Agalatiya 2 – CCL & KJV

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Agalatiya 2:1-21

Atumwi Alandira Paulo

1Kenaka, patatha zaka khumi ndi zinayi, ndinapitanso ku Yerusalemu, nthawi iyi ndinapita ndi Barnaba. Ndinatenganso Tito kuti apite nafe. 2Ine ndinapita chifukwa Mulungu anachita kundionetsera kuti ndipite ndipo ndinakakumana ndi atsogoleri mu msonkhano mwamseri ndi kuwafotokozera Uthenga Wabwino umene ndimalalikira pakati pa anthu a mitundu ina. Ndinachita zimenezi kuti ndikhale ndi chitsimikizo kuopa kuti mwina ndinathamanga kapena ndimathamanga liwiro pachabe. 3Komatu ngakhale Tito, amene anali nane sanakakamizidwe kuti achite mdulidwe, ngakhale iyeyo anali Mgriki. 4Nkhani iyi inayambika chifukwa abale ena achinyengo amene analowerera pakati pathu kuti adzaone za ufulu umene tili nawo mwa Khristu Yesu ndikuti atisandutse akapolo. 5Ife sitinawagonjere ndi pangʼono pomwe, nʼcholinga chakuti choonadi cha Uthenga Wabwino chikhalebe ndi ife.

6Koma kunena za aja ankaoneka ngati ofunika kwambiri, chimene iwo anali sichisintha kanthu kwa ine; chifukwa Mulungu alibe tsankho, iwowo sanawonjezepo kanthu pa uthenga wanga. 7Makamaka anaona kuti ine ndinapatsidwa ntchito yolalikira Uthenga Wabwino kwa anthu a mitundu ina monga momwe Petro anapatsidwa ntchito yolalikira Uthenga Wabwino kwa Ayuda. 8Pakuti Mulungu, amene amagwira ntchito mu utumiki wa Petro monga mtumwi kwa Ayuda, amagwiranso ntchito mu utumiki wanga monga mtumiki kwa anthu a mitundu ina. 9Yakobo, Petro ndi Yohane, amene ankatengedwa ngati mizati, atazindikira chisomo chimene chinapatsidwa kwa ine, anagwirana chanza ndi ine ndi Barnaba kusonyeza chiyanjano chathu. Iwo anavomereza kuti ife tipite kwa anthu a mitundu ina ndipo iwo apite kwa Ayuda. 10Chimene iwo anapempha ndi chakuti ife tipitirize kukumbukira osauka, chinthu chimene ine ndinali okonzeka kuchichita.

Paulo Adzudzula Petro

11Petro atafika ku Antiokeya, ine ndinamudzudzula pa gulu chifukwa anapezeka wolakwa. 12Pakuti asanafike anthu otumidwa ndi Yakobo, iye ankadya pamodzi ndi anthu a mitundu ina. Koma atafika, iyeyo anachoka pakati pa anthuwo nakakhala pa yekha chifukwa ankaopa anthu a mʼgulu la mdulidwe. 13Ayuda enanso anamutsata pochita zachinyengozi, kotero kuti ngakhale Barnaba anasocheretsedwa chifukwa cha chinyengo chawocho.

14Koma nditaona kuti iwo sankachita molingana ndi choonadi cha Uthenga Wabwino, ndinawuza Petro pamaso pa anthu onse kuti, “Iwe ndiwe Myuda koma ukukhala ngati munthu wa mtundu wina, osati Myuda. Nanga nʼchifukwa chiyani ukukakamiza anthu a mitundu ina kuti akhale ngati Ayuda?

15“Ife amene ndife Ayuda mwachibadwa, osati anthu a mitundu ina ochimwa, 16tikudziwa kuti munthu salungamitsidwa pochita ntchito za lamulo koma ndi chikhulupiriro mwa Yesu Khristu. Chomwecho, ifenso tinakhulupirira Khristu Yesu kuti tilungamitsidwe mwachikhulupiriro mwa Khristu ndipo osati pochita ntchito za lamulo, chifukwa palibe amene adzalungamitsidwa pochita ntchito za lamulo.

