Ahebri 7 – CCL & NIV

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ahebri 7:1-28

Za Melikizedeki Mkulu wa Ansembe

1Melikizedeki ameneyu anali mfumu ya ku Salemu, ndiponso wansembe wa Mulungu Wammwambamwamba. Anakumana ndi Abrahamu pamene ankabwerera kuchokera ku nkhondo atagonjetsa mafumu aja, Melikizedeki anakumana naye namudalitsa. 2Ndipo Abrahamu anamupatsa chakhumi cha zonse anafunkha. Choyamba dzina la Melikizedeki likutanthauza, “Mfumu ya chilungamo,” kenakanso, “Mfumu ya Salemu,” kutanthauza, “Mfumu ya mtendere.” 3Alibe abambo kapena mayi, alibe chiyambi kapena chitsiriziro cha moyo wake. Iye ali ngati Mwana wa Mulungu ndipo akupitirira kukhala wansembe wamuyaya.

4Mukuona tsono kuti munthuyo anali wamkulu ndithu, pakuti Abrahamu kholo lathu anamupatsa chakhumi cha zimene anafunkha. 5Tsono lamulo likuti, ana a Levi amene amakhala ansembe azilandira chakhumi kuchokera kwa Aisraeli, abale awo ngakhale kuti abale awowo ndi ochokera kwa Abrahamu. 6Melikizedeki sanali wochokera kwa Levi, komabe analandira chakhumi kuchokera kwa Abrahamu nadalitsa Abrahamuyo amene analandira malonjezo a Mulungu. 7Mosakayika konse, munthu amene amadalitsa ndi wamkulu kuposa amene akudalitsidwayo. 8Ansembe amene amalandira chakhumi amafa, choncho Melikizedeki ndi wamkulu kuwaposa iwo chifukwa Malemba amamuchitira umboni kuti ndi wamoyo. 9Wina angathe kunena kuti Levi, amene amalandira chakhumi, anapereka chakhumicho kudzera mwa Abrahamu, 10chifukwa pamene Melikizedeki anakumana ndi Abrahamu nʼkuti Levi ali mʼthupi la kholo lake.

Yesu Wofanana ndi Melikizedeki

11Kukanatheka kukhala wangwiro mwa unsembe wa Levi, pakuti Malamulo anapatsidwa kwa anthu mwa unsembe wa Levi, nʼchifukwa chiyani panafunikanso wansembe wina kuti abwere, wofanana ndi Melikizedeki, osati Aaroni? 12Pakuti pamene unsembe usintha, malamulonso amayenera kusintha. 13Ambuye athu Yesu, amene mawuwa akunena za Iye, anali wa fuko lina, ndipo palibe aliyense wochokera fuko lakelo amene anatumikira pa guwa lansembe. 14Pakuti nʼzodziwika bwino kuti Ambuye athu anachokera fuko la Yuda. Kunena za fuko limeneli, Mose sananenepo kanthu za ansembe. 15Ndipo zimene tanenazi zimamveka bwino ngati tiona kuti pafika wansembe wina wofanana ndi Melikizedeki. 16Yesu sanakhale wansembe chifukwa cha malamulo monga mwa mabadwidwe ake koma mwamphamvu ya moyo wosatha. 17Pakuti Mulungu anamuchitira umboni kuti,

“Iwe ndi wansembe wamuyaya,

monga mwa dongosolo la unsembe wa Melikizedeki.”

18Choncho lamulo loyamba lachotsedwa chifukwa linali lofowoka ndi lopanda phindu. 19Tsono Malamulo sangathe kusandutsa chilichonse kukhala changwiro, koma mʼmalo mwake mwalowa chiyembekezo chabwino, chimenechi timayandikira nacho kwa Mulungu.

20Izi sizinachitiketu wopanda lumbiro. Ena ankakhala ansembe popanda lumbiro. 21Koma Yesu ankakhala wansembe ndi lumbiro pamene Mulungu anati,

“Ambuye analumbira

ndipo sangasinthe maganizo ake,

‘Iwe ndi wansembe wamuyaya.’ ”

22Chifukwa cha lumbiroli, Yesu wakhala Nkhoswe ya Pangano lopambana.

