2 Samueli 6 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Samueli 6:1-23

Bokosi la Chipangano Libwera ku Yerusalemu

1Davide anasonkhanitsanso pamodzi ankhondo 3,000 osankhidwa pakati pa Aisraeli. 2Iye pamodzi ndi ankhondo ake onse anapita ku Baalahi ku Yuda kukatenga Bokosi la Chipangano la Mulungu, limene limadziwika ndi Dzina lake, dzina la Yehova Wamphamvuzonse, amene amakhala pakati pa Akerubi amene ali pa Bokosi la Chipanganolo. 3Iwo anayika Bokosi la Mulungu pa ngolo yatsopano nachoka nalo ku nyumba ya Abinadabu, imene inali pa phiri. Uza ndi Ahiyo ana a Abinadabu ndiwo ankayendetsa ngolo yatsopanoyo, 4imene inanyamula Bokosi la Mulungu, ndipo Ahiyo mwana wa Abinadabu ankayenda patsogolo pake. 5Davide pamodzi ndi Aisraeli onse ankakondwerera ndi mphamvu zawo zonse pamaso pa Yehova poyimba nyimbo pogwiritsa ntchito azeze, apangwe, matambolini, maseche ndi malipenga.

6Atafika pa malo opunthira tirigu a Nakoni, Uza anatambalitsa dzanja lake kuti agwire Bokosi la Mulungu, chifukwa ngʼombe zinkafuna kugwa. 7Yehova anapsera mtima Uza chifukwa chochita chinthu chosayenera kuchitika. Choncho Mulungu anamukantha ndipo anafera pomwepo pambali pa Bokosi la Mulungulo.

8Ndipo Davide anakhumudwa chifukwa Yehova anakantha Uza ndipo mpaka lero malowo amatchedwa Perezi Uza.

9Tsiku limenelo Davide anachita mantha ndi Yehova ndipo anati, “Kodi Bokosi la Yehova lingafike bwanji kwathu?” 10Iye sanafunenso kubwera ndi Bokosi la Yehova kawo ku mzinda wake wa Davide. Mʼmalo mwake anapita nalo ku nyumba ya Obedi-Edomu Mgiti. 11Bokosi la Yehova linakhala mʼnyumba ya Obedi-Edomu Mgiti kwa miyezi itatu, ndipo Yehova anamudalitsa kwambiri iyeyo ndi banja lake lonse.

12Tsono Mfumu Davide anawuzidwa kuti, “Yehova wadalitsa nyumba ya Obedi-Edomu ndi zonse zimene ali nazo, chifukwa cha Bokosi la Mulungu.” Choncho Davide anapita kukatenga Bokosi la Mulungu ku nyumba ya Obedi-Edomu ndi kupita nalo ku mzinda wa Davide akukondwera kwambiri. 13Anthu amene ananyamula Bokosi la Yehova ankati akayenda mapazi asanu ndi limodzi, iye ankapereka nsembe ngʼombe yayimuna ndi mwana wangʼombe wonenepa. 14Davide ankavina ndi mphamvu zake zonse pamaso pa Yehova atavala efodi ya nsalu yofewa yosalala, 15pamene iyeyo pamodzi ndi Aisraeli onse ankabwera ndi Bokosi la Yehova, akufuwula ndi kuyimba malipenga.

16Bokosi la Yehova likulowa mu Mzinda wa Davide, Mikala mwana wamkazi wa Sauli ankaona ali pa zenera. Ndipo ataona Mfumu Davide ikulumpha ndi kuvina pamaso pa Yehova, ankamunyogodola mu mtima mwake.

17Iwo anabwera nalo Bokosi la Yehova ndipo analiyika pamalo pake mʼkati mwa tenti imene Davide anayimika ndipo Davideyo anapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano pamaso pa Yehova. 18Atatsiriza kupereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano, iye anadalitsa anthu mʼdzina la Yehova Wamphamvuzonse. 19Kenaka iye anagawira Aisraeli onsewo, aamuna ndi aakazi, aliyense buledi mmodzi, nthuli yanyama, ndiponso keke yamphesa zowuma. Ndipo anthu onse anachokapo, napita aliyense ku nyumba kwake.

20Davide atabwerera ku nyumba kwake kukadalitsa banja lake, Mikala mwana wamkazi wa Sauli anatuluka kudzakumana naye ndipo anati, “Kodi mfumu ya Israeli ingatero kudzilemekeza kwake lero, kudzithyolathyola pamaso pa akapolo aakazi, antchito ake ngati munthu wamba.”

21Davide anamuyankha Mikala kuti, “Ndachita zimenezi molemekeza Yehova, amene anandisankha ine kupambana abambo ako, kapenanso kupambana banja la abambo ako. Ndipo anandisankha kuti ndikhale wolamulira Aisraeli, anthu a Yehova. Nʼchifukwa chake ndidzasangalalabe pamaso pa Yehova. 22Ineyo ndidzadzinyoza kuposa apa, ndipo ndidzakhala wonyozeka mʼmaso mwako. Koma pakati pa akapolo aakazi awa amene umanena za iwo, ndidzalemekezedwa.”

23Ndipo Mikala mwana wa Sauli sanakhalenso ndi mwana mpaka anamwalira.