Amosi 5 – CCL & NAV

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Amosi 5:1-27

Mawu Odandawulira Aisraeli

1Israeli, imva mawu awa, nyimbo ya maliro imene ndikuyimba za iweyo:

2“Namwali Israeli wagwa,

moti sadzadzukanso,

wasiyidwa mʼdziko lake lomwe,

popanda woti ndi kumudzutsa.”

3Ambuye Yehova akuti,

“Mzinda umene udzapite ku nkhondo ndi anthu 1,000 amphamvu

udzatsala ndi anthu 100 okha;

mzinda umene udzapite ku nkhondo ndi anthu 100 amphamvu

udzatsala ndi anthu khumi okha basi.”

4Zimene Yehova akunena kwa nyumba ya Israeli ndi izi:

“Mundifunefune kuti mukhale ndi moyo;

5musafunefune Beteli,

musapite ku Giligala,

musapite ku Beeriseba.

Pakuti Giligala adzatengedwa ndithu kupita ku ukapolo,

ndipo Beteli adzawonongekeratu.”

6Funani Yehova kuti mukhale ndi moyo,

mukapanda kutero Iye adzatentha nyumba ya Yosefe ngati moto;

motowo udzawononga,

ndipo sipadzakhala wina wozimitsa motowo ku Beteli.

7Inu amene mumasandutsa chiweruzo cholungama kukhala chowawa

ndi kunyoza chilungamo.

8(Iye amene analenga nyenyezi za Nsangwe ndi Akamwiniatsatana,

amene amasandutsa mdima kuti ukhale mmawa

ndi kudetsa usana kuti ukhale usiku,

amene amayitana madzi a mʼnyanja

ndi kuwathira pa dziko lapansi,

Yehova ndiye dzina lake.

9Iyeyo amabweretsa chiwonongeko modzidzimutsa pa anthu amphamvu

ndi kuwononga mizinda yotetezedwa),

10inu mumadana ndi amene amadzudzula mʼbwalo la milandu

ndi kunyoza amene amanena zoona.

11Mumapondereza munthu wosauka

ndi kumukakamiza kuti akupatseni tirigu.

Nʼchifukwa chake, ngakhale mwamanga nyumba zamiyala yosema,

inuyo simudzakhalamo.

Ngakhale mwalima minda yabwino ya mphesa,

inu simudzamwa vinyo wake.

12Pakuti Ine ndikudziwa kuchuluka kwa zolakwa zanu

ndi kukula kwa machimo anu.

Inu mumapondereza anthu olungama ndi kulandira ziphuphu

ndipo anthu osauka simuwaweruza mwachilungamo mʼmabwalo anu amilandu.

13Nʼchifukwa chake pa nthawi yotere munthu wanzeru sayankhulapo kanthu,

popeza ndi nthawi yoyipa.

14Muyike mtima wanu pa zabwino osati pa zoyipa,

kuti mukhale ndi moyo.

Mukatero Yehova Mulungu Wamphamvuzonse adzakhala nanu,

monga mmene mumanenera kuti ali nanu.

15Mudane ndi zoyipa, mukonde zabwino;

mukhazikitse chiweruzo cholungama mʼmabwalo anu amilandu.

Mwina mwake Yehova Mulungu Wamphamvuzonse adzachitira chifundo

anthu otsala a mʼbanja la Yosefe.

16Choncho izi ndi zimene Ambuye, Yehova Mulungu Wamphamvuzonse, akunena:

“Mʼmisewu monse mudzakhala kulira mofuwula,

ndi kulira chifukwa cha kuwawa kwa masautso kudzakhala paliponse.

Adzayitana alimi kuti adzalire,

ndipo anthu odziwa maliridwe anthetemya adzalira mofuwula.

17Mʼminda yonse ya mpesa mudzakhala kulira kokhakokha,

pakuti Ine ndidzadutsa pakati panu,”

akutero Yehova.

Tsiku la Yehova

18Tsoka kwa inu amene mumalakalaka

tsiku la Yehova!

Chifukwa chiyani mumalakalaka tsiku la Yehova?

Tsikulo kudzakhala mdima osati kuwala.

19Lidzakhala ngati tsiku limene munthu pothawa mkango

amakumana ndi chimbalangondo,

ngati pamene munthu walowa mʼnyumba,

natsamira dzanja lake pa khoma

ndipo njoka nʼkuluma.

20Kodi tsiku la Yehova silidzakhala mdima osati kuwala,

mdima wandiweyani, popanda powala pena paliponse?

21“Ndimadana nawo masiku anu achikondwerero ndipo ndimawanyoza;

sindikondwera nayo misonkhano yanu.

22Ngakhale mupereke nsembe zopsereza ndi nsembe zachakudya,

Ine sindidzazilandira.

Ngakhale mupereke nsembe zabwino zachiyanjano,

Ine sindidzaziyangʼana nʼkomwe.

