Aroma 11 – CCL & NIVUK

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Aroma 11:1-36

Aisraeli Otsala

1Ine ndikufunsa kuti kodi Mulungu anakana anthu ake? Ayi. Ndi pangʼono pomwe! Inenso ndine Mwisraeli, mmodzi mwa zidzukulu za Abrahamu, ndiponso wa fuko la Benjamini. 2Mulungu sanawakane anthu ake amene Iye anawadziwiratu. Kodi inu simukudziwa zimene Malemba akunena pa ndime imene Eliya akudandaula kwa Mulungu kuneneza Aisraeli? Iye anati, 3“Ambuye, anthuwa apha aneneri anu ndi kugwetsa maguwa anu ansembe. Ndatsala ine ndekha wamoyo ndipo akufuna kundipha?” 4Ndipo yankho la Mulungu linali lotani? “Ine ndadzisungira ndekha anthu 7,000 amene sanapembedzepo Baala.” 5Chimodzimodzinso lero lino, alipo Aisraeli pangʼono osankhidwa mwachisomo. 6Ndipo ngati ndi mwachisomo, sikungakhalenso mwa ntchito. Ngati zikanatero, chisomo sichikanakhalanso chisomo ayi.

7Nʼchiyani tsopano? Chimene Aisraeli anachifuna ndi mtima wonse sanachipeze koma osankhidwawo anachipeza. Enawo anawumitsidwa mtima 8monga kwalembedwa kuti,

“Mulungu anawapatsa mzimu wosatha kumvetsa zinthu,

maso osatha kupenya;

makutu osatha kumva

mpaka lero lino.”

9Ndipo Davide akuti,

“Maphwando awo asanduke msampha ndi diwa lowakola

ndi chopunthwitsa kuti alandire chilango.

10Maso awo atsekedwe kuti asaone,

ndi misana yawo ikhale yokhota nthawi zonse.”

Nthambi Zomangiriridwa

11Ine ndikufunsanso kuti, kodi iwo anapunthwa ndi kugwa kotheratu? Ayi. Ndi pangʼono pomwe! Koma chifukwa cha kulakwa kwawo, chipulumutso chinafika kwa a mitundu ina kuti Aisraeli achite nsanje. 12Koma ngati kulakwa kwawo kwapindulitsa dziko lapansi ndi kulephera kwawo kwapindulitsa a mitundu ina, nanga kudzakhala kupindula kwakukulu chotani iwo akadzabwera chonse!

13Ine ndikuyankhula kwa inu a mitundu ina monga ine ndili mtumwi wa kwa a mitundu ina ndipo ndimawunyadira utumiki wangawu. 14Ine cholinga changa nʼchakuti ndichititse nsanje anthu a mtundu wanga kuti ena mwa iwo apulumutsidwe. 15Pakuti ngati kukanidwa kwawo kunayanjanitsa anthu a dziko lapansi ndi Mulungu, nanga kudzatani, Iye akadzawalandiranso? Kudzakhala monga ngati anthu akufa akuuka. 16Ngati chigawo chimodzi cha buledi woperekedwa monga zipatso zoyamba ndi choyera, ndiye kuti zonsezo ndi zoyera. Ngati muzu ndi oyera, nʼchimodzimodzinso nthambi zake.

17Ngati nthambi zina zinakhadzulidwa ndipo inu, inu ndiye nthambi za olivi wakuthengo, nʼkulumikizidwa pamalo pa nthambi zimenezo, ndipo tsopano mukulandira nawo zakudya zochokera ku mizu ya olivi, 18musadzitame kunyoza nthambi zinazo. Ngati mutero, ganizirani ichi kuti Inu simugwiriziza mizu, koma muzu ukugwiriziza inu. 19Tsono mudzati, “Nthambizo zinakhadzulidwa kuti ine ndilumikizidwepo.” 20Nʼzoona. Koma iwo anakhadzulidwa chifukwa chosakhulupirira ndipo inu mukuyima mwachikhulupiriro. Musadzitukumule, koma muchite mantha. 21Pakuti ngati Mulungu sanalekerere nthambi zachibadwidwe, Iye sadzakulekererani inunso.

22Nʼchifukwa chake ganizirani za kukoma mtima ndi za ukali wa Mulungu. Ukali uli kwa iwo amene anagwa koma kukoma mtima kwa inu, malinga ngati musamala kukoma mtima kwakeko kupanda kutero inunso mudzakhadzulidwanso. 23Ngati iwo asiya kukhala osakhulupirira, adzalumikizidwanso pakuti Mulungu akhoza kuwalumikizanso. 24Pakuti ngati inu, mwa chilengedwe munali mtengo wa olivi wa kuthengo, Mulungu anakukhadzulani nakulumikizani ku mtengo wa olivi wodzalidwa, zomwe ndi zotsutsana ndi chilengedwe, kodi sikudzakhala kwapafupi kwa Iye kuwalumikizanso mu mtengo wawowawo wa olivi?

Aisraeli Onse Adzapulumuka

25Abale, ine sindifuna kuti mukhale osadziwa za chinsinsi ichi, kuti mungadziyese nokha anzeru. Kuwuma mtima kumene Aisraeli akuchita ndi kwa kanthawi kufikira chiwerengero cha a mitundu chitalowa. 26Kotero tsono Aisraeli onse adzapulumuka, monga kwalembedwa kuti,

“Mpulumutsi adzachokera ku Ziyoni;

Iye adzachotsa zoyipa zonse za Yakobo.

27Ndipo ili lidzakhala pangano langa ndi iwo

pamene Ine ndidzachotsa machimo awo.”