17“Tsono ngati ife, pamene tikufuna kulungamitsidwa mwa Khristu, zikuonekeratu poyera kuti ndifenso ochimwa, kodi zikutanthauza kuti Khristu amalimbikitsa uchimo? Ayi. Nʼkosatheka! 18Ngati ine ndimanganso chimene ndinachigumula, ndikuonetsa kuti ndine wophwanya lamulo.

19“Pakuti pamene ndinayesera kutsatira lamulo, lamulolo linandionetsa kuti ndine wochimwa. Choncho ndinasiya kutsatira lamulo kuti ndikhale ndi moyo kwa Mulungu. 20Ndinapachikidwa pa mtanda pamodzi ndi Khristu, kotero kuti sindinenso amene ndili ndi moyo, koma ndi Khristu amene ali ndi moyo mwa ine. Moyo umene ndili nawo tsopano mʼthupi lino, ndi moyo mwachikhulupiriro mwa Mwana wa Mulungu, amene anandikonda nadzipereka yekha chifukwa cha ine. 21Ine sindikukankhira kumbali chisomo cha Mulungu, chifukwa ngati chilungamo chikanapezeka pochita ntchito za lamulo, ndiye kuti Khristu anafa pachabe.”

King James Version

Galatians 2:1-21

1Then fourteen years after I went up again to Jerusalem with Barnabas, and took Titus with me also. 2And I went up by revelation, and communicated unto them that gospel which I preach among the Gentiles, but privately to them which were of reputation, lest by any means I should run, or had run, in vain. 3But neither Titus, who was with me, being a Greek, was compelled to be circumcised: 4And that because of false brethren unawares brought in, who came in privily to spy out our liberty which we have in Christ Jesus, that they might bring us into bondage: 5To whom we gave place by subjection, no, not for an hour; that the truth of the gospel might continue with you. 6But of these who seemed to be somewhat, (whatsoever they were, it maketh no matter to me: God accepteth no man’s person:) for they who seemed to be somewhat in conference added nothing to me: 7But contrariwise, when they saw that the gospel of the uncircumcision was committed unto me, as the gospel of the circumcision was unto Peter; 8(For he that wrought effectually in Peter to the apostleship of the circumcision, the same was mighty in me toward the Gentiles:) 9And when James, Cephas, and John, who seemed to be pillars, perceived the grace that was given unto me, they gave to me and Barnabas the right hands of fellowship; that we should go unto the heathen, and they unto the circumcision. 10Only they would that we should remember the poor; the same which I also was forward to do. 11But when Peter was come to Antioch, I withstood him to the face, because he was to be blamed. 12For before that certain came from James, he did eat with the Gentiles: but when they were come, he withdrew and separated himself, fearing them which were of the circumcision. 13And the other Jews dissembled likewise with him; insomuch that Barnabas also was carried away with their dissimulation. 14But when I saw that they walked not uprightly according to the truth of the gospel, I said unto Peter before them all, If thou, being a Jew, livest after the manner of Gentiles, and not as do the Jews, why compellest thou the Gentiles to live as do the Jews? 15We who are Jews by nature, and not sinners of the Gentiles, 16Knowing that a man is not justified by the works of the law, but by the faith of Jesus Christ, even we have believed in Jesus Christ, that we might be justified by the faith of Christ, and not by the works of the law: for by the works of the law shall no flesh be justified. 17But if, while we seek to be justified by Christ, we ourselves also are found sinners, is therefore Christ the minister of sin? God forbid. 18For if I build again the things which I destroyed, I make myself a transgressor. 19For I through the law am dead to the law, that I might live unto God. 20I am crucified with Christ: nevertheless I live; yet not I, but Christ liveth in me: and the life which I now live in the flesh I live by the faith of the Son of God, who loved me, and gave himself for me. 21I do not frustrate the grace of God: for if righteousness come by the law, then Christ is dead in vain.