Chivumbulutso 12 – CCL & HOF

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Chivumbulutso 12:1-18

Mayi ndi Chinjoka

1Chizindikiro chachikulu chinaoneka kuthambo; mayi atavala dzuwa, mapazi ake ataponda mwezi, pamutu pake pali chipewa chaufumu chokhala ndi nyenyezi khumi ndi ziwiri. 2Mayiyo anali woyembekezera ndipo pa nthawi yake yochira analira mokuwa chifukwa cha ululu wakubala. 3Kenaka ku thambo kunaonekanso chizindikiro china; chinjoka chachikulu kwambiri, chofiira chomwe chinali ndi mitu isanu ndi iwiri ndi nyanga khumi; pamutu uliwonse chitavala chipewa chaufumu. 4Mchira wake unakokolola gawo limodzi la magawo atatu a nyenyezi kuzichotsa ku thambo ndi kuziponya pa dziko lapansi. Chinjoka chija chinadzayima patsogolo pa mayi uja amene anali pafupi kuberekayu kuti mwanayo akangobadwa chimudye. 5Mayiyo anabereka mwana wamwamuna amene adzalamulira anthu a mitundu ina yonse ndi ndodo yachitsulo. Ndipo mwanayo analandidwa ku dzanja la mayiyo ndi kupita naye kwa Mulungu ku mpando wake waufumu. 6Mayiyo anathawira ku chipululu ku malo kumene Mulungu anamukonzera, kumene akasamalidweko masiku 1,260.

7Zitatero, kumwamba kunayambika nkhondo. Mikayeli ndi angelo ake kumenyana ndi chinjoka chija. Chinjokacho ndi angelo ake anabwezeranso. 8Koma analibe mphamvu ndipo anagonjetsedwa nathamangitsidwa kumwambako. 9Chinjoka chachikulu chija chinagwetsedwa pansi. Ichocho ndiye njoka yakalekale ija yotchedwa Mdierekezi kapena Satana, amene amasocheretsa anthu a pa dziko lonse lapansi. Chinaponyedwa pa dziko la pansi pamodzi ndi angelo ake.

10Kenaka ndinamva mawu ofuwula kumwamba akunena kuti,

“Tsopano chipulumutso, mphamvu,

ufumu wa Mulungu wathu

ndi ulamuliro wa Khristu wake zabwera.

Pakuti woneneza abale athu uja,

amene amangokhalira kuwaneneza pamaso pa Mulungu usana ndi usiku,

wagwetsedwa pansi.

11Abale athuwo anamugonjetsa

ndi magazi a Mwana Wankhosa

ndiponso mawu a umboni wawo.

Iwo anadzipereka kwathunthu,

moti sanakonde miyoyo yawo.

12Choncho, kondwerani, inu dziko lakumwamba

ndi onse okhala kumeneko!

Koma tsoka dziko lapansi ndi nyanja

chifukwa Mdierekezi wagwetsedwa kwa inu!

Iye wadzazidwa ndi ukali

chifukwa akudziwa kuti nthawi yake ndi yochepa.”

13Pamene chinjokacho chinaona kuti chagwetsedwa pa dziko lapansi, chinayamba kuthamangitsa mayi uja amene anali atabala mwana wamwamunayu. 14Mayiyo anapatsidwa mapiko awiri a chiwombankhanga chachikulu kuti athawire ku malo ake aja a ku chipululu. Kumeneko adzasamalidwako zaka zitatu ndi theka kuti chinjoka chija chisamupeze. 15Kenaka chinjoka chija chinalavulira mayiyo madzi ambiri ngati mtsinje, kuti madziwo amukokolole. 16Koma dziko lapansi linamuthandiza mayiyo. Nthaka inatsekuka ndi kumeza mtsinje uja unachokera mʼkamwa mwa chinjokacho. 17Pamenepo chinjokacho chinamupsera mtima mayiyo ndipo chinachoka kupita kukachita nkhondo ndi ana ena onse a mayiyo, ndiye kuti anthu amene anasunga malamulo a Mulungu ndi kuchitira umboni za Yesu.

18Kenaka ndinaona chinjokacho chitayima mʼmbali mwa nyanja.

