Aroma 14 – CCL & CCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Aroma 14:1-23

Ofowoka ndi Amphamvu

1Mulandire amene ndi ofowoka mʼchikhulupiriro, osatsutsana naye pa maganizo ake. 2Chikhulupiriro cha munthu wina chimamulola kudya china chilichonse koma munthu wina, amene chikhulupiriro chake ndi chofowoka, amangodya zamasamba zokha. 3Munthu amene amadya chilichonse sayenera kunyoza amene satero, ndipo munthu amene samadya chilichonse asaweruze munthu amene amatero, pakuti Mulungu anamulandira. 4Kodi ndiwe ndani kuti uweruze wantchito wamwini? Mbuye wake yekha ndiye aweruze ngati iye wakhoza kapena walephera pa ntchito yake. Ndipo adzakhoza popeza kuti Mbuye wake angathe kumukhozetsa.

5Munthu wina amayesa tsiku limodzi lopatulika kuposa lina. Munthu wina amayesa masiku onse ofanana. Aliyense akhale otsimikiza mʼmaganizo ake. 6Iye amene amaganiza kuti tsiku limodzi ndi lopambana, amatero kwa Ambuye. Iye amene amadya nyama, amadya mwa Ambuye pakuti amayamika Mulungu. Ndipo iye amene sadya, amatero kwa Ambuye ndi kuyamika Mulungu. 7Pakuti palibe wina wa ife amene amakhala moyo pa yekha ndiponso palibe wina wa ife amene amafa pa yekha. 8Ngati ife tikhala ndi moyo, ife tikhala ndi moyo kwa Ambuye. Ndipo ngati ife tifa, tifa kwa Ambuye. Choncho, ngati tikhala ndi moyo kapena kufa, ndife ake a Ambuye.

9Pa chifukwa ichi, Khristu anafa ndi kuukanso kotero kuti Iye akhale ndi Ambuye wa akufa ndi amoyo. 10Tsono nʼchifukwa chiyani iwe ukuweruza mʼbale wako? Kapena nʼchifukwa chiyani ukumunyoza mʼbale wako? Pakuti ife tonse tidzayima pa mpando wakuweruza wa Mulungu. 11Kwalembedwa, akutero Ambuye,

“Pamene Ine ndili ndi moyo,

aliyense adzandigwadira

ndipo lilime lililonse lidzavomereza Mulungu.”

12Choncho tsopano, aliyense wa ife adzafotokoza yekha kwa Mulungu.

13Motero, tiyeni tisiye kuweruzana wina ndi mnzake. Mʼmalo mwake, tsimikizani mʼmaganizo anu kuti musayike chokhumudwitsa kapena chotchinga mʼnjira ya mʼbale wanu. 14Monga mmodzi amene ndili mwa Ambuye Yesu, ndine wotsimikiza mtima kuti palibe chakudya chimene pachokha ndi chodetsedwa. Koma ngati wina atenga china chake kukhala chodetsedwa, kwa iyeyo ndi chodetsedwa. 15Ngati mʼbale wako akuvutika chifukwa cha chimene umadya, iwe sukuchitanso mwachikondi. Usamuwononge mʼbale wako amene Khristu anamufera chifukwa cha chakudya chakocho. 16Musalole kuti chimene muchiyesa chabwino achinene ngati choyipa. 17Pakuti Ufumu wa Mulungu si nkhani yakudya ndi kumwa, koma chilungamo, mtendere ndi chimwemwe mwa Mzimu Woyera. 18Nʼchifukwa chake aliyense amene atumikira Khristu mʼnjira iyi akondweretsa Mulungu ndi kuvomerezedwa ndi anthu.

19Tsono tiyeni tiyesetse kuchita zimene zidzabweretsa mtendere ndi kulimbikitsana mwachikondi. 20Musawononge ntchito ya Mulungu chifukwa cha chakudya. Chakudya chonse ndi choyera, koma munthu amalakwa ngati adya chilichonse chimene chimakhumudwitsa wina. 21Nʼkwabwino kusadya kapena kumwa vinyo kapena kuchita chilichonse chimene chidzachititsa mʼbale wako kugwa.

22Tsono zimene ukukhulupirira pa zinthu izi zikhale pakati pa iwe ndi Mulungu. Wodala munthu amene sadzitsutsa yekha pa zimene amazivomereza. 23Koma munthu amene akukayika atsutsidwa ngati adya, chifukwa kudya kwake si kwa chikhulupiriro; ndipo chilichonse chosachokera mʼchikhulupiriro ndi tchimo.

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

罗马书 14:1-23

体恤弱者

1你们要接纳信心软弱的弟兄姊妹,不要因为看法不同便彼此批评。 2有人相信什么都可以吃,但信心软弱的人只吃素菜。 3吃的人不可轻看不吃的人,不吃的人也不可批评吃的人,因为两者都蒙上帝接纳。 4你是谁,竟然批评别人的仆人?他做得是否合宜,自然有他的主人负责。他必能做得合宜,因为主能使他做得合宜。

5有人认为这日比那日好,有人认为天天都一样,各人应该照着自己的信念拿定主意。 6守日子的人是为主而守,吃的人是为主而吃,因为他感谢上帝;不吃的人是为主不吃,他也同样感谢上帝。 7因为我们没有人为自己活,也没有人为自己死。 8我们活是为主而活,死是为主而死。因此,我们无论生死都是属主的人。 9正是为这个缘故,基督死了,又复活了,好做死人和活人的主。

10那么,你为什么论断弟兄姊妹呢?为什么轻视弟兄姊妹呢?将来我们都要一同站在上帝的审判台前。 11圣经上说:“主说,‘我凭我的永恒起誓,万膝必向我跪拜,万口必称颂上帝。’” 12这样看来,我们各人都要在上帝面前陈明自己一切的事。

不要使人犯罪

13所以,我们不可再互相论断,要留心自己的言行,不要绊倒弟兄姊妹。 14我知道并靠着主耶稣深信,没有什么是不洁净的,但若有人以为某物不洁净,那物对他来说就不洁净。 15如果你吃的东西令弟兄姊妹不安,你就不是凭爱心行事。你不可因为一点食物而损害基督舍命救赎的人。 16所以,不要让你们认为好的事被别人诟病。 17因为上帝的国不是关乎吃什么喝什么,而是关乎公义、平安和圣灵所赐的喜乐。 18以这样的态度事奉基督的人才会得到上帝的喜悦和大家的称赞。

19所以,我们要努力追求和睦,彼此造就。 20不可因食物的问题而破坏上帝的工作。所有的食物固然都是洁净的,但人若因所吃的食物绊倒别人,就有罪了。 21无论是吃肉、喝酒还是做任何别的事,如果会绊倒别人,就应该一概不做。 22你有信心认为可以做的,只要你和上帝知道就可以了。人如果在自己认为可以做的事上问心无愧,就有福了。 23人如果心里疑惑,却仍然吃,就有罪了,因为他不是凭信心吃。凡不凭信心去做的,就是犯罪。