2 Timoteyo 4 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Timoteyo 4:1-22

1Pamaso pa Mulungu ndi pamaso pa Khristu Yesu, amene adzaweruza amoyo ndi akufa omwe pamene adzaonekera ndi ufumu wake, ndikukulamula kuti: 2Lalikira Mawu; khala wokonzeka pa nthawi yake, ngakhale pamene si pa nthawi yake. Konza zolakwa zawo, dzudzula ndipo limbikitsa moleza mtima kwambiri ndi malangizo osamalitsa. 3Pakuti idzafika nthawi imene anthu adzakana chiphunzitso choona. Mʼmalo mwake, chifukwa chokhumba kumva zowakomera zokha, adzasonkhanitsa aphunzitsi ambiri omawawuza zimene iwo akufuna kumva. 4Sadzafuna kumva choona koma adzafuna kumva nthano chabe. 5Koma iwe, khala tcheru nthawi zonse, pirira mʼzovuta, gwira ntchito ya mlaliki, gwira ntchito zonse za utumiki wako.

6Pakuti moyo wanga wayamba kale kuthiridwa ngati nsembe, ndipo nthawi yakwana yoti ndinyamuke ulendo wanga. 7Ndamenya nkhondo yabwino, ndatsiriza bwino mpikisano wa liwiro ndipo ndasunga chikhulupiriro. 8Tsopano mphotho yanga ikundidikira imene ndi chipewa cha chilungamo, imene Ambuye, woweruza wolungama, adzandipatsa pa tsiku lijalo, osati ine ndekha komanso onse amene akufunitsitsa kubwera kwake.

Ndemanga ya Paulo

9Uyesetse kubwera kuno msanga. 10Paja Dema anandisiya chifukwa chokonda dziko lapansi lino, ndipo anapita ku Tesalonika. Kresike anapita ku Galatiya ndipo Tito anapita ku Dalimatiya. 11Ndatsala ndi Luka yekha basi. Mutenge Marko ndipo ubwere naye kuno, chifukwa amandithandiza mu utumiki wanga. 12Ndatumiza Tukiko ku Efeso. 13Pobwera, unditengere chofunda pamwamba chimene ndinachisiya kwa Kupro ku Trowa. Unditengerenso mabuku anga, makamaka aja azikopawa.

14Alekisandro, mmisiri wa zitsulo anandichitira zoyipa kwambiri. Ambuye adzamubwezera pa zimene anachita. 15Iwenso ukhale naye tcheru chifukwa anatsutsa kwambiri uthenga wathu.

16Podziteteza koyamba pa mlandu wanga, panalibe ndi mmodzi yemwe amene anandithandiza, koma aliyense anandithawa. Mulungu awakhululukire. 17Koma Ambuye anayima nane limodzi, ndipo anandipatsa mphamvu, kuti kudzera mwa ine, uthenga ulalikidwe kwambiri, ndikuti anthu a mitundu ina amve. Ndipo ndinalanditsidwa mʼkamwa mwa mkango. 18Ambuye adzandilanditsa ku chilichonse chofuna kundichita choyipa ndipo adzandisamalira bwino mpaka kundilowetsa chonse mu ufumu wake wakumwamba. Kwa Iye kukhale ulemerero mpaka muyaya.

Mawu Otsiriza

19Pereka moni kwa Prisila ndi Akura pamodzi ndi banja lonse la Onesiforo. 20Erasto anatsalira ku Korinto. Trofimo ndinamusiya akudwala ku Mileto. 21Uyesetse kubwera kuno nthawi yozizira isanafike. Eubulo akupereka moni, ndiponso Pude, Lino, Klaudiya ndi abale onse nawonso akupereka moni.

22Ambuye akhale ndi mzimu wako. Chisomo chikhale ndi inu nonse.