2 Timoteyo 2 – CCL & CRO

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Timoteyo 2:1-26

1Tsono iwe, mwana wanga, limbika mʼchisomo chimene chili mwa Khristu Yesu. 2Ndipo zinthu zimene unamva ine ndikuziyankhula pamaso pa mboni zambiri, uziphunzitse kwa anthu odalirika amene akaphunzitsenso ena. 3Umve nane zowawa, monga msilikali wa Khristu Yesu. 4Palibe msilikali amene ali pa ntchito amagwiranso ntchito za anthu wamba, iye amafuna kukondweretsa bwana wolamulira. 5Chimodzimodzinso, munthu amene ali pa mpikisano waliwiro, salandira mphotho ya wopambana pokhapokha atatsiriza monga mwa malamulo a mpikisanowo. 6Mlimi wolimbika ndi amene amayembekezereka kukhala woyambirira kulandira gawo la zokolola. 7Lingalira zimene ndikunenazi, pakuti Ambuye adzakuzindikiritsa zonsezi.

8Kumbukira Yesu Khristu wochokera ku mtundu wa Davide kuti anauka kwa akufa. Uwu ndiye uthenga wanga wabwino 9umene ndikuwuvutikira choterewu mpaka kumangidwa ndi maunyolo ngati wakuba. Koma mawu a Mulungu sanamangidwe ndi maunyolo. 10Choncho ndikupirira chilichonse chifukwa cha osankhidwa, kuti nawonso apulumutsidwe ndi Khristu Yesu ndi kulandira ulemerero wosatha.

11Mawu oyenera kuwadalira ndi awa:

Ngati ife tinafa naye pamodzi,

tidzakhalanso moyo pamodzi naye.

12Ngati tinapirira,

tidzalamuliranso naye pamodzi.

Ngati ife timukana,

Iye adzatikananso.

13Ngati ndife osakhulupirika,

Iye adzakhalabe wokhulupirika

popeza sangathe kudzikana.

Kuthana ndi Aphunzitsi Onyenga

14Uziwakumbutsa anthu a Mulungu zinthu izi. Uwachenjeze pamaso pa Mulungu kuti asamakangane pa za mawu. Zimenezi nʼzopanda phindu ndipo zimangowononga amene akumvawo. 15Uyesetse kukhala wovomerezeka pamaso pa Mulungu monga wantchito wopanda chifukwa chochitira manyazi amene amalalikira mawu achoonadi molondola. 16Upewe nkhani zopanda pake, zosalemekeza Mulungu, chifukwa anthu oyankhula zotere amanka napotokerapotokera. 17Chiphunzitso chawo chidzafalikira ngati chilonda. Mwa anthuwa muli Humenayo ndi Fileto. 18Iwowa apatuka pa choonadi. Iwo amaphunzitsa kuti kuuka kwa akufa kunachitika kale, motero amawononga chikhulupiriro cha anthu ena. 19Komabe maziko olimba, amene Mulungu anawayika ngokhazikika, ndipo mawu olembedwapo ndi awa: “Yehova amadziwa amene ndi ake,” ndiponso, “Aliyense amene amavomereza dzina la Ambuye ayenera kusiya zoyipa.”

20Mʼnyumba yayikulu simukhala ziwiya zagolide ndi zasiliva zokha, koma mumakhalanso zamtengo ndi zadothi. Zina zimakhala za ntchito yapamwamba, zina za ntchito wamba. 21Munthu akadziyeretsa nʼkusiya ntchito za wambazi, adzakhala chiwiya cha ntchito yapamwamba, woyeretsedwa, ndi waphindu kwa Ambuye wake, wokonzeka kugwira ntchito iliyonse yabwino.