23Musandisokose nazo nyimbo zanu!

Sindidzamvetsera kulira kwa azeze anu.

24Koma chiweruzo cholungama chiyende ngati madzi,

chilungamo ngati mtsinje wosaphwa!

25“Kodi pa zaka makumi anayi zimene munakhala mʼchipululu muja

munkandibweretsera nsembe ndi zopereka, inu nyumba ya Israeli?

26Inu mwanyamula kachisi wa mfumu yanu,

ndi nyenyezi ija Kaiwani,

mulungu wanu,

mafano amene munadzipangira.

27Nʼchifukwa chake Ine ndidzakupititsani ku ukapolo, kutali kupitirira ku Damasiko,”

akutero Yehova, amene dzina lake ndi Mulungu Wamphamvuzonse.

Ketab El Hayat

عاموس 5:1-27

مرثية ودعوة إلى التوبة

1اسْمَعُوا هَذِهِ الْمَرْثِيَّةَ الَّتِي أَرْثِيكُمْ بِها يَا بَنِي إِسْرَائِيلَ. 2قَدْ سَقَطَتْ عَذْرَاءُ إِسْرَائِيلَ وَلَنْ تَنْهَضَ بَعْدُ. صَارَتْ طَرِيحَةً عَلَى أَرْضِهَا وَلَيْسَ مَنْ يُقِيمُهَا. 3لأَنَّهُ هَكَذَا يَقُولُ الرَّبُّ: إِنَّ الْمَدِينَةَ الَّتِي قَدَّمَتْ أَلْفاً مِنْ رِجَالِهَا لِلْحَرْبِ، لَا يَبْقَى لَهَا مِنْهُمْ سِوَى مِئَةٍ. وَالَّتِي قَدَّمَتْ مِئَةً مِنْهُمْ لِلْحَرْبِ لَا يَبْقَى لِبَيْتِ إِسْرَائِيلَ مِنْهُمْ سِوَى عَشَرَةٍ.

4لأَنَّ هَذَا مَا يَقُولُهُ الرَّبُّ لِبَيْتِ إِسْرَائِيلَ: الْتَمِسُونِي فَتَحْيَوْا. 5لَا تَسْعَوْا وَرَاءَ بَيْتِ إِيلَ، وَلا تَدْخُلُوا الْجِلْجَالَ، وَلا تَعْبُرُوا إِلَى بِئْرِ سَبْعٍ، لأَنَّ أَهْلَ الْجِلْجَالِ لابُدَّ أَنْ يَتِمَّ سَبْيُهُمْ، وَبَيْتَ إِيلَ تُصْبِحُ عَدَماً. 6الْتَمِسُوا الرَّبَّ فَتَحيَوْا لِئَلّا يَنْدَلِعَ كَنَارٍ تُحْرِقُ بَيْتَ يُوسُفَ وَتَلْتَهِمُ بَيْتَ إِيلَ، وَلَيْسَ مَنْ يُطْفِئُ. 7إِنَّكُمْ تُحَوِّلُونَ الْعَدْلَ مَرَارَةً، وَتَطْرَحُونَ الْحَقَّ إِلَى الأَرْضِ.

8إِنَّهُ هُوَ الَّذِي خَلَقَ الثُّرَيَّا وَالْجَبَّارَ، وَيُحَوِّلُ دَيَاجِيرَ الظُّلْمَةِ إِلَى نَهَارٍ، وَالنَّهَارَ إِلَى لَيْلٍ، وَيَسْتَدْعِي مِيَاهَ الْبَحْرِ وَيُفِيضُهَا عَلَى وَجْهِ الأَرْضِ، الرَّبُّ اسْمُهُ. 9الَّذِي يُنْزِلُ الْخَرَابَ بِالْقَوِيِّ، فَيَعْصِفُ الدَّمَارُ بِالْحُصُونِ. 10قَدْ أَبْغَضُوا مَنْ يُنَدِّدُ بِالْجَوْرِ فِي سَاحَةِ الْقَضَاءِ، وَيَكْرَهُونَ مَنْ يَنْطِقُ بِالْحَقِّ. 11فَلأَنَّكُمْ تَطَأُونَ الْمِسْكِينَ وَتَبْتَزُّونَ مِنْهُ رِشْوَةَ قَمْحٍ حَتَّى تُشَيِّدُوا بُيُوتاً مِنْ حِجَارَةٍ مَنْحُوتَةٍ، فَإِنَّكُمْ لَنْ تَسْكُنُوا فِيهَا، وَتَغْرِسُوا كُرُوماً شَهِيَّةً وَلَكِنَّكُمْ لَنْ تَشْرَبُوا مِنْ خَمْرِهَا. 12لأَنَّنِي عَالِمٌ بِكَثْرَةِ مَعَاصِيكُمْ وَعِظَمِ خَطَايَاكُمْ، إِذْ إِنَّكُمْ تُضَايِقُونَ الْبَارَّ أَيُّهَا الْمُرْتَشُونَ الَّذِينَ تَصُدُّونَ الْمِسْكِينَ عَنْ حَقِّهِ فِي سَاحَةِ الْقَضَاءِ. 13لِهَذَا يَصْمُتُ الْعَاقِلُ فِي مِثْلِ هَذَا الزَّمَانِ الرَّدِيءِ.

