Chivumbulutso 16 – CCL & CCBT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Chivumbulutso 16:1-21

Mbale Zisanu ndi Ziwiri za Mkwiyo wa Mulungu

1Kenaka ndinamva mawu ofuwula kuchokera ku Nyumba ya Mulungu ija kuwuza angelo asanu ndi awiri kuti, “Pitani, katsanulireni pa dziko lapansi ukali wa Mulungu umene uli mʼmbale zisanu ndi ziwirizi!”

2Mngelo woyamba anapita natsanula mbale yake pa dziko lapansi ndipo zilonda zoyipa ndi zowawa zinabuka pa anthu amene anali ndi chizindikiro cha chirombo chija, napembedza fano lake.

3Mngelo wachiwiri anapita natsanula mbale yake pa nyanja ndipo madzi ake anasanduka magazi, magazi ake ngati a munthu wakufa. Chamoyo chilichonse cha mʼnyanjamo chinafa.

4Mngelo wachitatu anapita natsanula mbale yake pa mitsinje ndi akasupe amadzi ndipo zinasanduka magazi. 5Kenaka ndinamva mngelo wolamulira madzi uja akuti,

“Inu mwachita chilungamo, Inu Woyerayo,

amene mulipo ndipo munalipo;

6pakuti iwo anakhetsa magazi a oyera anu ndi aneneri anu,

nʼchifukwa chake mwawapatsa magazi kuti amwe, zomwe zikuwayenera.”

7Kenaka ndinamva mawu ochokera ku guwa lansembe akuti,

“Inde, Ambuye Mulungu Wamphamvuzonse,

chiweruzo chanu ndi choona ndi cholungama.”

8Mngelo wachinayi anapita natsanula mbale yake pa dzuwa ndipo dzuwa linapatsidwa mphamvu yopsereza anthu ndi moto. 9Anapserera nako kutentha kwakukuluko ndipo anatukwana Mulungu, amene anali ndi ulamuliro pa miliri imeneyi, koma anakana kulapa ndi kumulemekeza.

10Mngelo wachisanu anapita natsanula mbale yake pa mpando waufumu wa chirombo chija ndipo mdima unagwa ponse pamene panali ufumu wake. Anthu analuma malilime awo chifukwa cha ululu. 11Ndipo anatukwana Mulungu wakumwamba chifukwa cha maululu awo ndi zilonda zawo koma anakana kulapa pa zimene anachita.

12Mngelo wachisanu ndi chimodzi anapita natsanula mbale yake pa mtsinje waukulu wa Yufurate, ndipo madzi ake anaphwa kuti pakhale njira yodzera mafumu ochokera kummawa. 13Kenaka ndinaona mizimu yoyipa itatu imene inkaoneka ngati achule; inatuluka mʼkamwa mwa chinjoka chija, mʼkamwa mwa chirombo chija ndi mʼkamwa mwa mneneri wonyenga uja. 14Imeneyi ndiyo mizimu ya ziwanda imene imachita zizindikiro zodabwitsa ndipo imatuluka kupita kwa mafumu a dziko lonse, kukawasonkhanitsa ku nkhondo ya pa tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuzonse.

15“Taonani, ndikubwera ngati mbala! Wodala munthu amene ali maso, nasunga zovala zake, kuti asayende maliseche kuti angaonetse maliseche ake.”

16Kenaka mizimu ija inasonkhanitsa pamodzi mafumu ku malo amene mʼChihebri amatchedwa Armagedo.

17Mngelo wachisanu ndi chiwiri anatsanulira mbale yake mu mlengalenga ndipo ku Nyumba ya Mulungu kunamveka mawu ofuwula kuchokera ku mpando waufumu kuti, “Kwatha!” 18Kenaka kunachitika mphenzi, phokoso, mabingu ndi chivomerezi choopsa. Chivomerezi ngati ichi sichinachitikepo chikhalire cha munthu pa dziko lapansi. Chinali chivomerezi choopsa kwambiri. 19Mzinda waukuluwo unagawika magawo atatu ndipo mizinda ya mitundu ya anthu inagwa. Mulungu anakumbukira Babuloni Wamkulu namupatsa chikho chake chodzaza ndi vinyo wa ukali wa mkwiyo wake. 20Chilumba chilichonse chinathawa ndipo mapiri sanaonekenso. 21Matalala akuluakulu olemera pafupifupi makilogalamu makumi asanu anagwa kuchokera kumwamba kugwera pa anthu. Ndipo anthu anatukwana Mulungu chifukwa cha mliri wa matalala popeza unali mliri woopsa kwambiri.

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

啟示錄 16:1-21

1我聽見殿中有宏亮的聲音對七位天使說:「去將那盛滿上帝烈怒的七個碗傾倒在地上。」

2第一位天使離去,將碗倒在了地上,那些有怪獸的印記、敬拜獸像的人身上長出奇痛無比的毒瘡。

3第二位天使將碗倒在了海洋裡,海水變得像死人的血,海中的活物都死光了。

4第三位天使將碗倒在了江河與水泉裡,水就變成了血。 5我聽見掌管各水源的天使說:

「昔在今在的聖者啊!

你是公義的,

因為你施行了審判。

6由於他們流了眾聖徒和先知們的血,

現在你使他們喝血,

這正是他們應得的報應。」

7我又聽見從祭壇發出的聲音說:

「是的,全能的主上帝,

你的判決真實公義。」

8第四位天使將碗倒在太陽上,太陽就變得炙熱如火,可以灼傷人。 9人們被炙熱灼傷,就褻瀆掌管這些災禍的上帝的名,他們毫無悔意,不肯歸榮耀給上帝。

10第五位天使將碗倒在那海中怪獸的座位上,牠的國便被黑暗籠罩,牠的國民痛苦難當,咬自己的舌頭。 11他們因為痛苦和毒瘡就褻瀆天上的上帝,不肯為自己的所作所為悔改。

12第六位天使將碗倒在幼發拉底大河上,河水立刻乾了,為東方各國的王預備了道路。 13我又看見三個像青蛙一樣的污鬼分別從巨龍、怪獸和假先知的口裡跳出來。 14其實牠們都是鬼魔的靈,能行奇蹟。牠們到普天下召集各王,預備在全能上帝的大日子來臨時聚集爭戰。

15「看啊!我要像賊一樣出其不意地來到。那警醒等候,看守自己衣裳,不致赤身行走蒙受羞辱的人有福了。」

16鬼魔把眾王召集到一個希伯來話叫哈米吉多頓的地方。

17第七位天使將碗倒在空中時,從殿裡的寶座上傳出響亮的聲音說:「成了!」 18隨後雷電交加,伴隨著巨響,還有空前劇烈的大地震。 19巴比倫大城裂作三段,其他各國的城邑也都倒塌了。上帝並沒有忘記巴比倫大城的罪惡,要把那杯盛滿祂烈怒的酒給她喝。 20海島都沉沒了,山嶺也都不見了, 21又有重達三十四公斤16·21 三十四公斤」希臘文是「一他連得」。的巨型冰雹從天而降,打在世人身上。世人無法忍受這極大的災禍,就褻瀆上帝。