2 Samueli 5 – CCL & CCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Samueli 5:1-25

Davide Adzozedwa Kukhala Mfumu ya Israeli

1Mafuko onse a Israeli anabwera kwa Davide ku Hebroni ndipo anati, “Ife ndife mafupa ndi mnofu wanu. 2Kale lija, pamene Sauli anali mfumu yathu, inu ndinu amene munkatsogolera Aisraeli pa nkhondo zawo. Ndipo Yehova anakuwuzani kuti, ‘Udzaweta anthu anga Aisraeli, ndipo udzakhala mfumu yawo.’ ”

3Akuluakulu onse a Israeli atafika kwa Mfumu Davide ku Hebroni, mfumu inachita nawo pangano ku Hebroni pamaso pa Yehova, ndipo anamudzoza Davide kukhala mfumu ya Israeli.

4Davide anali ndi zaka makumi atatu pamene anakhala mfumu, ndipo analamulira zaka makumi anayi. 5Analamulira Yuda ali ku Hebroni kwa zaka zisanu ndi ziwiri ndi miyezi isanu ndi umodzi, ndipo ali ku Yerusalemu analamulira Israeli yense ndi Yuda kwa zaka 33.

Davide Alanda Mzinda wa Yerusalemu

6Mfumu ndi ankhondo ake anapita ku Yerusalemu kukathira nkhondo Ayebusi amene ankakhala kumeneko. Ayebusiwo anamuwuza Davide kuti, “Inu simulowa muno. Ngakhale osaona ndi olumala akhoza kukuthamangitsani.” Iwo ankaganiza kuti, “Davide sangathe kulowa momwemo.” 7Komabe Davide analanda linga la Ziyoni, limene ndi mzinda wa Davide.

8Pa tsiku limenelo Davide anati, “Aliyense wogonjetsa Ayebusi ayenera kudzera mʼngalande ya madzi kuti akafike kwa iwo amene ndi ‘olumala ndi osaona,’ amene ndi adani a Davide.” Nʼchifukwa chake amanena kuti, “Olumala ndi osaona sadzalowa mʼnyumba yaufumu.”

9Tsono Davide anakhazikika mu lingamo ndipo mzindawu anawutcha, Mzinda wa Davide. Iye anamanga malo onse ozungulira kuyambira ku matsitso ozungulira khoma. 10Ndipo mphamvu za Davide zinkakulirakulira chifukwa anali ndi Yehova Mulungu Wamphamvuzonse.

11Tsono Hiramu mfumu ya Turo inatumiza amithenga ake kwa Davide, pamodzi ndi mitengo ya mkungudza ndi amisiri a matabwa ndi amisiri a miyala, ndipo anamumangira Davide nyumba yaufumu. 12Choncho Davide anazindikira kuti Yehova wamukhazikitsa kukhala mfumu ya Israeli ndipo wakuza ufumu wake chifukwa cha anthu ake, Aisraeli.

13Davide atafika ku Yerusalemu kuchokera ku Hebroni, anakwatira azikazi natenganso akazi ena kumeneko, ndipo anabereka ana aamuna ndi aakazi ambiri. 14Mayina a ana amene anabereka ku Yerusalemu ndi awa: Samua, Sobabu, Natani, Solomoni, 15Ibihari, Elisua, Nefegi, Yafiya, 16Elisama, Eliada ndi Elifeleti.

Davide Agonjetsa Afilisti

17Afilisti atamva kuti Davide wadzozedwa kukhala mfumu ya Israeli, iwo anapita mwamphamvu kukamusakasaka. Koma Davide atamva zimenezi anakalowa mu linga. 18Ndipo Afilisti anabwera ndi kukhala momwazika mʼChigwa cha Refaimu. 19Davide anafunsa Yehova kuti, “Kodi ndipite kukathira nkhondo Afilisti? Kodi mukawapereka mʼmanja mwanga?”

Yehova anamuyankha kuti, “Pita, Ine ndidzawapereka ndithu mʼmanja mwako.”

