Chivumbulutso 18 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Chivumbulutso 18:1-24

Kugwa kwa Babuloni

1Zitatha izi ndinaona mngelo wina akutsika kuchokera kumwamba. Iye anali ndi ulamuliro waukulu, ndipo dziko lapansi linawala ndi ulemerero. 2Mngeloyo anafuwula ndi mawu amphamvu kuti:

“ ‘Wagwa! Wagwa Babuloni Wamkulu!’

Wasandulika mokhalamo ziwanda

ndi kofikako mizimu yonse yoyipa

ndi mbalame zonse zonyansa

ndi zodetsedwa.

3Pakuti mayiko onse amwa

vinyo ozunguza mutu wazigololo zake.

Mafumu a dziko lapansi achita naye chigololo,

ndipo amalonda a dziko lapansi analemera kuchokera pa zolakalaka zake zosefukira.”

Awachenjeza kuti Athawe Chiweruzo cha Babuloni

4Ndiponso ndinamva mawu ena kuchokera kumwamba akuti:

“ ‘Anthu anga tulukani, mwa iye,’

mungachimwe naye

kuti musadzalandire nawo gawo lililonse la miliri yake;

5pakuti machimo ake awunjikana mpaka kumwamba,

ndipo Mulungu wakumbukira milandu yake.

6Bwezerani Iye monga momwe iye anakuchitirani.

Mubwezereni mowirikiza pa zimene anachita.

Mumusakanizire magawo awiri kuchokera mʼchikho chake.

7Mumuzunze, kumumvetsa chisoni kwambiri

monga mwaulemerero ndi zolakalaka

zimene anadzaza mu mtima mwake. Iye anadzikuza nʼkumati,

‘Ndinakhala monga mfumu yayikazi,

ine sindine wamasiye

ndipo sindidzalira maliro.’

8Chifukwa chake miliri yake idzamugonjetsa tsiku limodzi;

imfa, kulira maliro ndi njala.

Iye adzanyeka ndi moto

pakuti wamphamvu ndi Mulungu Ambuye amene wamuweruza.

Tsoka la Babuloni

9“Mafumu a dziko lapansi, amene anachita naye chigololo nachita naye pamodzi zosangalatsa moyo uno, akadzaona utsi wa kunyeka kwake, adzalira nakhuza maliro ake. 10Iwo adzayima kutali nalira chifukwa choopsedwa ndi mazunzo ake.

“ ‘Tsoka! Tsoka mzinda waukulu

iwe, Babuloni mzinda wamphamvu!

Mu ora limodzi chiwonongeko chako chafika!’

11“Amalonda a dziko lapansi adzalira nakhuza maliro ake chifukwa palibenso amene akugula katundu wawo, 12katundu wagolide, siliva, miyala yamtengo wapamwamba ndi ngale; nsalu zoyera kwambiri zapamwamba ndi zofiira; nsalu zasilika ndi zapepo; mitengo iliyonse yonunkhira ndi zinthu zilizonse zopangidwa ndi mnyanga, kapena matabwa ogulidwa ndi ndalama zambiri kapena mkuwa kapena chitsulo ndi mwala wonyezimira; 13zokometsera zakudya, mure, lubani ndi zofukiza zina, vinyo ndi mafuta a olivi, ufa wosalala ndi tirigu; ngʼombe ndi nkhosa; akavalo ndi ngolo; ndi anthu adzagulitsidwa ukapolo.

14“Iwo adzanena kuti, ‘Chipatso chimene unachilakalaka chakuchokera. Chuma chako chonse ndi ulemerero zatha, sizidzapezekanso.’ 15Amalonda amene anagulitsa zinthu izi napeza chuma kuchokera kwa iye adzayima patali potero ataopsedwa ndi mazunzo ake. Adzalira ndi kukhuza maliro 16ndipo adzalira mokuwa kuti,

“ ‘Tsoka! Tsoka! Mzinda waukulu,

iwe wovala nsalu zoyera kwambiri, zapepo ndi zofiira,

ndi wonyezimira ndi golide, miyala yamtengo wapamwamba ndi ngale!

17Chuma chambiri choterechi chafika powonongeka mu ora limodzi!’

“Oyendetsa sitima ndi onse oyenda pa sitima ya pamadzi, ogwira ntchito mʼsitima ndi onse amene amadalira nyanja pamoyo wa tsiku ndi tsiku adzayima patali potero. 18Akadzaona utsi wa kunyeka kwake, adzakuwa kuti, ‘Kodi panalinso mzinda wina ngati mzinda waukuluwu?’ 19Adzathira fumbi pamitu pawo ndipo adzalira nakhuza maliro kuti,

“Tsoka! Tsoka mzinda waukulu iwe,

kumene onse anali ndi sitima pa nyanja

analemera kudzera mʼchuma chake!

Mu ora limodzi wawonongedwa.

20“Kondwerani chifukwa cha iye inu kumwamba!

Kondwerani oyera mtima

ndi atumwi ndi aneneri!

Mulungu wamuweruza iye

monga momwe anakuchitirani inu.”

Chiwonongeko Chotsiriza cha Babuloni

21Kenaka mngelo wamphamvu ananyamula mwala waukulu ngati mphero yayikulu nawuponya mʼnyanja nanena kuti,

“Mwa mphamvu chonchi

mzinda waukulu wa Babuloni udzaponyedwa pansi,

sudzapezekanso.

22Mwa iwe simudzamvekanso liwu la woyimba zeze, ndi akatswiri a zoyimbayimba,

oyimba zitoliro, ndi lipenga.

Mwa iwe simudzapezekanso

mʼmisiri wina aliyense.

Mwa iwe simudzapezekanso

phokoso la mphero.

23Kuwala kwa nyale

sikudzawunikanso mwa inu.

Mawu a mkwati ndi mkwatibwi

sadzamvekanso mwa iwe.

Amalonda anu anali akuluakulu a dziko lapansi.

Mitundu yonse inasokonezedwa ndi zamatsenga zako.

24Mwa iye munapezeka magazi a aneneri ndi a oyera mtima,

ndi onse amene anaphedwa pa dziko lapansi.”