14اطْلُبُوا الْخَيْرَ لَا الشَّرَّ لِتَحْيَوْا، فَيَكُونَ الرَّبُّ الإِلَهُ الْقَدِيرُ مَعَكُمْ كَمَا تَقُولُونَ. 15امْقُتُوا الشَّرَّ وَأَحِبُّوا الْخَيْرَ وَأَقِيمُوا الْعَدْلَ فِي سَاحَةِ الْقَضَاءِ، لَعَلَّ الرَّبَّ الإِلَهَ الْقَدِيرَ يَتَرَفَّقُ عَلَى بَقِيَّةِ بَيْتِ يُوسُفَ.

16لِذَلِكَ، هَذَا مَا يَقُولُهُ الرَّبُّ الإِلَهُ الْقَدِيرُ، سَيَمْلأُ النَّحِيبُ أَرْجَاءَ السَّاحَاتِ، وَيَرْتَفِعُ عَوِيلُهُمْ فِي الشَّوَارِعِ قَائِلِينَ: آهِ! آهِ! وَيَدْعُونَ الْفَلاحِينَ إِلَى الْبُكَاءِ، وَالنَّادِبَاتِ إِلَى الرِّثَاءِ، 17وَتَعْلُو الْوَلْوَلَةُ فِي جَوَانِبِ الْكُرُومِ، لأَنِّي سَأَجْتَازُ مُنْتَقِماً فِي وَسَطِكُمْ يَقُولُ الرَّبُّ.

يوم الرب

18وَيْلٌ للَّذِينَ يَتَشَوَّقُونَ لِيَوْمِ الرَّبِّ. لِمَاذَا تَطْلُبُونَ مَجِيءَ يَوْمِ الرَّبِّ؟ فَيَوْمُ الرَّبِّ هُوَ ظُلْمَةٌ لَا نُورٌ. 19فَتَكُونُونَ كَرَجُلٍ هَرَبَ مِنْ وَجْهِ أَسَدٍ فَلَقِيَهُ دُبٌّ، أَوْ كَمَنْ دَخَلَ إِلَى بَيْتٍ وَاتَّكَأَ بِيَدِهِ عَلَى حَائِطٍ فَلَدَغَتْهُ أَفْعَى. 20أَوَ لَيْسَ يَوْمُ الرَّبِّ ظُلْمَةً لَا نُوراً، وَقَتَاماً خَالِياً مِنَ الضِّيَاءِ؟

21إِنِّي أَمْقُتُ أَعْيَادَكُمْ وَأَحْتَقِرُهَا، وَلا أُسَرُّ بِاحْتِفَالاتِكُمْ. 22وَمَعَ أَنَّكُمْ تُقَرِّبُونَ لِي ذَبَائِحَ مُحْرَقَاتِكُمْ وَتَقْدِمَاتِكُمْ مِنَ الدَّقِيقِ، فَإِنِّي لَا أَقْبَلُهَا وَلا أَلْتَفِتُ إِلَى ذَبَائِحِ السَّلامِ مِنْ مُسَمَّنَاتِ مَوَاشِيكُمْ. 23أَبْعِدُوا عَنِّي جَلَبَةَ أَغَانِيكُمْ لأَنِّي لَنْ أَصْغِيَ إِلَى نَغَمَاتِ رَبَابَاتِكُمْ. 24إِنَّمَا لِيَجْرِ الْحَقُّ مُتَدَفِّقاً كَالْمِيَاهِ وَالْعَدْلُ كَنَهْرٍ سَيَّالٍ.

25هَلْ قَرَّبْتُمْ لِي ذَبَائِحَ وَتَقْدِمَاتٍ طَوَالَ أَرْبَعِينَ سَنَةً فِي الْبَرِّيَّةِ، يَا بَيْتَ إِسْرَائِيلَ؟ 26بَلْ إِنَّ الْمَلِكَ الَّذِي حَمَلْتُمْ خَيْمَتَهُ وَنَصْبَ تَمَاثِيلِهِ لَمْ يَكُنْ سِوَى نَجْمٍ صَنَعْتُمُوهُ لأَنْفُسِكُمْ وَعَبَدْتُمُوهُ كَإِلَهٍ. 27لِذَلِكَ أَسْبِيكُمْ إِلَى مَا وَرَاءَ دِمَشْقَ، يَقُولُ الرَّبُّ الَّذِي اسْمُهُ الإِلَهُ الْقَدِيرُ.