Agalatiya 3 – CCL & CCBT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Agalatiya 3:1-29

Chikhulupiriro Kapena Ntchito za Lamulo

1Agalatiya opusa inu, anakulodzani ndani? Tinamuonetsa poyera pamaso panu Yesu Khristu monga wopachikidwa pa mtanda. 2Ine ndikufuna ndiphunzire kuchokera kwa inu chinthu chimodzi ichi: Kodi munalandira Mzimu pochita ntchito za lamulo, kapena pokhulupirira zimene munamva? 3Kani ndinu opusa chotere? Inu mutayamba ndi Mzimu, kodi mukufuna kutsiriza ndi ntchito zathupi? 4Kodi munavutika kwambiri pachabe, ngati kunali kwachabedi? 5Kodi Mulungu amene anakupatsani Mzimu wake ndi kuchita zodabwitsa pakati panu, amachita zimenezi chifukwa mumachita ntchito za lamulo kapena chifukwa mumakhulupirira zimene munamva? 6Nʼchimodzimodzinso Abrahamu, “Iye anakhulupirira Mulungu, ndipo Mulungu anamutenga kukhala wolungama.”

7Tsono zindikirani kuti amene akhulupirira, ndi ana a Abrahamu. 8Malemba anaonetseratu kuti Mulungu adzalungamitsa anthu a mitundu ina mwachikhulupiriro, ndipo ananeneratu Uthenga Wabwino kwa Abrahamu kuti, “Mitundu yonse ya anthu idzadalitsika kudzera mwa iwe.” 9Choncho iwo amene ali ndi chikhulupiriro ndi odalitsidwa pamodzi ndi Abrahamu, munthu wachikhulupiriro.

10Onse amene amadalira ntchito za lamulo ndi otembereredwa, pakuti zalembedwa mʼBuku la Malamulo kuti, “Ndi wotembereredwa aliyense amene sachita zonse zimene zalembedwa mʼBuku la Malamulo.” 11Chodziwikiratu nʼchakuti palibe amene amalungamitsidwa pamaso pa Mulungu ndi lamulo, chifukwa, “Wolungama adzakhala ndi moyo mwachikhulupiriro.” 12Koma chikhulupiriro si Malamulo, chifukwa Malemba akuti, “Munthu amene achita zinthu izi adzakhala ndi moyo pozichita.” 13Khristu anatiwombola ku temberero la lamulo pokhala temberero mʼmalo mwathu, pakuti analemba kuti, “Aliyense wopachikidwa pamtengo ndi wotembereredwa.” 14Iye anatiwombola ife ndi cholinga chakuti madalitso woperekedwa kwa Abrahamu abwere kwa anthu a mitundu ina kudzera mwa Khristu Yesu, kuti ndi chikhulupiriro tilandire lonjezo la Mzimu.

Lamulo ndi Lonjezo

15Abale, ndiloleni ndipereke chitsanzo cha zochitika mʼmoyo wa tsiku ndi tsiku. Pangano likakhazikitsidwa palibe amene angachotsepo kapena kuwonjezerapo, choncho ndi chimodzimodzi pa nkhani iyi. 16Malonjezo awa anaperekedwa kwa Abrahamu ndi kwa mbewu yake. Malemba sakunena kuti, “kwa mbewu zake,” kutanthauza anthu ambiri, koma, “kwa mbewu yako,” kutanthauza munthu mmodzi, amene ndi Khristu. 17Chimene ndikutanthauza ine ndi ichi: Malamulo amene anabwera patatha zaka 430, sangathetse pangano limene linakhazikitsidwa kale ndi Mulungu ndi kuliwononga lonjezolo. 18Ngati madalitso athu akudalira ntchito za lamulo ndiye kuti madalitsowo sakupatsidwa chifukwa cha lonjezo. Koma Mulungu mwachisomo chake anadalitsa Abrahamu kudzera mu lonjezo.

19Nanga tsono cholinga cha lamulo chinali chiyani? Linaperekedwa chifukwa cha zolakwa mpaka itafika mbewu imene lonjezo limanena. Malamulowo anaperekedwa ndi angelo kudzera mwa mʼkhalapakati. 20Ngakhale zili chomwecho, mʼkhalapakati sayimira mbali imodzi yokha, koma Mulungu ndi mmodzi.

21Kodi ndiye kuti lamulo limatsutsana ndi malonjezo a Mulungu? Ayi. Nʼkosatheka! Pakuti ngati tikanapatsidwa malamulo opatsa moyo ndiye kuti mwa lamulo tikanakhala olungama. 22Koma Malemba akunenetsa kuti dziko lonse lili mu ulamuliro wauchimo, kuti mwachikhulupiriro mwa Yesu Khristu, chimene chinalonjezedwa chiperekedwe kwa amene akhulupirira.

