Ahebri 2 – CCL & CCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ahebri 2:1-18

Kusamalira Chipulumutso

1Nʼchifukwa chake, ife tiyenera kusamalira kwambiri zimene tinamva, kuopa kuti pangʼono ndi pangʼono tingazitaye. 2Popeza uthenga umene unayankhulidwa kudzera mwa angelo unali okhazikika ndithu, choncho aliyense amene ananyozera ndi kusamvera analandira chilango choyenera. 3Nanga ife tidzapulumuka bwanji tikapanda kusamala chipulumutso chachikulu chotere? Ambuye ndiye anayamba kuyankhula za chipulumutsochi, kenaka amenenso anamvawo anatitsimikizira. 4Mulungu anachitiranso umboni pochita zizindikiro, zinthu zodabwitsa ndi zamphamvu zamitundumitundu ndi powapatsa mphatso za Mzimu Woyera monga mwachifuniro chake.

Yesu Wofanana ndi Abale ake

5Mulungu sanapereke kwa angelo ulamuliro wa dziko limene likubwerali, limene ife tikulinena. 6Koma palipo pena pamene wina anachitira umboni kuti,

“Kodi munthu ndani kuti muzimukumbukira,

kapena mwana wa munthu kuti muzimusamalira?

7Munamuchepetsa pangʼono kusiyana ndi angelo;

munamupatsa ulemerero ndi ulemu.

8Munamupatsa ulamuliro pa zinthu zonse.”

Poyika zinthu zonse pansi pa ulamuliro wake, Mulungu sanasiye kanthu kamene sikali mu ulamuliro wake. Koma nthawi ino sitikuona zinthu pansi pa ulamuliro wake. 9Koma tikuona Yesu, amene kwa kanthawi kochepa anamuchepetsa pangʼono kwa angelo, koma tsopano wavala ulemerero ndi ulemu chifukwa anamva zowawa za imfa, kuti mwachisomo cha Mulungu, Iye afere anthu onse.

10Mulungu amene analenga zinthu zonse ndipo zinthu zonse zilipo chifukwa cha Iye ndi mwa Iye, anachiona choyenera kubweretsa ana ake ambiri mu ulemerero. Kunali koyenera kudzera mʼnjira ya zowawa, kumusandutsa Yesu mtsogoleri wangwiro, woyenera kubweretsa chipulumutso chawo. 11Popeza iye amene ayeretsa ndi oyeresedwa onse ndi abanja limodzi. Nʼchifukwa chake Yesu sachita manyazi kuwatcha iwo abale ake. 12Iye akuti,

“Ine ndidzawuza abale anga za dzina lanu.

Ndidzakuyimbirani nyimbo zamatamando pamaso pa mpingo.”

13Ndiponso,

“Ine ndidzakhulupirira Iyeyo.”

Ndiponso Iye akuti,

“Ine ndili pano pamodzi ndi ana amene Mulungu wandipatsa.”

14Tsono popeza kuti anawo ndi anthu, okhala ndi mnofu ndi magazi, Yesu nayenso anakhala munthu ngati iwowo kuti kudzera mu imfa yake awononge Satana amene ali ndi mphamvu yodzetsa imfa. 15Pakuti ndi njira yokhayi imene Iye angamasule amene pa moyo wawo wonse anali ngati akapolo chifukwa choopa imfa. 16Pakuti tikudziwanso kuti sathandiza angelo, koma zidzukulu za Abrahamu. 17Chifukwa cha zimenezi, Iye anayenera kukhala wofanana ndi abale ake pa zonse, kuti akhale mkulu wa ansembe wachifundo ndi wokhulupirika potumikira Mulungu, kuti potero achotse machimo a anthu. 18Popeza Iye mwini anamva zowawa pamene anayesedwa, Iyeyo angathe kuthandiza amene akuyesedwanso.

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

希伯来书 2:1-18

持守真道

1因此,我们必须更加重视所听的道,以免随流漂去。 2既然借天使传下来的话正确无误,凡干犯、违背的人都受到了应有的报应, 3我们若忽略了这么大的救恩,怎能逃避惩罚呢?这救恩首先由主亲口宣讲出来,后来由听见的人向我们证实了。 4同时,上帝按自己的旨意,用神迹、奇事、各样的异能、圣灵的恩赐和他们一同做见证。

救恩的元帅

5上帝并没有把我们所谈论的未来世界交给天使掌管。 6相反,有人在圣经中做见证说:

“人算什么,你竟顾念他?

世人算什么,你竟眷顾他?

7你使他暂时比天使低微一点,

赐他荣耀和尊贵作冠冕,

派他管理你所造的一切,

8使万物降服在他脚下。”

既说叫万物都降服在人的管理之下,就没有一样例外。不过,我们到现在还没有看到万物都降服在人的管理之下, 9只看见耶稣暂时比天使低微一点,好靠着上帝的恩典为全人类亲尝死亡的滋味。祂因为经历死亡的痛苦而得到了尊贵和荣耀作冠冕。

10作为万物的归宿和根源的上帝,叫救恩的元帅耶稣经历苦难而得以纯全,以便带领许多的儿女进入荣耀,这样的安排是恰当的。 11因为使人圣洁的耶稣和那些得以圣洁的人都出自同一位父亲,所以耶稣不以称呼他们弟兄姊妹为耻。 12祂说:

“我要向众弟兄传扬你的名,

在会众中歌颂你。”

13又说:

“我要倚靠祂。”

还说:

“看啊,我和上帝赐给我的儿女都在这里。”

14因为众儿女都是血肉之躯,所以祂也同样取了血肉之躯,为要亲身经历死亡,借此摧毁掌握死亡权势的魔鬼, 15释放那些因怕死而一生做奴隶的人。 16很明显,祂要救助的不是天使,而是亚伯拉罕的后裔。 17所以祂必须在每一方面都与祂的弟兄姊妹相同,以便在事奉上帝的事上成为一位仁慈忠信的大祭司,替众人献上赎罪祭。 18祂经历过受试炼的痛苦,所以能帮助受试炼的人。