Chivumbulutso 22 – CCL & HHH

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Chivumbulutso 22:1-21

Mtsinje Wamoyo

1Ndipo mngeloyo anandionetsa mtsinje wamadzi amoyo, oyera ngati mwala wa krustalo ukutuluka ku mpando waufumu wa Mulungu ndi wa Mwana Wankhosa, 2Ukuyenda pakati pa msewu waukulu wa mu mzindawo. Mbali iliyonse ya mtsinjewo kunali mtengo wamoyo, utabala zipatso khumi ndi ziwiri. Kubereka zipatso mwezi uliwonse. Ndipo masamba a mtengowo ndi mankhwala wochiritsa anthu a mitundu ina. 3Sipadzakhalanso temberero lililonse. Mpando waufumu wa Mulungu ndi wa Mwana Wankhosa udzakhala mu mzindawo, ndipo atumiki ake adzamutumikira. 4Iwo adzaona nkhope yake ndipo dzina lake lidzalembedwa pa mphumi zawo. 5Sipadzakhalanso usiku. Sadzafuna kuwala kwa nyale kapena kwa dzuwa pakuti Ambuye Mulungu adzakhala kuwala kwawo. Ndipo adzalamulira kwamuyaya.

6Mngeloyo anandiwuza kuti, “Mawu awa ndi okhulupirika ndi owona. Ambuye Mulungu wa mizimu ya aneneri anatumiza mngelo wake kudzaonetsa atumiki ake zinthu zimene ziyenera kuchitika posachedwapa.”

Yesu Akubweranso

7“Taonani, ndikubwera posachedwa! Wodala ndi amene asunga mawu oneneratu za kutsogolo a mʼbuku ili.”

8Ine Yohane, ndine amene ndinamva ndi kuona zinthu izi. Ndipo pamene ndinamva ndi kuona izi ndinagwa pansi kuti ndipembedze mngelo amene amandionetsa zimenezi. 9Koma mngeloyo anandiwuza kuti, “Usatero ayi! Ine ndine wotumikira monga iwe pamodzi ndi abale ako aneneri ndi onse amene amasunga mawu a mʼbuku pembedzani Mulungu.”

10Kenaka anandiwuza kuti, “Usabise mawu onena zamʼtsogolo a mʼbuku ili chifukwa nthawi yayandikira. 11Wochita zoyipa apitirire kuchita zoyipazo; wochita zonyansa apitirire kuchita zonyansazo; wochita zabwino apitirire kuchita zabwinozo; ndipo woyera mtima apitirire kukhala woyera mtima.”

Mawu Otsiriza: Kuyitanidwa ndi Chenjezo

12“Taonani, ndikubwera posachedwa! Ndikubwera ndi mphotho zanga kuti ndidzapereke kwa aliyense malinga ndi zimene anachita. 13Ine ndine Alefa ndi Omega, Woyamba ndi Wotsiriza, Chiyambi ndi Chimaliziro ndine.

14“Odala amene achapa mikanjo yawo, kuti akhale ndi ufulu wopita ku mtengo wamoyo ndi kuti akalowe mʼzipata za mu mzindawo. 15Kunja kuli agalu, amatsenga, achiwerewere, akupha anthu, opembedza mafano ndi aliyense amene amakonda bodza ndi kulichita.

16“Ine Yesu, ndatuma mngelo wanga kuti achitire umboni uwu ku mipingo. Ine ndine Muzu ndi Chipatso cha Davide ndipo ndine Nthanda Yonyezimira.”

17Mzimu Woyera ndi mkwatibwi akuti, “Bwerani!” Ndipo amene akumva anena kuti Bwerani! Iye amene ali ndi ludzu abwere, ndipo aliyense amene afuna alandire mphatso yaulere ya madzi amoyo.

18Ndikuchenjeza aliyense amene akumva mawu onena zamʼtsogolo a mʼbukuli kuti, “Ngati wina awonjezerapo kalikonse, Mulungu adzamuwonjezera miliri imene yalembedwa mʼbuku ili. 19Ndipo wina akachotsapo mawu onena zamʼtsogolo a mʼbuku ili, Mulungu adzachotsa gawo lake pa mtengo wamoyo ndi la mu mzinda woyera zimene zanenedwa mʼbuku ili.”

