Aroma 3 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Aroma 3:1-31

Kukhulupirika kwa Mulungu

1Nanga kodi pali ubwino wotani pokhala Myuda, kapena muli ubwino wanjinso mu mdulidwe? 2Ubwino wake ndi wambiri mʼnjira zonse! Choyambirira iwo anapatsidwa Mawu a Mulungu kuti awasunge.

3Nanga zili bwanji ngati ena analibe chikhulupiriro? Kodi kupanda chikhulupiriro kwawo kukanalepheretsa kukhulupirika kwa Mulungu? 4Ayi. Mʼnjira iliyonse ayi! Mulungu akhale woona, ndi munthu aliyense akhale wonama. Monga kwalembedwa kuti,

“Kotero kuti inu mwapezeka kuti ndinu wolungama pamene muyankhula

ndi kupambana pamene muweruza.”

5Koma ngati kuyipa mtima kwathu kuonetsa poyera kuti Mulungu ndi wolungama, ife tinganene chiyani? Kodi tinganene kuti Mulungu ndi wosalungama pamene aonetsa mkwiyo wake pa ife? (Ine ndikuyankhula monga mmene anthu ena amayankhulira). 6Ayi. Mʼnjira iliyonse ayi! Ngati zikanakhala zotero, kodi Mulungu akanaweruza bwanji dziko lapansi? 7Wina atanena kuti, “Ngati kunama kwanga kukuonetsa koposa kuti Mulungu ndi woona, ndi kuwonjezera pa ulemerero wake, nanga nʼchifukwa chiyani ndikuweruzidwa kuti ndine wochimwa?” 8Nʼchifukwa chiyani osanena kuti, monga ena amanena mosasamala kuti, “Tiyeni tichite zoyipa kuti zabwino zionekere?” Anthu onena zoterewa kulangidwa kwawo ndi koyenera.

Palibe Munthu Wolungama

9Kodi timalize bwanji? Kodi Ayuda ndife oposa anthu ena? Ayi. Mʼnjira iliyonse ayi! Ife tinanena kale kuti Ayuda ndi a mitundu ina omwe ndi ochimwa. 10Monga kwalembedwa kuti,

“Palibe munthu wolungama, inde palibe ndi mmodzi yemwe.

11Palibe ndi mmodzi yemwe amene amazindikira,

palibe amene amafunafuna Mulungu.

12Onse apatukira kumbali,

onse pamodzi asanduka opandapake.

Palibe ndi mmodzi yemwe amene amachita zabwino,

palibe ngakhale mmodzi.”

13“Kummero kwawo kuli ngati manda apululu;

ndi lilime lawo amayankhula zachinyengo.”

“Ululu wa mamba uli pa milomo yawo.”

14“Mʼkamwa mwawo ndi modzaza ndi zotemberera ndi mawu owawa.”

15“Mapazi awo afulumira kukakhetsa magazi.

16Kusakaza ndi chisoni kumaonekera mʼnjira zawo,

17ndipo njira ya mtendere sayidziwa.”

18“Saopa Mulungu ndi pangʼono pomwe.”

19Tsopano tikudziwa kuti chilichonse Malamulo amanena, amanena kwa amene amalamulidwa ndi Malamulowo, ndi cholinga chakuti aliyense asowe chonena, ndipo dziko lonse lidzayimbidwa mlandu ndi Mulungu. 20Chifukwa chake palibe mmodzi amene adzayesedwa wolungama pamaso pake chifukwa chosunga Malamulo, kuti ife timazindikira tchimo kupyolera mu Malamulo.

Kulungama Mwachikhulupiriro

21Koma tsopano chilungamo chochokera kwa Mulungu, osati chochokera ku Malamulo, chaonetsedwa. Ichi ndi chimene Malamulo ndi Aneneri amachitira umboni. 22Timakhala olungama pamaso pa Mulungu pamene takhulupirira Yesu Khristu. Mulungu amachitira zimenezi anthu onse amene akhulupirira Khristu. Palibe kusiyana pakati pa Myuda ndi a mitundu ina, 23pakuti onse anachimwa naperewera pa ulemerero wa Mulungu 24ndipo onse alungamitsidwa mwaulere mwa chisomo chake chifukwa cha Khristu Yesu amene anawawombola. 25Mulungu anamupereka Iyeyu kuti pokhetsa magazi ake, akhale nsembe yokhululukira machimo. Mulungu anachita zimenezi kufuna kuonetsa chilungamo chake. Chifukwa cha kuleza mtima kwake, sanalange anthu chifukwa cha machimo amene anachita kale. 26Iye anachita izi kuti aonetse chilungamo chake lero lino. Anthu azindikire kuti Iye ndi wolungama ndipo amalungamitsa aliyense amene akhulupirira Yesu.

27Nanga tsono pamenepa munthu anganyadenso? Kunyadatu kwachotsedwa. Chifukwa cha Malamulo? Kodi Malamulo samafuna ntchito za munthu? Ayi, koma mwachikhulupiriro. 28Ife tikunenabe kuti munthu amalungamitsidwa mwachikhulupiriro osati mwakusunga Malamulo. 29Kodi Mulungu ndi Mulungu wa Ayuda okha? Kodi si Mulungu wa a mitundu inanso? Inde wa a mitundu inanso, 30popeza ndi Mulungu mmodzi yemweyo amene adzalungamitsa mwachikhulupiriro ochita mdulidwe ndi osachita mdulidwe kudzera mʼchikhulupiriro chomwecho. 31Kodi tsono ife, tikutaya Malamulo pamene tikunena kuti pafunika chikhulupiriro? Ayi. Mʼnjira iliyonse ayi! Komatu ife tikukwaniritsadi Malamulo.