Ahebri 1 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ahebri 1:1-14

Khristu Mwana wa Mulungu Aposa Angelo

1Kale lija Mulungu ankayankhula ndi makolo athu pa nthawi zosiyanasiyana ndiponso mwa njira zosiyanasiyana kudzera mwa aneneri. 2Koma masiku otsiriza ano, Mulungu wayankhula nafe kudzera mwa Mwana wake. Mwanayu anamusankha kuti akhale mwini wa zinthu zonse, ndiponso Mulungu analenga dziko lonse kudzera mwa Iye. 3Mwanayo ndiye kuwala kwa ulemerero wa Mulungu, chithunzithunzi chenicheni cha khalidwe lake. Iyeyu amachirikiza zinthu zonse ndi mphamvu ya mawu ake. Iye atayeretsa anthu kuchoka ku machimo awo, anakhala pansi kumwamba kudzanja lamanja la Mulungu waulemerero. 4Mwanayu ndi wamkulu koposa angelo, monga momwe dzina limene analandira limaposa dzina la angelo.

5Kodi ndi kwa mngelo uti, kumene Mulungu anati,

“Iwe ndiwe mwana wanga;

Ine lero ndakhala Atate ako.”

Kapena kunenanso kuti,

“Ine ndidzakhala abambo ake;

iye adzakhala mwana wanga.”

6Pamene Mulungu amatuma Mwana wake woyamba kubadwa ku dziko lapansi anati,

“Angelo onse a Mulungu amupembedze Iye.”

7Iye ponena za angelo akuti,

“Mulungu amasandutsa angelo ake mphepo,

amasandutsa atumiki ake malawi amoto.”

8Koma za Mwana wake akuti,

“Inu Mulungu, mpando wanu waufumu udzakhala mpaka muyaya,

ndipo mudzaweruza molungama mu ufumu wanu.

9Mwakonda chilungamo ndi kudana ndi zoyipa;

Nʼchifukwa chake, Mulungu wanu wakukwezani kuposa anzanu

pokudzozani mafuta osonyeza chimwemwe.”

10Mulungu akutinso,

“Ambuye, pachiyambi Inu munayika maziko a dziko lapansi;

ndipo zakumwambako ndi ntchito za manja anu.

11Zimenezi zidzatha, koma Inu ndinu wachikhalire.

Izo zidzatha ngati zovala.

12Mudzazipindapinda ngati chofunda;

ndipo zidzasinthidwa ngati chovala.

Koma Inu simudzasintha,

ndipo zaka zanu sizidzatha.”

13Kodi ndi kwa Mngelo uti kumene Mulungu ananenapo kuti,

“Khala kudzanja langa lamanja

mpaka nditapanga adani ako

kukhale chopondapo mapazi ako.”

14Kodi angelo onse si mizimu yotumikira odzalandira chipulumutso?