Aroma 15 – CCL & SNC

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Aroma 15:1-33

1Ife amene tili ndi chikhulupiriro champhamvu tiziwalezera mtima anthu ofowoka, ndipo tisamadzikondweretse tokha. 2Aliyense wa ife akondweretse mnzake pomuchitira zabwino zomulimbikitsa. 3Pakuti ngakhale Khristu sanadzikondweretsa yekha koma, monga kwalembedwa kuti, “Chipongwe cha anthu okunyozani chinagwera Ine.” 4Pakuti zilizonse zimene zinalembedwa kale zinalembedwa kuti zitiphunzitse ife. Malembawo amatilimbikitsa kupirira kuti tikhale ndi chiyembekezo.

5Mulungu amene amapereka kupirira ndi chilimbikitso akupatseni maganizo amodzi pakati panu monga inu mukutsatira Khristu Yesu, 6kotero kuti ndi mtima umodzi ndi movomerezana mulemekeze Mulungu ndi Atate a Ambuye athu Yesu Khristu.

7Tsopano landiranani wina ndi mnzake, monganso Khristu anakulandirani inu, ndi cholinga choti Mulungu alemekezeke. 8Chifukwa kunena zoona, Khristu wasanduka mtumiki wa Ayuda, kuonetsa kuti Mulungu ndi wokhulupirika pa malonjezo amene anachita kwa makolo awo 9kuti a mitundu ina atamande Mulungu chifukwa cha chifundo chake. Monga kwalembedwa kuti,

“Choncho ine ndidzakutamandani pakati pa a mitundu;

ndidzayimba nyimbo zotamanda dzina lanu.”

10Akutinso,

“Kondwerani inu anthu a mitundu ina pamodzi ndi anthu ake.”

11Ndipo akutinso,

“Tamandani Ambuye, inu nonse a mitundu ina,

ndi kuyimba zotamanda Iye, inu anthu onse.”

12Ndiponso Yesaya akuti,

“Muzu wa Yese udzaphuka,

wina amene adzauka kulamulira anthu a mitundu ina;

mwa Iye mudzakhala chiyembekezo cha a mitundu ina.”

13Mulungu amene amatipatsa chiyembekezo adzaze mitima yanu ndi chimwemwe ndi mtendere pamene mukumudalira Iye, kuti chiyembekezo chanu chisefukire mwamphamvu ya Mzimu Woyera.

Paulo Mtumwi wa Anthu a Mitundu Ina

14Abale anga, ine mwini ndikutsimikiza kuti inuyo ndinu abwino, odzaza ndi chidziwitso ndi okhoza kulangizana wina ndi mnzake. 15Ine ndakulemberani inu molimba mtima pa fundo zina, kukhala ngati kukukumbutsaninso za zimenezo, chifukwa cha chisomo chimene Mulungu anandipatsa ine 16kukhala mtumiki wa Khristu Yesu wa a mitundu ina ndi udindo wa wansembe, kulalikira Uthenga Wabwino wa Mulungu, kuti a mitundu ina akhale nsembe yolandiridwa kwa Mulungu, yopatsidwa ndi Mzimu Woyera.

17Choncho, ine ndikunyadira mwa Khristu Yesu potumikira Mulungu wanga. 18Ine sindidzayesera kuyankhula za kanthu kalikonse koma zimene Khristu wazichita kudzera mwa ine zotsogolera a mitundu ina kuti amvere Mulungu mwa zimene ndinanena ndi kuzichita 19mwamphamvu ya zizindikiro ndi zodabwitsa kudzera mwamphamvu ya Mzimu Woyera. Choncho kuchokera ku Yerusalemu ndi kuzungulira ku Iluriko, ine ndalalikira kwathunthu Uthenga Wabwino wa Khristu. 20Chakhala chilakolako changa nthawi zonse kuti ndilalikire Uthenga Wabwino kumene Khristu sadziwika, kuti ine ndisamange pa maziko a wina wake. 21Koma monga kwalembedwa kuti,

“Iwo amene sanawuzidwe za Iye adzaona,

ndi iwo amene sanamve adzazindikira.”

22Ichi nʼchifukwa chake ine ndakhala ndikuletsedwa kawirikawiri kubwera kwa inu.

Paulo Akonza Zopita ku Roma

23Koma tsopano popeza kulibenso malo anga woti ndigwire ntchito mʼmadera awa, ndakhala ndikufuna kukuonani kwa zaka zambiri. 24Ine ndikukonza kuti nditero pamene ndipita ku Spaniya. Ine ndikuyembekeza kudzakuchezerani pamene ndikudutsa ndi kuti inu mudzathandize popitiriza ulendo wanga, nditasangalala ndi kukhala nanu kwa kanthawi. 25Koma tsopano, ine ndili pa ulendo wopita ku Yerusalemu potumikira oyera mtima akumeneko. 26Pakuti kunakomera a ku Makedoniya ndi a ku Akaya kupereka thandizo kwa osauka pakati pa oyera mtima mu Yerusalemu. 27Iwo chinawakomera kuchita ichi, ndipo ndithu anali ndi ngongole kwa iwo. Pakuti ngati a mitundu ina anagawana ndi Ayuda madalitso auzimu, iwo ali ndi ngongole kwa Ayuda kuti agawane nawo madalitso awo a ku thupi. 28Tsono ine nditamaliza ntchito iyi ndi kutsimikiza kuti alandira chipatsochi, ndidzadzera kwanuko kudzakuchezerani pa ulendo wanga popita ku Spaniya. 29Ine ndikudziwa kuti pamene ndidzabwera kwa inu, ndidzafika ndili wodzaza ndi madalitso a Khristu.

