala mʼbusa wawo.

‘Iye adzawatsogolera ku akasupe a madzi amoyo.’

‘Ndipo Mulungu adzawapukuta misozi yonse mʼmaso mwawo.’ ”