Hoffnung für Alle

Offenbarung 12:1-18

Die Frau und die beiden Tiere

(Kapitel 12–14)

Die Frau und der Drache

1Am Himmel sah man jetzt eine gewaltige Erscheinung: eine Frau, die mit der Sonne bekleidet war und den Mond unter ihren Füßen hatte. Auf dem Kopf trug sie eine Krone aus zwölf Sternen. 2Sie war hochschwanger und schrie unter den Geburtswehen vor Schmerz. 3Dann gab es noch eine Erscheinung am Himmel: Plötzlich sah ich einen riesigen, feuerroten Drachen mit sieben Köpfen und zehn Hörnern. Auf jedem seiner Köpfe trug er eine Krone. 4Mit seinem Schwanz fegte er ein Drittel aller Sterne vom Himmel und schleuderte sie auf die Erde. Der Drache stellte sich vor die Frau; denn er wollte ihr Kind verschlingen, sobald es geboren war. 5Die Frau brachte einen Sohn zur Welt, der einmal mit eisernem Zepter über die Völker der Erde herrschen sollte. Das Kind wurde zu Gott entrückt und vor seinen Thron gebracht. 6Die Frau aber floh in die Wüste, wo Gott selbst einen Zufluchtsort für sie vorbereitet hatte. 1260 Tage sollte sie dort versorgt werden.

7Dann brach im Himmel ein Krieg aus: Michael und seine Engel griffen den Drachen an. Der Drache schlug mit seinem Heer von Engeln zurück; 8doch sie verloren den Kampf und durften nicht länger im Himmel bleiben. 9Der große Drache ist niemand anders als der Teufel oder Satan, die listige Schlange, die schon immer die ganze Welt verführt hat. Er wurde mit allen seinen Engeln aus dem Himmel auf die Erde hinuntergestürzt.

10Jetzt hörte ich eine gewaltige Stimme im Himmel rufen:

»Nun hat Gott den Sieg errungen,

er hat seine Stärke gezeigt

und seine Herrschaft aufgerichtet!

Alle Macht liegt in den Händen dessen,

den er als König auserwählt und eingesetzt hat:

Jesus Christus12,10 Wörtlich: (in den Händen) seines Christus. – »Christus« ist die griechische Übersetzung des hebräischen »Messias« (= der gesalbte König). Vgl. »salben/Salbung« in den Sacherklärungen.! Denn der Ankläger ist gestürzt,

der unsere Brüder und Schwestern

Tag und Nacht vor Gott beschuldigte.

11Sie haben ihn besiegt durch das Blut des Lammes

und weil sie sich zu dem Lamm bekannt haben.

Für dieses Bekenntnis haben sie ihr Leben

eingesetzt und den Tod nicht gefürchtet.

12Darum freu dich nun, Himmel,

freut euch alle, die ihr darin wohnt!

Aber wehe euch, Erde und Meer!

Der Teufel ist zu euch herabgekommen.

Er schnaubt vor Wut, denn er weiß,

dass ihm nicht mehr viel Zeit bleibt.«

13Als der Drache merkte, dass er auf die Erde hinabgeworfen worden war, verfolgte er die Frau, die den Sohn geboren hatte. 14Doch Gott gab der Frau die starken Flügel eines Adlers. So konnte sie an ihren Zufluchtsort in der Wüste fliehen. Dreieinhalb Jahre12,14 Wörtlich: Eine Zeit und (zwei) Zeiten und eine halbe Zeit. – Vgl. Daniel 7,25; 12,7. wurde sie hier versorgt und war vor den Angriffen des Drachen, der bösen Schlange, sicher. 15Doch die Schlange gab nicht auf. Sie ließ eine gewaltige Wasserflut aus ihrem Rachen schießen, mit der die Frau fortgerissen werden sollte. 16Aber die Erde half der Frau. Sie öffnete sich und verschlang die Wassermassen, die der Drache ausspuckte. 17Darüber wurde der Drache so wütend, dass er jetzt alle anderen Nachkommen dieser Frau bekämpfte. Das sind die Menschen, die nach Gottes Geboten leben und sich zu Jesus bekennen. 18Und der Drache begab sich an den Strand des Meeres.