Ahebri 3 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ahebri 3:1-19

Yesu ndi Wamkulu Kuposa Mose

1Nʼchifukwa chake abale oyera mtima, amenenso munayitanidwa ndi kumwamba, lingalirani za Yesu amene ndi Mtumwi ndi Mkulu wa ansembe wa chikhulupiriro chimene timavomereza. 2Iye anali wokhulupirika kwa Mulungu amene anamupatsa udindowo, monga momwe Mose anali wokhulupirika mʼnyumba yonse ya Mulungu. 3Yesu anapezeka woyenera kulandira ulemu waukulu kuposa Mose, monga momwemonso womanga nyumba amalandira ulemu waukulu kuposa nyumbayo. 4Pakuti nyumba iliyonse imamangidwa ndi munthu wina, koma amene anapanga zonse ndi Mulungu. 5Mose anali wokhulupirika monga mtumiki mʼnyumba yonse ya Mulungu, kuchitira umboni zimene zidzayankhulidwe mʼtsogolo. 6Koma Khristu ndi wokhulupirika monga mwana pa nyumba ya Mulungu. Ndipo ndife nyumba yake ngati tipitirire kulimbika mtima ndi kunyadira zomwe tikuyembekerazo.

Chenjezo pa Kusakhulupirira

7Tsono monga Mzimu Woyera akuti,

“Lero mukamva mawu ake,

8musawumitse mitima yanu

ngati munachitira pamene munawukira,

pa nthawi yoyesedwa mʼchipululu.

9Pamene makolo anu anandiputa ndi kundiyesa,

ndipo kwa zaka makumi anayi anaona zimene Ine ndinachita.

10Nʼchifukwa chake ndinawukwiyira mʼbadowo,

ndipo Ine ndinati, ‘Nthawi zonse mitima yawo imasochera,

ndipo iwo sadziwa njira zanga.’

11Kotero Ine ndinalumbira nditakwiya kuti,

‘Iwo sadzalowa mu mpumulo wanga.’ ”

12Abale samalani, kuti pasapezeke wina aliyense mwa inu wokhala ndi mtima woyipa ndi wosakhulupirira, womulekanitsa ndi Mulungu wamoyo. 13Koma muzilimbikitsana tsiku ndi tsiku, ikanalipo nthawi imene imatchedwa kuti “Lero” kuti aliyense wa inu mtima wake usawumitsidwe ndi chinyengo cha tchimo. 14Pakuti timakhala anzake a Khristu, ngati tigwiritsitsa mpaka potsiriza chitsimikizo chimene tinali nacho pachiyambi. 15Monga kunanenedwa kuti,

“Lero ngati mumva mawu ake,

musawumitse mitima yanu

ngati momwe munachitira pamene munawukira.”

16Nanga amene anamva ndi kuwukira anali ndani? Kodi si onse amene Mose anawatulutsa mu Igupto? 17Nanga amene Mulungu anawakwiyira zaka makumi anayi anali ndani? Kodi si anthu amene anachimwa, amene mitembo yawo inatsala mʼchipululu muja? 18Nanga Mulungu ankanena za ndani kuti sadzalowa mu mpumulo wake? Pajatu ankanena za anthu amene sanamvere aja. 19Tsono ife tikuona kuti sanalowe chifukwa cha kusakhulupirika kwawo.