Ahebri 6 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ahebri 6:1-20

1Tsono tiyeni tisangoyima pa maphunziro oyambirira enieni a Khristu koma tipitirire kuti mukule msinkhu. Tisaphunzitsenso zinthu zomwe zili ngati maziko, monga za kutembenuka mtima kusiya ntchito zosapindulitsa pa moyo wosatha, za kukhulupirira Mulungu, 2za maubatizo, za kusanjika manja, za kuuka kwa akufa ndi za chiweruzo chotsiriza. 3Ndipo Mulungu akalola, tidzaterodi.

4Nʼkosatheka kuwabwezanso anthu amene nthawi ina anawunikiridwa. Iwowa analawapo mphatso yochokera kumwamba, nʼkulandira nawo Mzimu Woyera. 5Analawa kukoma kwa mawu a Mulungu ndi mphamvu za nthawi ikubwera. 6Popeza anabwerera mʼmbuyo, nʼkosatheka kuti atembenukenso mtima chifukwa akupachikanso Mwana wa Mulungu ndi kumunyozetsa poyera.

7Nthaka yolandira mvula kawirikawiri nʼkubala mbewu zopindulitsa oyilima, Mulungu amayidalitsa. 8Koma nthaka yobereka minga ndi nthula ndi yopanda phindu ndipo ili pafupi kutembereredwa. Matsiriziro ake idzatenthedwa mʼmoto.

9Okondedwa anga, ngakhale tikuyankhula zimenezi, ife tikudziwa kuti muli nazo zinthu zabwino zomwe zimabwera pamodzi ndi chipulumutso. 10Mulungu ndi wolungama, sangayiwale ntchito zanu ndi chikondi chanu chimene munamuonetsa pothandiza anthu ake monga mmene mukuchitirabe tsopano. 11Ife tikufuna kuti aliyense wa inu aonetse changu chomwechi mpaka kumapeto, kuti zichitikedi zomwe mukuyembekezera. 12Ife sitikufuna kuti inu mukhale aulesi, koma mutsatire anthu amene, pokhulupirira ndi kupirira, akulandira zimene zinalonjezedwa.

Kukhazikika kwa Malonjezo a Mulungu

13Pamene Mulungu ankamulonjeza Abrahamu, popeza panalibe wamkulu womuposa, amene akanamutchula ndikulumbira mwa Iye, analumbira mwa Iye yekha kuti, 14“Ine ndidzakudalitsa ndithu, ndipo ndidzakupatsa zidzukulu zambiri.” 15Ndipo Abrahamu atayembekezera mofatsa, analandira zimene anamulonjezazo.

16Anthu amalumbira mʼdzina la wina amene akuwaposa, ndipo lumbiro lotere limatsimikizira zomwe zayankhulidwa ndi kuthetsa mikangano yonse. 17Momwemonso Mulungu pofuna kutsimikizira anthu amene adzalandire lonjezo, kuti Iye sangasinthe maganizo, anatsimikiza lonjezo lakelo ndi lumbiro. 18Mulungu anachita zinthu ziwiri, lonjezo ndi lumbiro, zimene sizingathe kusintha ndipo Mulungu sangathe kunama. Choncho Mulungu akutilimbikitsa mtima ife amene tinathawira kwa Iye kuti tichigwiritsitse chiyembekezo chimene tinalandira. 19Chiyembekezo chimenechi tili nacho ngati nangula wa moyo wathu. Nʼchokhazikika ndi chosagwedezeka ndipo chimalowa mʼkatikati mwa malo opatulika, kuseri kwa chinsalu chotchinga. 20Yesu anatitsogolera kupita kumeneko, nalowako mʼmalo mwathu. Iye anasanduka Mkulu wa ansembe onse wamuyaya, monga mwa dongosolo la unsembe wa Melikizedeki.