Aroma 9 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Aroma 9:1-33

Chisankho Chopambana cha Mulungu

1Ine ndikunena zoona mwa Khristu. Sindikunama ndipo chikumbumtima changa kudzera mwa Mzimu Woyera chikundichitira umboni. 2Ndili ndi chisoni chachikulu ndipo ndikumva kupwetekeka kosalekeza mu mtima mwanga. 3Pakuti ndikanafuna ine mwini nditatembereredwa ndi kuchotsedwa mwa Khristu chifukwa cha abale anga, amene ndi a mtundu wanga, 4anthu Aisraeli. Iwo anasankhidwa kukhala ana. Mulungu anawapatsa ulemerero, anachita nawo mapangano, kuwapatsa Malamulo, Nyumba yopembedzeramo ndi malonjezano ake. 5Awo ndi makolo athu. Kuchokera kwa iwo mʼthupi ndi kumene kunachokera makolo a Khristu Yesu amene ndi Mulungu wolamulira zinthu zonse, alemekezeke mpaka muyaya! Ameni.

6Sikuti mawu a Mulungu analephera. Pakuti si onse obadwa mwa Israeli amene ndi Israeli. 7Kapena kuti ana ake chifukwa anachokera mwa Abrahamu. Koma zidzukulu zako zidzachokera mwa Isake. 8Kutanthauza kuti, si ana obadwa mʼthupi amene ndi ana a Mulungu koma ndi ana a lonjezano amene amatengedwa kukhala zidzukulu za Abrahamu. 9Pakuti Mulungu analonjeza ponena kuti, “Pa nthawi yake ngati yomwe ino chaka chamawa ndidzabweranso, ndipo Sara adzakhala ndi mwana wamwamuna.”

10Ndipo si pokhapo ayi. Ana awiri a Rebeka aja abambo awo anali mmodzi, kholo lathu Isake. 11Komabe, ana amapasawa asanabadwe kapena asanachite chilichonse chabwino kapena choyipa, nʼcholinga choti chifuniro cha Mulungu chosankhiratu munthu aliyense chipitirire, 12osati chifukwa cha ntchito za munthu koma chifuniro cha Iye mwini, anawuza Rebeka kuti, “Wamkulu adzatumikira wamʼngʼono.” 13Monga momwe kwalembedwa kuti, “Ine ndinakonda Yakobo, koma ndinamuda Esau.”

14Nanga tsono tidzanena chiyani? Kodi Mulungu ndi osalungama? Ayi, ndi pangʼono pomwe! 15Pakuti Mulungu anawuza Mose kuti,

“Ine ndidzachitira chifundo amene ndikufuna kumuchitira chifundo,

ndipo ndidzakomera mtima amene ndikufuna kumukomera mtima.”

16Nʼchifukwa chake, izi sizitengera zokhumba za munthu kapena kuyesetsa koma chifundo cha Mulungu. 17Malemba akuti Mulungu anamuwuza Farao kuti, “Ine ndakuyika kukhala mfumu ndi cholinga choti ndionetse mphamvu zanga, kuti mwa iwe dzina langa litchuke pa dziko lonse lapansi.” 18Choncho Mulungu amachitira chifundo munthu amene akufuna kumuchitira chifundo ndipo amawumitsa mtima munthu amene Iye akufuna kumuwumitsa mtima.

19Tsono mmodzi wa inu nʼkundifunsa kuti, “Nanga nʼchifukwa chiyani Mulungu amatipeza olakwa? Nanga ndani amene amakana chifuniro chake?” 20Koma ndiwe yani, munthu wamba, woti nʼkutsutsana ndi Mulungu? “Kodi chimene chinawumbidwa nʼkufunsa amene anachiwumba kuti, ‘Kodi unandiwumbiranji motere?’ ” 21Kodi wowumba alibe ufulu wowumba kuchokera ku dothi lomwelo mbiya yamtengowapatali ndi ina yamtengo wotsika?

22Koma Mulungu, anafuna kuonetsa mkwiyo wake ndi kuti mphamvu yake idziwike. Iye anapirira modekha mtima kwambiri zochita za anthu omwe anawakwiyirawo amene anayeneradi chiwonongeko. 23Iye anachita izi kufuna kuonetsa kulemera kwa ulemerero wake ndi kuti udziwike kwa amene analandira chifundo chake. Iye anawakonzeratu kuti alandire ulemerero wake 24ngakhale ifenso amene anatiyitana osati kuchokera kwa Ayuda okha komanso kwa a mitundu ina. 25Monga momwe Mulungu akunenera mʼbuku la Hoseya kuti,

“Amene sanali anthu anga ndidzawatcha ‘anthu anga;’

ndipo Ine ndidzatcha ‘wokondedwa wanga’ amene sali wokondedwa wanga,”

26ndipo,

“Pamalo omwewo pamene ananena kuti,

‘Sindinu anthu anga,’

pomweponso adzawatchula kuti, ‘Ana a Mulungu wamoyo.’ ”

27Yesaya anafuwula za Aisraeli kuti,

“Ngakhale chiwerengero cha Aisraeli chingakhale ngati mchenga wa ku nyanja,

otsala okha ndiye adzapulumuke.

28Pakuti Ambuye adzagamula milandu

ya anthu pa dziko lapansi mofulumira ndi kumaliziratu.”

29Monga momwe Yesaya ananena malo ena kuti,

“Ngati Yehova Wamphamvuzonse

akanapanda kutisiyira zidzukulu,

ife tikanawonongeka

ngati anthu a ku Sodomu, tikanakhala ngati anthu a ku Gomora.”

Kusakhulupirira kwa Aisraeli

30Kodi nanga tidzati chiyani? Tidzati a mitundu ina amene sanafune chilungamo analandira chilungamo chachikhulupiriro 31koma Aisraeli, amene anafuna chilungamo cha lamulo sanachilandire. 32Chifukwa chiyani? Chifukwa iwo sanachifune ndi chikhulupiriro koma ngati mwa ntchito. Iwo anapunthwa pa “Mwala wopunthwitsa.” 33Monga momwe kwalembedwa kuti,

“Taonani, Ine ndikuyika mwala mu Ziyoni wopunthwitsa anthu,

thanthwe limene limagwetsa anthu.

Koma amene akhulupirira Iye sadzachititsidwa manyazi.”