28Chifukwa cha Uthenga Wabwino, Aisraeli asanduka adani a Mulungu kuti inu mupindule. Koma kunena za kusankhidwa, iwo ndi okondedwa ndi Mulungu chifukwa cha makolo awo aja. 29Pakuti Mulungu akayitana munthu ndi kumupatsa mphatso sangasinthenso. 30Monga mmene inu munalili, osamvera Mulungu pa nthawi ina, tsopano mwalandira chifundo chifukwa cha kusamvera kwawo. 31Chonchonso iwo akhala osamvera tsopano kuti iwonso alandire chifundo chifukwa cha chifundo cha Mulungu kwa inu. 32Pakuti Mulungu anasandutsa anthu onse a mʼndende ya kusamvera kuti Iye akaonetse chifundo kwa onse.

Kulemekeza Mulungu

33Aa! Nzeru za Mulungu ndi chidziwitso chake ndi zozama kwambiri!

Ndani angazindikire maweruzidwe ake,

ndipo njira zake angazitulukire ndani?

34“Kodi wadziwa ndani maganizo a Ambuye?

Kapena ndani anakhalapo mlangizi wake?”

35“Kodi ndani anapereka mphatso kwa Mulungu,

kuti Mulunguyo amubwezere iye?”

36Pakuti zinthu zonse nʼzochokera kwa Iye, nʼzolengedwa ndi Iye ndipo zimabweretsa ulemerero kwa Iye.

Kwa Iye kukhale ulemerero mpaka muyaya! Ameni.

New International Version – UK

Romans 11:1-36

The remnant of Israel

1I ask then: did God reject his people? By no means! I am an Israelite myself, a descendant of Abraham, from the tribe of Benjamin. 2God did not reject his people, whom he foreknew. Don’t you know what Scripture says in the passage about Elijah – how he appealed to God against Israel: 3‘Lord, they have killed your prophets and torn down your altars; I am the only one left, and they are trying to kill me’11:3 1 Kings 19:10,14? 4And what was God’s answer to him? ‘I have reserved for myself seven thousand who have not bowed the knee to Baal.’11:4 1 Kings 19:18 5So too, at the present time there is a remnant chosen by grace. 6And if by grace, then it cannot be based on works; if it were, grace would no longer be grace.

7What then? What the people of Israel sought so earnestly they did not obtain. The elect among them did, but the others were hardened, 8as it is written:

‘God gave them a spirit of stupor,

eyes that could not see

and ears that could not hear,

to this very day.’11:8 Deut. 29:4; Isaiah 29:10

9And David says:

‘May their table become a snare and a trap,

a stumbling-block and a retribution for them.

10May their eyes be darkened so they cannot see,

and their backs be bent for ever.’11:10 Psalm 69:22,23

Ingrafted branches

11Again I ask: did they stumble so as to fall beyond recovery? Not at all! Rather, because of their transgression, salvation has come to the Gentiles to make Israel envious. 12But if their transgression means riches for the world, and their loss means riches for the Gentiles, how much greater riches will their full inclusion bring!

13I am talking to you Gentiles. Inasmuch as I am the apostle to the Gentiles, I take pride in my ministry 14in the hope that I may somehow arouse my own people to envy and save some of them. 15For if their rejection brought reconciliation to the world, what will their acceptance be but life from the dead? 16If the part of the dough offered as firstfruits is holy, then the whole batch is holy; if the root is holy, so are the branches.

17If some of the branches have been broken off, and you, though a wild olive shoot, have been grafted in among the others and now share in the nourishing sap from the olive root, 18do not consider yourself to be superior to those other branches. If you do, consider this: you do not support the root, but the root supports you. 19You will say then, ‘Branches were broken off so that I could be grafted in.’ 20Granted. But they were broken off because of unbelief, and you stand by faith. Do not be arrogant, but tremble. 21For if God did not spare the natural branches, he will not spare you either.

22Consider therefore the kindness and sternness of God: sternness to those who fell, but kindness to you, provided that you continue in his kindness. Otherwise, you also will be cut off. 23And if they do not persist in unbelief, they will be grafted in, for God is able to graft them in again. 24After all, if you were cut out of an olive tree that is wild by nature, and contrary to nature were grafted into a cultivated olive tree, how much more readily will these, the natural branches, be grafted into their own olive tree!

All Israel will be saved

25I do not want you to be ignorant of this mystery, brothers and sisters, so that you may not be conceited: Israel has experienced a hardening in part until the full number of the Gentiles has come in, 26and in this way11:26 Or and so all Israel will be saved. As it is written:

‘The deliverer will come from Zion;

he will turn godlessness away from Jacob.

27And this is11:27 Or will be my covenant with them

when I take away their sins.’11:27 Isaiah 59:20,21; 27:9 (see Septuagint); Jer. 31:33,34

28As far as the gospel is concerned, they are enemies for your sake; but as far as election is concerned, they are loved on account of the patriarchs, 29for God’s gifts and his call are irrevocable. 30Just as you who were at one time disobedient to God have now received mercy as a result of their disobedience, 31so they too have now become disobedient in order that they too may now11:31 Some manuscripts do not have now. receive mercy as a result of God’s mercy to you. 32For God has bound everyone over to disobedience so that he may have mercy on them all.

Doxology

33Oh, the depth of the riches of the wisdom and11:33 Or riches and the wisdom and the knowledge of God!

How unsearchable his judgments,

and his paths beyond tracing out!

34‘Who has known the mind of the Lord?

Or who has been his counsellor?’11:34 Isaiah 40:13

35‘Who has ever given to God,

that God should repay them?’11:35 Job 41:11

36For from him and through him and for him are all things.

To him be the glory for ever! Amen.