Ahebri 8 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ahebri 8:1-13

Mkulu wa Ansembe wa Pangano Latsopano

1Fundo yayikulu pa zimene tikunenazi ndi iyi: Tili naye ife Mkulu wa ansembe, amene anakhala ku dzanja lamanja la mpando waufumu wa Mulungu Waulemerero kumwamba. 2Ndipo akutumikira mʼmalo opatulika, mu Tenti yeniyeni yoyikidwa ndi Ambuye, osati ndi munthu.

3Mkulu wa ansembe aliyense amasankhidwa kuti azipereka mphatso ndi nsembe kwa Mulungu, ndipo kunali koyenera kuti wansembe wathunso akhale nʼkanthu kopereka. 4Ngati iye akanakhala pa dziko lapansi, sakanakhala wansembe pakuti alipo kale anthu amene amapereka mphatso zolembedwa mʼMalamulo. 5Iwo amatumikira pamalo opatulika amene ndi chithunzi ndi chifanizo cha zimene zili kumwamba. Ichi ndi chifukwa chake Mose anachenjezedwa pamene anali pafupi kumanga Tenti: “Uwonetsetse kuti wapanga zonse monga momwe ndikukuonetsera pa phiri pano.” 6Koma Yesu analandira utumiki wopambana kuposa wawo monga Iyenso ali Nkhoswe ya pangano lopambana kuposa lakale lija, chifukwa pangano latsopano lakhazikika pa malonjezano opambana kwambiri.

7Ngati pangano loyamba lija likanakhala langwiro, sipakanafunikanso lina mʼmalo mwake. 8Koma Mulungu anapeza zolakwika pakati pa anthu ndipo anati,

“Masiku akubwera,” akutero Yehova,

“pamene ndidzachita pangano latsopano

ndi Aisraeli

ndiponso nyumba ya Yuda.

9Silidzakhala ngati pangano

limene ndinachita ndi makolo awo,

pamene ndinawagwira padzanja

nʼkuwatulutsa ku Igupto

chifukwa iwo sanasunge pangano langa lija

ndipo Ine sindinawasamalire,

akutero Ambuye.

10Tsono ili ndi pangano ndidzapangane ndi nyumba ya Israeli:

Atapita masiku amenewa, akutero Ambuye,

Ine ndidzayika malamulo anga mʼmaganizo mwawo,

ndi kulemba mʼmitima mwawo.

Ine ndidzakhala Mulungu wawo,

ndipo iwo adzakhala anthu anga.

11Sipadzafunikanso wina kuti aphunzitse mnzake,

kapena munthu kuphunzitsa mʼbale wake, kunena kuti, udziwe Ambuye

chifukwa onse adzandidziwa,

kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu.

12Pakuti Ine ndidzawakhululukira zoyipa zawo,

ndipo sindidzakumbukiranso machimo awo.”

13Ponena kuti, pangano “latsopano” Mulungu wapanga pangano loyamba lija kukhala lotha ntchito, ndipo chilichonse chimene chayamba kutha ntchito ndi kukalamba, chili pafupi kuchokeratu.