20Choncho Davide anapita ku Baala-Perazimu ndi kugonjetsa Afilistiwo. Iye anati, “Monga amasefukira madzi, Yehova waphwanya adani anga ine ndikuona.” Choncho anawatcha malowa Baala Perazimu. 21Afilisti anasiya mafano awo kumeneko ndipo Davide ndi ankhondo ake anawatenga.

22Nthawi inanso Afilisti anabweranso namwazikana mʼChigwa cha Refaimu; 23Davide anafunsa Yehova ndipo Yehovayo anayankha kuti, “Usapite molunjika koma uzungulire kumbuyo kwawo ndipo ukawathire nkhondo patsogolo pa mitengo ya mkandankhuku. 24Mukakangomva phokoso pa msonga za mitengo ya mkandankhuku, mukayende mofulumira, chifukwa izi zikasonyeza kuti Yehova ali patsogolo panu kukantha ankhondo a Afilisti.” 25Kotero Davide anachita zimene Yehova anamulamulira ndipo anakantha Afilisti njira yonse kuchokera ku Geba mpaka ku Gezeri.

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

撒母耳记下 5:1-25

大卫统治全以色列

1以色列各支派都来希伯仑大卫,对他说:“我们是你的骨肉同胞。 2从前扫罗做王的时候,率领以色列人出征打仗的是你,耶和华也曾应许让你做祂以色列子民的牧者和首领。” 3以色列的长老都到希伯仑大卫王,大卫与他们在耶和华面前立约,他们膏立大卫以色列的王。 4大卫三十岁登基,执政共四十年。 5他在希伯仑统治犹大七年半,在耶路撒冷统治以色列犹大三十三年。

6大卫率领军队来到耶路撒冷,要攻打那里的耶布斯人。耶布斯人对大卫说:“你攻不进来,就连我们这里的瞎子、瘸子都可以把你赶走。”他们以为大卫攻不进去。 7结果大卫的军队攻取了锡安的堡垒,即后来的大卫城。 8那天,大卫下令军队从地下水道爬进城去,攻打那些“瞎子、瘸子”,他憎恶这些耶布斯人。后来便有一句俗语:“瞎子、瘸子不得进殿!” 9大卫住在锡安的堡垒里,并称之为大卫城,他又从米罗兴建环城围墙。 10大卫日渐强盛,因为万军之上帝耶和华与他同在。

11泰尔希兰差遣使者带着香柏木、木匠和石匠去为大卫建造宫殿。 12那时,大卫知道耶和华已立他做以色列王,并因祂以色列子民的缘故而使他国家兴旺。

13大卫希伯仑迁到耶路撒冷以后,又选立妃嫔,生了更多的儿女。 14以下是他在耶路撒冷生的儿子:沙姆亚朔罢拿单所罗门15益辖以利书亚尼斐雅非亚16以利沙玛以利雅大以利法列

大卫战胜非利士人

17非利士人听说大卫已被膏立为以色列王,就全军出动,要搜寻大卫大卫得到消息便退到坚城里。 18非利士人大军压境,散布在利乏音谷。 19大卫求问耶和华:“我可以去迎战非利士人吗?你会把他们交在我手里吗?”耶和华说:“去吧,我必把他们交在你手里。” 20大卫前往巴力·毗拉心,在那里打败了敌人。他说:“耶和华像洪水决堤一样为我冲垮了仇敌。”于是他称那地方为巴力·毗拉心5:20 巴力·毗拉心”意思是“冲垮之主”。21大卫和他的军队带走了非利士人所丢弃的神像。

22后来非利士人又卷土重来,散布在利乏音谷。 23大卫又求问耶和华,耶和华说:“你不要正面出击,要绕到他们后面,从桑林对面攻打他们。 24当你听见桑树梢上响起脚步声时,就要快速进攻,因为那表示耶和华已在你前头去攻击非利士的军队了。” 25大卫遵命而行,打败非利士人,由迦巴一直杀到基色