23Chikhulupiriro ichi chisanabwere, ife tinali mʼndende ya lamulo, otsekeredwa mpaka pamene chikhulupiriro chikanavumbulutsidwa. 24Choncho lamulo linayikidwa kukhala lotiyangʼanira kuti lititsogolere kwa Khristu kuti tilungamitsidwe mwachikhulupiriro. 25Tsopano pakuti chikhulupiriro chabwera, ife sitilinso mu ulamuliro wa lamulo.

Ana a Mulungu

26Nonse ndinu ana a Mulungu kudzera mʼchikhulupiriro mwa Khristu Yesu, 27pakuti nonse amene munalumikizana ndi Khristu mu ubatizo munavala Khristu. 28Palibe Myuda kapena Mgriki, kapolo kapena mfulu, mwamuna kapena mkazi, pakuti nonse ndinu amodzi mwa Khristu Yesu. 29Ngati inu muli ake a Khristu, ndiye kuti ndinu mbewu ya Abrahamu, ndi olowamʼmalo molingana ndi lonjezo.

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

加拉太書 3:1-29

行律法與信基督

1無知的加拉太人啊!誰又迷惑了你們呢?耶穌基督被釘在十字架上的事早就像一幅畫一樣展現在你們眼前了。 2我只想問,你們領受了聖靈是靠遵行律法呢,還是因為相信所聽見的福音呢? 3你們既然靠聖靈開始了基督徒的生活,現在卻想靠肉體達到純全嗎?你們就這麼無知嗎? 4你們受了許多苦,難道都是徒然的嗎?都白受了嗎? 5上帝將聖靈賜給你們又在你們中間行神蹟,是因為你們遵行律法呢,還是因為你們相信所聽到的福音呢?

6聖經上說:「亞伯拉罕信上帝,就被算為義人。」 7因此,你們要明白,那些信上帝的人才是亞伯拉罕的子孫。 8聖經早就指明,上帝要叫外族人因信而被稱為義人,祂預先將福音傳給亞伯拉罕,說:「萬國必因你而蒙福。」 9所以那些信上帝的人必和有信心的亞伯拉罕一同得到祝福。

10凡以遵行律法為本的人都在咒詛之下,因為聖經上說:「凡不遵行律法書上一切命令的人必受咒詛。」 11非常明顯,沒有人能靠遵行律法在上帝面前被稱為義人,因為聖經上說:「義人必靠信心而活。」 12律法卻不是以信心為本,而是說:「遵行的人必存活。」

13但基督替我們受了咒詛,從而救贖我們脫離了律法的咒詛,因為聖經上說:「凡掛在木頭上的人都是受咒詛的。」 14這樣,賜給亞伯拉罕的祝福可以藉著基督耶穌臨到外族人,使我們也可以藉著信得到上帝應許賜給我們的聖靈。

律法與應許

15弟兄姊妹,我舉個日常生活中的例子。世人的合約一經雙方簽訂之後,就不能作廢,也不能加添。 16上帝曾向亞伯拉罕和他的後裔賜下應許,不過這裡沒有說「後裔們」——指許多人,而是說「你的後裔」——指一個人,就是基督。 17我的意思是:四百三十年後頒佈的律法不會廢除上帝先前立下的約,以致應許落空。 18倘若我們是靠守律法去承受產業,我們就不是倚靠上帝的應許。但上帝是憑應許把產業賜給了亞伯拉罕

19那麼,為什麼會有律法呢?律法是為了使人知罪而頒佈的,等那位承受應許的後裔來到後,律法的任務就完成了。律法是通過天使交給一位中間人頒佈的。 20中間人代表雙方,但上帝則單方面賜下應許。

21這樣看來,上帝的律法和上帝的應許是否互相矛盾呢?當然不是!如果賜下的律法能帶給人生命,人就可以靠律法成為義人了。 22但聖經說萬物都在罪的權勢下,爲要使那些相信的人因爲相信耶稣基督而得到應許3·22 因爲相信耶稣基督而得到應許」或譯「因爲耶稣基督的信實而得到應許」。

23信耶穌的時代3·23 信耶穌的時代」希臘文是「信心」,下同25節。還沒有來臨以前,律法暫時監管我們。等到信耶穌之道顯明出來後,律法就不再監管我們。 24因此,律法是我們的監護人,負責引領我們歸向基督,使我們可以因信而被稱為義人。 25現在信耶穌的時代已經來臨,我們不再受律法監管。 26你們都藉著信基督耶穌而成為上帝的兒女, 27因為你們受洗歸入基督就是披戴基督3·27 披戴基督」是個隱喻,主要的意思是「像基督」,象徵有基督的生命與品格。28從此不再分猶太人和希臘人,自由人和奴隸,男人和女人,因為你們都在基督耶穌裡合而為一了。 29你們若屬於基督,就是亞伯拉罕的後裔,都是照著上帝的應許承受產業的人。