Amosi 4 – CCL & NSP

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Amosi 4:1-13

Israeli Sanabwerere kwa Mulungu

1Imvani mawu awa, inu ngʼombe zazikazi za ku Basani, okhala pa Phiri la Samariya,

inu akazi amene mumapondereza anthu osauka ndi kuzunza anthu osowa

ndi kumanena kwa amuna anu kuti, “Tipatseni zakumwa!”

2Ambuye Yehova, mwa kuyera mtima kwake walumbira kuti,

“Nthawi idzafika ndithu

pamene adzakukokani ndi ngowe,

womaliza wa inu adzakokedwa ndi mbedza.

3Mudzatulukira mʼmingʼalu ya pa khoma

aliyense payekhapayekha,

ndipo mudzatayidwa ku Harimoni,”

akutero Yehova.

4“Bwerani ku Beteli mudzachimwe;

ndi ku Giligala kuti mudzapitirize kuchimwa.

Bweretsani nsembe zanu mmawa uliwonse,

bweretsani chakhumi chanu masiku atatu aliwonse.

5Wotchani buledi wokhala ndi yisiti ngati nsembe yachiyamiko

ndi kumanyadira poyera za zopereka zanu zaufulu.

Inu Aisraeli, zinyadireni nsembezo,

pakuti izi ndi zimene mumakonda kuchita,”

akutero Ambuye Yehova.

6“Ndine amene ndinakusendetsani milomo mʼmizinda yanu yonse,

ndipo munasowa chakudya mʼmizinda yanu.

Komatu inu simunabwerere kwa Ine,”

akutero Yehova.

7“Ndinenso amene ndinamanga mvula

patangotsala miyezi itatu kuti mukolole.

Ndinagwetsa mvula pa mzinda wina,

koma pa mzinda wina ayi,

mvula inkagwa pa munda wina;

koma sinagwe pa munda wina ndipo mbewu zinawuma.

8Anthu ankayenda mzinda ndi mzinda kufuna madzi,

koma sanapeze madzi okwanira kumwa.

Komabe inu simunabwerere kwa Ine,”

akutero Yehova.

9“Nthawi zambiri ndinakantha mbewu zanu ndiponso minda ya mpesa,

ndinayikantha ndi chinsikwi ndiponso ndi chiwawu.

Dzombe linawononga mikuyu yanu ndi mitengo ya olivi.

Komabe inu simunabwerere kwa Ine,”

akutero Yehova.

10“Ine ndinabweretsa miliri pakati panu

monga ndinachitira ku Igupto.

Ndinapha anyamata anu ndi lupanga,

ndinapereka akavalo anu kwa adani.

Ndinakununkhitsani fungo la mitembo lochokera mʼmisasa yanu ya nkhondo.

Komatu inu simunabwerere kwa Ine,”

akutero Yehova.

11“Ndinawononga ena mwa inu

monga ndinawonongera Sodomu ndi Gomora.

Inu munali ngati chikuni choyaka chimene chafumulidwa pa moto.

Komabe inu simunabwerere kwa Ine,”

akutero Yehova.

12“Choncho izi ndi zimene ndidzakuchitire iwe Israeli,

chifukwa ndidzakuchitira zimenezi,

konzekera kukumana ndi Mulungu wako, iwe Israeli.”

13Iye amene amawumba mapiri,

amalenga mphepo,

ndipo amawululira munthu za mʼmaganizo ake,

Iye amene amasandutsa usana kuti ukhale mdima,

ndipo amayenda pa zitunda za dziko lapansi,

dzina lake ndi Yehova Mulungu Wamphamvuzonse.

New Serbian Translation

Књига пророка Амоса 4:1-13

Израиљ се није вратио Богу

1Чујте ову реч, о, краве васанске које сте на брду Самарије,

што тлачите сиромаха, обарате убогога

и говорите мужевима: „Донесите нам да пијемо!“

2Господ Бог се заклео светошћу својом:

„Гле, ево долазе вам дани

када ће вас извлачити кукама,

а последње од вас удицама.

3Излазиће свака од вас,

равно напред, кроз пукотине

и разбацаће вас по Армону4,3 Или: по ђубришту.

– говори Господ.

4Дођите у Ветиљ и грешите,

а у Галгалу грешите још више.

Своје жртве јутром приносите

и трећег дана своје десетке.

5Захвалнице са квасцем приносите,

објавите добровољне жртве,

разгласите их, јер вам је то по вољи,

децо Израиљева

– говори Господ Бог.

6А ја сам вам дао чисте зубе4,6 Сликовити израз за недостатак хране. у свим вашим градовима,

оскудицу хлеба у свим местима вашим,

али ви ми се нисте вратили

– говори Господ.

7Још сам вам и кишу ускратио,

а било је три месеца пред жетву.

На један град сам послао кишу,

а на други нисам.

Послао сам кишу на једну њиву да је натопи,

а она која није натапана се осушила.

8Два су се, па и три града дотетурала до једног града да пију воде.

И нису се напили

и ви ми се нисте вратили

– говори Господ.

9Ударио сам медљиком и кукољем

баште ваше и ваше винограде,

ваше смокве и винограде ваше.

Појео их је скакавац,

али ви ми се нисте вратили

– говори Господ.

10И помор сам слао међу вас

као на Египат.

Мачем сам сасекао ваше младиће

са све вашим преотетим коњима.

Дао сам да вам се до носа подиже смрад вашег табора,

али ви ми се нисте вратили

– говори Господ.

11Затирао сам неке од вас

као што је Бог опустошио Содому и Гомору,

били сте као угарак извучен из ложишта,

али ви ми се нисте вратили

– говори Господ.

12Зато ћу тако да ти урадим, о, Израиљу!

И због тога што ћу да ти урадим,

припреми се да сретнеш свога Бога, о, Израиљу!“

13Јер, ево онога што је горе начинио,

што је ветар саздао

и јавио човеку мисао своју;

који зору у таму претвара

и хода по узвишењима земље –

име му је Господ, Бог над војскама!