30Abale, ine ndikukupemphani, mwa Ambuye athu Yesu Khristu ndi mwachikondi cha Mzimu, kuti mukhale nane pa kulimbika kwanga pondipempherera kwa Mulungu. 31Pempherani kuti ine ndilanditsidwe kwa osakhulupirira a ku Yudeya ndi kuti utumiki wanga mu Yerusalemu ukhale ovomerezeka ndi oyera mtima. 32Kuti mwachifuniro cha Mulungu ndibwere kwa inu ndi chimwemwe kuti ndidzapumule pamodzi ndi inu. 33Mulungu wamtendere akhale ndi inu nonse. Ameni.

Slovo na cestu

Římanům 15:1-33

Kde je opravdová víra, tam je trvalý soulad

1My vyspělejší ve víře jsme povinni snášet nedostatky těch, kdo tak pokročilí nejsou, a nesmíme být na svou úroveň domýšliví. 2Pamatujte především na bližní a na to, co prospívá jim. 3Vždyť ani Kristus nehledal svůj prospěch, ale podle prorockých slov ze žalmu snášel výsměch nepřátel: „Urážky těch, kdo tebe, Bože, tupili, snesly se na moji hlavu.“ 4I toto, jako vše v Písmu, bylo napsáno k našemu naučení, abychom získali vytrvalost a čerpali z toho povzbuzení a naději.

5Ať vám tedy Bůh, dárce toho všeho, dá žít navzájem v souladu. 6Tak si to přál Ježíš Kristus, abyste jednomyslně oslavovali Boha, jeho Otce.

Společenství mezi věřícími

7Nechtějte být nějakou uzavřenou společností. Nestraňte se jeden druhého; přijímejte se navzájem, jako nás Kristus přijal do slávy. 8Kristus byl poslán k židům, aby tak Bůh prokázal svou věrnost a splnil sliby, jež dal praotcům. 9Současně přinesl milost i všem ostatním lidem, aby také oni oslavovali Boha. Bible to potvrzuje na mnoha místech. Cituji alespoň některá:

„Velebit tě budu mezi pohany a před nevěrci budu chválit tvé jméno.“

10„Pohani, i vy se radujte společně s jeho lidem!“

11„Chvalte Boha ve všech národech,

celý svět mu vzdej chválu!“

12„Z kořene Jišajova vyroste výhonek,

početných národů stane se vládcem.

On bude nadějí pohanů,

nadějí vzdálených Bohu.“

13Ať vás Bůh, dárce naděje, naplní pokojem, radostí a důvěrou, abyste s pomocí Ducha svatého naději neztráceli, ale naopak šířili.

Odpovědnost vede Pavla k otevřenosti

14Nepochybuji o tom, moji bratři, že co do vědomostí i schopností jste sami dostatečně na výši, abyste se obešli i bez mých rad. 15Přesto jsem si v tomto dopise dovolil připomenout vám některé věci. 16K tomu mne přece Bůh povolal, abych byl služebníkem Ježíše Krista mezi všemi národy. Plním tedy tento svatý úkol, aby se všichni obrátili k Bohu a pod vedením Ducha svatého se mu cele odevzdali.

17Účast na Božím díle je mou největší chloubou. 18-19Považuji za přednost, že Kristus mým prostřednictvím probouzí víru v pohanech, mění jejich život a zázračným způsobem je přesvědčuje o své moci. Rozšířil jsem jeho poselství po celém okolí Jeruzaléma a ve všech krajích až po Illyrii. 20Zakládám si na tom, že zvěstuji Krista těm, kteří o něm dosud neslyšeli. Nechci stavět na cizích základech, 21ale řídím se slovy Písma:

„Uvidí ho ti, kdo o něm nic nevěděli,

a poznají ho ti, kdo o něm nikdy neslyšeli.“

Pavel vysvětluje plán své další cesty

22To byl tedy důvod, který mě dlouho zdržoval od cesty k vám do Říma. 23Ale nyní jsem v této oblasti svou práci dokončil. 24Už několik let se těším, že se u vás zastavím při cestě do Španělska. Doufám, že teď se mi to přání konečně splní a že se s vámi nějakou chvíli potěším, než mne zase vyprovodíte dál. 25Zatím však musím ještě podniknout cestu do Jeruzaléma, abych pomohl tamním křesťanům. 26V Makedonii a Řecku uspořádali totiž sbírku na potřebné bratry v Jeruzalémě. 27Rozhodli se tak, protože jsou Jeruzalémským zavázáni vděčností za užitek z jejich duchovního bohatství. 28Až tedy vyřídím tuto záležitost a vybrané peníze odevzdám, vypravím se do Španělska a cestou se zastavím u vás. 29Už teď cítím, že Kristus našemu setkání určitě požehná.

30Chci vás ještě poprosit, milí bratři, modlete se za mne, 31abych byl ochráněn před nepřátelstvím nevěřících v Judsku a také aby Jeruzalémští mou službu dobře přijali. 32Potom – když mi to dopřeje Bůh – s radostí přijdu k vám, abych mezi vámi trochu pookřál.

33Bůh, dárce pokoje, buď s vámi všemi.