Amosi 2 – CCL & KJV

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Amosi 2:1-16

1Yehova akuti,

“Chifukwa anthu a ku Mowabu akunka nachimwirachimwira,

Ine sindileka kuwalanga.

Popeza anatentha mafupa a mfumu ya ku Edomu,

mpaka kuwasandutsa phulusa,

2Ine ndidzatumiza moto pa Mowabu,

umene udzanyeketsa nyumba zaufumu za ku Keriyoti.

Mowabu adzafera pakati pa nkhondo yoopsa,

mʼkati mwa mfuwu wa nkhondo ndi kuliza malipenga.

3Ndidzawononga wolamulira wake

ndi kupha akuluakulu onse amene ali pamodzi ndi iye,”

akutero Yehova.

4Yehova akuti,

“Chifukwa anthu a ku Yuda akunka nachimwirachimwira,

Ine sindileka kuwalanga.

Popeza iwo akana lamulo la Yehova

ndipo sanasunge malangizo ake,

popeza asocheretsedwa ndi milungu yabodza,

milungu imene makolo awo ankayitsatira,

5Ine ndidzatumiza moto pa Yuda,

umene udzanyeketsa nyumba zaufumu za ku Yerusalemu.”

Chilango cha Anthu a ku Israeli

6Yehova akuti,

“Chifukwa anthu a ku Israeli akunka nachimwirachimwira,

Ine sindileka kuwalanga.

Iwo amagulitsa anthu olungama ndi siliva,

ndi osauka ndi nsapato.

7Amapondereza anthu osauka

ngati akuponda fumbi,

ndipo sawaweruza mwachilungamo anthu oponderezedwa.

Abambo ndi mwana wawo amagonana ndi mtsikana mmodzi yemweyo,

ndipo potero amanyozetsa dzina langa loyera.

8Anthuwo amakagonana mʼmbali mwa guwa lililonse la nsembe

pa zovala zimene anatenga ngati chikole.

Mʼnyumba ya mulungu wawo

amamweramo vinyo amene analipiritsa anthu pa milandu.

9“Ine ndinawononga Aamori pamaso pawo,

ngakhale iwo anali anthu ataliatali ngati mikungudza

ndiponso amphamvu ngati mitengo ya thundu.

Ndinawononga zipatso zawo

ndiponso mizu yawo.

10“Ine ndinakutulutsani ku Igupto,

ndipo ndinakutsogolerani mʼchipululu kwa zaka makumi anayi,

kudzakupatsani dziko la Aamori.

11Ine ndinawutsanso ena mwa ana ako kuti akhale aneneri,

ndi ena mwa anyamata ako kuti akhale anaziri.

Kodi si choncho, inu Aisraeli?”

akutero Yehova.

12“Koma inu munawamwetsa vinyo anaziri aja,

ndipo munalamula aneneri kuti asanenere.

13“Tsono Ine ndidzakupsinjani

monga imapsinjikira ngolo imene yadzaza ndi tirigu.

14Munthu waliwiro sadzatha kuthawa,

munthu wamphamvu sadzakhalanso ndi nyonga,

wankhondo sadzapulumutsa moyo wake.

15Munthu wa uta sadzalimbika,

msilikali wothamanga kwambiri sadzapulumuka,

ndipo wokwera pa akavalo sadzapulumutsa moyo wake.

16Ngakhale asilikali olimba mtima kwambiri

adzathawa ali maliseche pa tsikulo,”

akutero Yehova.

King James Version

Amos 2:1-16

1Thus saith the LORD; For three transgressions of Moab, and for four, I will not turn away the punishment thereof; because he burned the bones of the king of Edom into lime: 2But I will send a fire upon Moab, and it shall devour the palaces of Kerioth: and Moab shall die with tumult, with shouting, and with the sound of the trumpet: 3And I will cut off the judge from the midst thereof, and will slay all the princes thereof with him, saith the LORD.

4¶ Thus saith the LORD; For three transgressions of Judah, and for four, I will not turn away the punishment thereof; because they have despised the law of the LORD, and have not kept his commandments, and their lies caused them to err, after the which their fathers have walked: 5But I will send a fire upon Judah, and it shall devour the palaces of Jerusalem.

6¶ Thus saith the LORD; For three transgressions of Israel, and for four, I will not turn away the punishment thereof; because they sold the righteous for silver, and the poor for a pair of shoes; 7That pant after the dust of the earth on the head of the poor, and turn aside the way of the meek: and a man and his father will go in unto the same maid, to profane my holy name:2.7 maid: or, young woman 8And they lay themselves down upon clothes laid to pledge by every altar, and they drink the wine of the condemned in the house of their god.2.8 the condemned: or, such as have fined, or, mulcted

9¶ Yet destroyed I the Amorite before them, whose height was like the height of the cedars, and he was strong as the oaks; yet I destroyed his fruit from above, and his roots from beneath. 10Also I brought you up from the land of Egypt, and led you forty years through the wilderness, to possess the land of the Amorite. 11And I raised up of your sons for prophets, and of your young men for Nazarites. Is it not even thus, O ye children of Israel? saith the LORD. 12But ye gave the Nazarites wine to drink; and commanded the prophets, saying, Prophesy not. 13Behold, I am pressed under you, as a cart is pressed that is full of sheaves.2.13 I am…: or, I will press your place, as a cart full of sheaves presseth 14Therefore the flight shall perish from the swift, and the strong shall not strengthen his force, neither shall the mighty deliver himself:2.14 himself: Heb. his soul, or, life 15Neither shall he stand that handleth the bow; and he that is swift of foot shall not deliver himself: neither shall he that rideth the horse deliver himself. 16And he that is courageous among the mighty shall flee away naked in that day, saith the LORD.2.16 courageous: Heb. strong of his heart