Amosi 7 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Amosi 7:1-17

Dzombe, Moto ndi Chingwe Chowongolera Khoma

1Zimene Ambuye Yehova anandionetsa ndi izi: Yehova ankasonkhanitsa gulu la dzombe nthawi imene gawo la zokolola za mfumu linali litakololedwa kale ndipo mbewu zachiwiri zinali zitangoyamba kumera kumene. 2Dzombelo litadya zomera zonse za mʼdzikomo, Ine ndinafuwula kuti, “Ambuye Yehova, khululukani! Kodi Yakobo adzapulumuka bwanji? Iye ndi wofowoka kwambiri!”

3Kotero Yehova anakhululuka.

Yehovayo anati, “Izi sizidzachitika.”

4Zimene Ambuye Yehova anandionetsa ndi izi: Ambuye Yehova ankayitana malawi a moto kuti alange anthu. Motowo unawumitsa nyanja yakuya ndi kupsereza dziko. 5Tsono ine ndinafuwula kuti, “Ambuye Yehova, chonde ndikukupemphani, lekani! Kodi Yakobo adzapulumuka bwanji? Iye ndi wofowoka kwambiri!”

6Kotero Yehova anakhululuka.

Ambuye Yehova anati, “Izinso sizidzachitika.”

7Zimene Iye anandionetsa ndi izi: Ambuye anayima pambali pa khoma lomangamanga, mʼmanja mwake muli chingwe chowongolera khoma. 8Ndipo Ambuye anandifunsa kuti, “Amosi, nʼchiyani ukuonachi?”

Ine ndinayankha kuti, “Chingwe chowongolera khoma.”

Ndipo Yehova anati, “Taona, Ine ndikuyika chingwe chowongolerachi pakati pa anthu anga, Aisraeli; sindidzawalekereranso.

9“Malo achipembedzo a Isake adzawonongedwa

ndipo malo opatulika a Israeli adzasanduka bwinja;

ndidzagwetsa nyumba ya Yeroboamu ndi lupanga langa.”

Amosi ndi Amaziya

10Pamenepo Amaziya wansembe wa ku Beteli anatumiza uthenga kwa Yeroboamu mfumu ya Israeli kuti, “Amosi akukuutsirani chiwembu pakati pa Aisraeli. Dziko silingalekerere zonena zake zonsezo. 11Pakuti zimene Amosi akunena ndi izi:

“ ‘Yeroboamu adzaphedwa ndi lupanga,

ndipo Israeli adzapita ndithu ku ukapolo,

kutali ndi dziko lake.’ ”

12Ndipo Amaziya anawuza Amosi kuti, “Choka, mlosi iwe! Bwerera ku dziko la Yuda. Uzikalosera kumeneko ndipo anthu a kumeneko azikakudyetsa. 13Usanenerenso ku Beteli, chifukwa kumeneko ndi malo opatulika a mfumu ndiponso ndi malo a nyumba yachipembedzo yaufumu.”

14Amosi anayankha Amaziya kuti, “Ine sindine mneneri kapena mwana wa mneneri; koma ndine woweta ziweto, ndiponso mlimi wa nkhuyu. 15Koma Yehova ananditenga ndikuweta nkhosa ndipo anati, ‘Pita ukanenere kwa anthu anga Aisraeli.’ 16Tsono imva mawu a Yehova. Iwe ukunena kuti,

“ ‘Usanenere zotsutsa Israeli,

ndipo siya kulalikira motsutsa nyumba ya Isake.’ ”

17“Tsono zimene akunena Yehova ndi izi:

“ ‘Mkazi wako adzasanduka wachiwerewere mu mzindamu,

ndipo ana ako aamuna ndi aakazi adzaphedwa ndi lupanga.

Munda wako udzayezedwa ndi chingwe ndi kugawidwa,

ndipo iwe mwini udzafera mʼdziko la anthu osapembedza Mulungu.

Ndipo Israeli adzatengedwa ndithu kupita ku ukapolo,

kutali ndi dziko lake.’ ”