Amosi 6 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Amosi 6:1-14

Tsoka kwa Osalabadira Kanthu

1Tsoka kwa amene simukulabadira kanthu ku Ziyoni,

ndiponso kwa inu amene mukukhala mwamtendere pa Phiri la Samariya,

inu anthu otchuka ochokera ku mtundu wa anthu omveka,

kumene Aisraeli amafikako!

2Pitani ku mzinda wa Kaline mukawuyangʼane;

mukapitenso ku Hamati-raba mzinda waukulu uja,

ndipo mukatsikirenso ku Gati kwa Afilisti.

Kodi mizinda imeneyi ndi yopambana maufumu anu awiriwa?

Kodi dziko lawo ndi lalikulu kupambana lanu?

3Inu simulabadirako kuti tsiku loyipa lidzafika,

zochita zanu zimafulumizitsa ulamuliro wankhanza.

4Mumagona pa mabedi owakongoletsa ndi minyanga ya njovu,

mumagona pa mipando yanu ya wofuwofu.

Mumadya ana ankhosa onona

ndi ana angʼombe onenepa.

5Mumayimba azeze anu ndi kumangopeka

nyimbo pa zingʼwenyengʼwenye ngati Davide.

6Mumamwera vinyo mʼzipanda zodzaza

ndipo mumadzola mafuta abwino kwambiri,

koma simumva chisoni ndi kuwonongeka kwa Yosefe.

7Nʼchifukwa chake inu mudzakhala mʼgulu la anthu oyamba kupita ku ukapolo;

maphwando ndi zikondwerero zanu zidzatheratu.

Yehova Amanyansidwa ndi Kunyada kwa Israeli

8Ambuye Yehova walumbira mʼdzina lake. Yehova Mulungu Wamphamvuzonse walengeza kuti,

“Ndimanyansidwa ndi kunyada kwa Yakobo,

ndimadana ndi nyumba zake zaufumu;

Ine ndidzawupereka mzindawu

pamodzi ndi zonse zili mʼmenemo.”

9Ngati anthu khumi otsala adzabisala mʼnyumba imodzi, nawonso adzafa ndithu. 10Ndipo ngati mʼbale wake wa wina wakufayo, woyenera kusamala za maliro, adzafika kudzatulutsa mitembo mʼnyumbamo nʼkufunsa aliyense amene akubisalabe mʼnyumbamo kuti, “Kodi uli ndi wina wamoyo mʼmenemo?” Ndipo munthu wobisalayo ndi kuyankha kuti, “Ayi,” mʼbaleyo adzanena kuti, “Khala chete! Ife tisayerekeze kutchula dzina la Yehova.”

11Pakuti Yehova walamula kuti

nyumba zikuluzikulu Iye adzazigamulagamula,

ndipo nyumba zazingʼono zidzasanduka maduka okhaokha.

12Kodi akavalo amathamanga pa thanthwe?

Kodi wina amatipula ndi ngʼombe mʼnyanja?

Koma chiweruzo cholungama mwachisandutsa kukhala zinthu zakupha

ndipo chipatso cha chilungamo mwachisandutsa kukhala chowawa.

13Inu amene mukunyadira kuti munagonjetsa Lo Debara

ndipo mukunena kuti, “Kodi sitinatenge Karinaimu ndi mphamvu zathu zokha?”

14Koma Yehova Mulungu Wamphamvuzonse akulengeza kuti,

“Inu nyumba ya Israeli, ndidzakudzutsirani mtundu wina wa anthu

umene udzakuzunzani

kuchokera ku Lebo Hamati mpaka ku Chigwa cha Araba.”