Aroma 13 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Aroma 13:1-14

Kumvera Aulamuliro

1Aliyense ayenera kumvera akulu olamulira, chifukwa palibe ulamuliro umene sunachokere kwa Mulungu. Olamulira amene alipo anayikidwa ndi Mulungu. 2Kotero kuti, iwo amene awukira ulamuliro atsutsana ndi chimene Mulungu anakhazikitsa. Ndipo amene atero adzibweretsera okha chilango. 3Pakuti olamulira saopseza amene amachita zabwino koma amene amachita zoyipa. Kodi mukufuna kukhala osaopa olamulira? Tsono chitani zoyenera ndipo adzakuyamikirani. 4Pakuti iyeyo ndi mtumiki wa Mulungu wokuchitirani zabwino. Koma ngati muchita zoyipa muchite mantha, pakuti iye ali ndi mphamvu zolangira. Iye ndi mtumiki wa Mulungu wobweretsa mkwiyo ndi kulanga onse ochita zoyipa. 5Nʼchifukwa chake ndi koyenera kugonjera olamulira, osati chifukwa choopa kulangidwa kokha komanso chifukwa cha chikumbumtima. 6Ichi nʼchifukwa chakenso inu mumapereka msonkho. Pakuti olamulira ndi atumiki a Mulungu amene amapereka nthawi yawo yonse kulamulira. 7Mubwezereni aliyense amene munamukongola. Ngati inu muli ndi ngongole yamsonkho, perekani msonkho kwa oyenera kuwalipira. Ngati ndi kuopa perekeni kwa oyenera kuwaopa ndipo ngati ndi ulemu kwa oyenera ulemu.

Chikondi Chimakwaniritsa Malamulo

8Musakhale ndi ngongole ndi wina aliyense kupatula ngongole ya kukondana wina ndi mnzake. Pakuti amene amakonda munthu mnzake wakwaniritsa lamulo. 9Malamulo awa: “Usachite chigololo,” “Usaphe,” “Usabe,” “Usasirire,” ndi malamulo ena onse amene alipo, akhazikika pa lamulo limodzi ili, “Konda mnansi wako monga iwe mwini.” 10Chikondi sichichitira mnzake zoyipa. Chifukwa chake chikondi ndicho chokwaniritsa lamulo.

11Ndipo chitani ichi pozindikira nthawi ino. Nthawi yafika yoti inu mudzuke kutulo, chifukwa chipulumutso chathu chili pafupi tsopano kuposa pamene tinayamba kukhulupirira. 12Usiku watsala pafupifupi kutha. Kwatsala pangʼono kucha. Tiyeni tsono tichotse ntchito zamdima ndipo tivale chovala chakuwunika. 13Tiyeni tikhale moyenera monga nthawi ya masana, osati mʼmagulu amadyerero, achiwerewere ndi kuledzera, mʼmadama ndi zonyansa komanso osati mʼmagawano ndi nsanje. 14Koma valani Ambuye Yesu Khristu ndipo musaganizire za momwe mungakwaniritsire zokhumba zachikhalidwe cha uchimo.