20Iye amene akuchitira umboni pa zinthu izi akuti, “Inde, Ine ndikubwera posachedwa.”

Ameni. Bwerani Ambuye Yesu.

21Chisomo cha Ambuye Yesu chikhale ndi anthu onse. Ameni.

Habrit Hakhadasha/Haderekh

התגלות 22:1-21

1לאחר מכן הוא הראה לי נהר מים חיים, זכים כבדולח, יוצא מכיסא האלוהים והשה 2וזורם אל הרחוב המרכזי. על כל אחת משתי גדות הנהר היה נטוע עץ־חיים שנושא שנים־עשר סוגי פירות, בכל חודש פרי אחר, ועלי העץ משמשים כתרופה לעמים השונים.

3בעיר הקודש לא יהיה יותר כל דבר רע וטמא, כי יהיה בה כיסא המלכות של אלוהים והשה, ועבדיו ישרתוהו. 4עבדיו יראו את פניו, ושמו יהיה כתוב על מצחם. 5לא יהיה יותר לילה, ולא יהיה צורך בנרות או באור השמש, כי ה׳ אלוהים יאיר להם, והם ימלכו לעולם ועד.

6”דברים אלה אמיתיים ונכונים“, אמר לי המלאך. ”האלוהים אשר מעניק השראה לנביאים שלח את מלאכו להראות לעבדיו את אשר יתרחש בקרוב.“

7”אני בא במהרה!“ אמר ישוע. ”ברוכים השומרים את דברי הנבואה של הספר הזה.“

8אני, יוחנן, שמעתי וראיתי את כל הדברים האלה. כאשר שמעתי וראיתי אותם, נפלתי לרגלי המלאך שהראה לי את כל זאת. כאשר עמדתי להשתחוות לו, 9הוא עצר בעדי ואמר: ”לא, אל תשתחווה לי, כי אני עבד המשיח כמוך, כאחיך המאמינים, כנביאים וככל השומרים את דברי הספר הזה. עליך להשתחוות לאלוהים.“

10המלאך הורה לי במפורש: ”אל תחתום את הדברים שכתבת, כי קרוב מועד התרחשותם. 11עד אז הגזלן ימשיך לגזול, הטמא ימשיך במעשי טומאתו; הצדיק יוסיף על צדקתו, והקדוש יוסיף על קדושתו.“

12”אני בא במהרה,“ אמר ישוע, ”ואביא איתי שכר שאותו אשלם לכל איש כגמולו. 13אני האלף והתו, ההתחלה והסוף, הראשון והאחרון.“

14ברוכים המכבסים את גלימותיהם (והשומרים את מצוותיו), על־מנת לזכות בפרי עץ־החיים ולהיכנס לעיר דרך השערים. 15הכלבים, המכשפים, הזונים, הרוצחים, עובדי האלילים, אוהבי השקר והרמאים יישארו מחוץ לעיר.

16”אני, ישוע, שלחתי את מלאכי אליך כדי לספר דברים אלה לקהילות. אני שורש דויד וצאצאו, אני כוכב נוגה השחר.“

17”בוא!“ קוראים הרוח והכלה. וכל השומע את קריאתם יאמר: ”בוא!“

בואו, כל הצמאים, שתו את מים־החיים – מתנת חינם לכל מי שרוצה.

18אני מזהיר את כל קוראי הספר הזה: כל המוסיף על הכתוב יוסיף לו אלוהים את המגפות שכתובות בספר הזה! 19כל הגורע מדברי הספר הזה, יגרע אלוהים את חלקו מעץ־החיים ומעיר הקודש שנזכרים בספר הזה.

20המעיד עדות זאת אומר: ”אכן, אני בא במהרה!“ אמן! בואה־נא, אדון ישוע!

21חסד ישוע המשיח אדוננו יהיה עם כל המאמינים. – אמן.