23Tsono ansembe akale aja analipo ambiri, popeza imfa imawalepheretsa kupitiriza ntchitoyi. 24Koma Yesu popeza ndi wamuyaya, unsembe wake ndi wosatha. 25Chifukwa chake Iye amapulumutsa kwathunthu amene amabwera kwa Mulungu kudzera mwa Iyeyo. Iye ali ndi moyo nthawi zonse kuti adziwapempherera iwo.

26Uyu ndi Mkulu wa ansembe amene tikumufuna chifukwa ndi woyera, wopanda choyipa kapena chodetsa chilichonse, wosiyana ndi anthu ochimwa, ndiponso wokwezedwa kuposa zonse zakumwambaku. 27Kusiyana ndi akulu a ansembe ena aja, Yesu sanafunike kupereka nsembe tsiku ndi tsiku poyamba chifukwa cha machimo ake, ndipo kenaka chifukwa cha machimo a anthu ena. Iye anadzipereka nsembe chifukwa cha machimo awo kamodzi kokha pamene anadzipereka yekha. 28Pakuti lamulo limasankha anthu amene ndi ofowoka kukhala akulu a ansembe; koma lumbiro, lomwe linabwera pambuyo pa lamulo, linasankha Mwana, amene anapangidwa kukhala wangwiro kwamuyaya.

New International Version

Hebrews 7:1-28

Melchizedek the Priest

1This Melchizedek was king of Salem and priest of God Most High. He met Abraham returning from the defeat of the kings and blessed him, 2and Abraham gave him a tenth of everything. First, the name Melchizedek means “king of righteousness”; then also, “king of Salem” means “king of peace.” 3Without father or mother, without genealogy, without beginning of days or end of life, resembling the Son of God, he remains a priest forever.

4Just think how great he was: Even the patriarch Abraham gave him a tenth of the plunder! 5Now the law requires the descendants of Levi who become priests to collect a tenth from the people—that is, from their fellow Israelites—even though they also are descended from Abraham. 6This man, however, did not trace his descent from Levi, yet he collected a tenth from Abraham and blessed him who had the promises. 7And without doubt the lesser is blessed by the greater. 8In the one case, the tenth is collected by people who die; but in the other case, by him who is declared to be living. 9One might even say that Levi, who collects the tenth, paid the tenth through Abraham, 10because when Melchizedek met Abraham, Levi was still in the body of his ancestor.

Jesus Like Melchizedek

11If perfection could have been attained through the Levitical priesthood—and indeed the law given to the people established that priesthood—why was there still need for another priest to come, one in the order of Melchizedek, not in the order of Aaron? 12For when the priesthood is changed, the law must be changed also. 13He of whom these things are said belonged to a different tribe, and no one from that tribe has ever served at the altar. 14For it is clear that our Lord descended from Judah, and in regard to that tribe Moses said nothing about priests. 15And what we have said is even more clear if another priest like Melchizedek appears, 16one who has become a priest not on the basis of a regulation as to his ancestry but on the basis of the power of an indestructible life. 17For it is declared:

“You are a priest forever,

in the order of Melchizedek.”7:17 Psalm 110:4

18The former regulation is set aside because it was weak and useless 19(for the law made nothing perfect), and a better hope is introduced, by which we draw near to God.

20And it was not without an oath! Others became priests without any oath, 21but he became a priest with an oath when God said to him:

“The Lord has sworn

and will not change his mind:

‘You are a priest forever.’ ”7:21 Psalm 110:4

22Because of this oath, Jesus has become the guarantor of a better covenant.

23Now there have been many of those priests, since death prevented them from continuing in office; 24but because Jesus lives forever, he has a permanent priesthood. 25Therefore he is able to save completely7:25 Or forever those who come to God through him, because he always lives to intercede for them.

26Such a high priest truly meets our need—one who is holy, blameless, pure, set apart from sinners, exalted above the heavens. 27Unlike the other high priests, he does not need to offer sacrifices day after day, first for his own sins, and then for the sins of the people. He sacrificed for their sins once for all when he offered himself. 28For the law appoints as high priests men in all their weakness; but the oath, which came after the law, appointed the Son, who has been made perfect forever.