22Thawa zilakolako zoyipa zachinyamata. Funafuna chilungamo, chikhulupiriro, chikondi ndi mtendere pamodzi ndi amene akuyitanira pa dzina la Ambuye ndi mtima osadetsedwa. 23Ukane matsutsano oyipa ndi opusa, chifukwa amayambitsa mikangano. 24Ndiponso mtumiki wa Ambuye asamakangane ndi anthu, koma azikhala wachifundo kwa aliyense, wodziwa kuphunzitsa, osati wokalipakalipa. 25Otsutsana naye awalangize mofatsa, mwina Mulungu adzawapatsa mwayi woti asinthike ndi kuzindikira choonadi. 26Motero nzeru zawo zidzabweramo, ndipo adzathawa msampha wa mdierekezi, amene anawagwira ukapolo kuti azichita zofuna zake.

Knijga O Kristu

2 Timoteju 2:1-26

Dobar Kristov vojnik

1Timoteju, sinko, jačaj u milosti koju nam daje Isus Krist! 2Što si od mene čuo pred mnogim svjedocima, prenesi pouzdanim ljudima koji će to moći prenijeti drugima.

3Dijeli sa mnom tegobe kao dobar vojnik Krista Isusa. 4Kristov si vojnik; ne zapleći se u svagdanje poslove jer inače nećeš moći ugoditi vojskovođi. 5Pokoravaj se Božjim pravilima, baš kao sportaš koji ne može dobiti nagradu ako se propisno ne natječe. 6Ratar koji naporno radi treba prvi uživati u plodovima svojega truda. 7Razmisli što ti govorim. Gospodin će dati da razumiješ sve to.

8Nemoj nikad zaboraviti da je Isus Krist rođen kao potomak kralja Davida i da je uskrsnuo od mrtvih. To je Radosna vijest koju naviještam. 9Zbog nje trpim nevolju i okovan sam poput kakva zločinca. Ali ako sam ja okovan, Božja riječ nije. 10Voljan sam sve podnijeti zaradi onih koje je Bog izabrao da postignu spasenje i vječnu slavu u Kristu Isusu.

11Ove su riječi istinite:

Umremo li s njim,

s njim ćemo i živjeti.

12Podnesemo li nevolje,

kraljevat ćemo s njim.

Ako ga se odreknemo,

i on će se nas odreći.

13Ako mu ne budemo vjerni,

on će ostati vjeran

jer ne može sâm sebe zanijekati.

Djelatnik potvrđen od Boga

14Podsjećaj ljude na to i zaklinji ih pred Bogom da se ne prepiru. To ničemu ne koristi, a na propast je onima koji slušaju. 15Marljivo se trudi da se pred Bogom pokažeš prokušanim, dobrim djelatnikom koji se nema čega stidjeti i koji točno razlaže riječ istine. 16Svjetovne i isprazne rasprave izbjegavaj jer one vuku u sve veću bezbožnost. 17Takve se riječi šire poput gnjileži. Takvi su Himenej i Filet. 18Zastranili su od istine tvrdeći da se uskrsnuće već zbilo. Time su potkopali vjeru nekih.

19Ali Božja istina stoji čvrsto poput temelja s natpisom: “Gospodin poznaje svoje”2:19 Brojevi 16:5. i “Tko god tvrdi da pripada Gospodinu neka se kloni zla.”2:19 Vidjeti: Izaija 52:11.

20U bogatoj kući ima posuda načinjenih od zlata i srebra, ali i od drva i gline. Jedne se rabe u časne, druge u nečasne svrhe. 21Bude li se dakle tko čuvao čistim od toga, bit će posuda korisna Gospodaru—časna, posvećena, čista i prikladna za svako dobro djelo.

22Kloni se svega što potiče mladenačke strasti! Teži za pravednošću, vjerom, ljubavlju, mirom sa svima koji čistog srca zazivaju Gospodina.

23Kloni se nerazumnih i neobuzdanih rasprava jer znaš da one završavaju svađom. 24A sluga Gospodnji ne smije se svađati, nego prema svima mora biti blag. Treba biti sposoban poučavati i otrpjeti 25te blago prekoriti protivnike ne bi li im Bog darovao obraćenje da spoznaju istinu. 26Tada će se prenuti iz đavolske zamke grijeha u koju su bili uhvaćeni i ispunjavali njegovu volju.