2 Samueli 22 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Samueli 22:1-51

Nyimbo ya Mayamiko ya Davide

1Davide anayimbira Yehova nyimbo iyi pamene Yehovayo anamupulumutsa mʼdzanja la adani ake onse ndiponso mʼdzanja la Sauli. 2Iye anati,

“Yehova ndiye thanthwe langa, chitetezo changa ndi mpulumutsi wanga.

3Mulungu wanga ndiye thanthwe langa, mʼmene ndimathawiramo,

chishango changa ndi ndodo yachipulumutso changa.

Iye ndi linga langa, pothawirapo panga ndi mpulumutsi wanga.

Munandipulumutsa mʼmanja mwa anthu ankhanza.

4“Ndimayitana Yehova amene ndi woyenera matamando,

ndipo ndapulumutsidwa kwa adani anga.

5“Mafunde a imfa anandizinga;

mitsinje yothamanga yachiwonongeko inandiopsa kwambiri.

6Anandimanga ndi zingwe za ku manda;

misampha ya imfa inalimbana nane.

7“Mʼmasautso anga ndinapemphera kwa Yehova;

ndinapemphera kwa Mulungu wanga.

Iye ali mʼnyumba yake, anamva mawu anga;

kulira kwanga kunafika mʼmakutu ake.

8“Dziko lapansi linanjenjemera ndi kuchita chivomerezi,

maziko a miyamba anagwedezeka;

ananjenjemera chifukwa Iye anakwiya.

9Mʼmphuno mwake munatuluka utsi;

moto wonyeketsa unatuluka mʼkamwa mwake,

makala amoto anali lawilawi mʼkamwa mwake.

10Iye anangʼamba thambo natsika pansi;

pansi pa mapazi ake panali mitambo yakuda.

11Iye anakwera pa Kerubi ndi kuwuluka;

nawuluka ndi mphepo mwaliwiro.

12Iye anapanga mdima kukhala chofunda chake,

mitambo yakuda ya mlengalenga.

13Mʼkuwala kumene kunali pamaso pake

munkachokera makala amoto alawilawi.

14Yehova anabangula kumwamba ngati bingu,

mawu a Wammwambamwamba anamveka ponseponse.

15Iye anaponya mivi yake, nabalalitsa adani ake,

ndi zingʼaningʼani zake anawagonjetsa.

16Zigwa za mʼnyanja zinaonekera poyera,

ndipo maziko a dziko lapansi anakhala poyera,

Yehova atabangula mwaukali,

pamene mpweya wamphamvu unatuluka mʼmphuno mwake.

17“Ali kumwamba, Iye anatambalitsa dzanja lake ndipo anandigwira;

anandivuwula mʼmadzi ozama.

18Anandipulumutsa kwa mdani wanga wamphamvu,

adani anga amene anali amphamvu kuposa ine.

19Adaniwo analimbana nane pamene ndinali pa mavuto,

koma Yehova anali thandizo langa.

20Iye anandipititsa kumalo otakasuka;

anandipulumutsa chifukwa amakondwera nane.

21“Yehova wandithandiza molingana ndi chilungamo changa;

molingana ndi makhalidwe anga abwino, Iye wandipulumutsa.

22Pakuti ine ndinatsata njira za Yehova;

ndilibe mlandu wochoka pamaso pa Mulungu wanga.

23Malamulo ake onse ali pamaso panga,

sindinasiye malangizo ake.

24Ndakhala moyo wosalakwa pamaso pake

ndipo ndakhala ndi kupewa tchimo.

25Yehova wandipatsa mphotho molingana ndi chilungamo changa,

molingana ndi makhalidwe anga abwino pamaso pake.

26“Kwa wokhulupirika, Inu mumaonetsa kukhulupirika kwanu,

kwa anthu amakhalidwe abwino, Inu mumaonetsanso makhalidwe abwino,

27Kwa woyera mtima, Inu mumaonetsa kuyera mtima kwanu,

koma kwa anthu achinyengo mumaonetsanso kunyansidwa nawo.

28Inu mumapulumutsa anthu odzichepetsa,

koma maso anu amatsutsana ndi odzikuza ndipo mumawatsitsa.

29Inu Yehova, ndinu nyale yanga;

Yehova wasandutsa mdima wanga kukhala kuwunika.

30Ndi thandizo lanu nditha kulimbana ndi gulu la ankhondo,

ndi Mulungu wanga nditha kuchita zosatheka ndi munthu.

31“Kunena za Mulungu, zochita zake ndi zangwiro;

mawu a Yehova alibe cholakwika.

Iye ndi chishango

kwa onse amene amathawira kwa iye.

32Mulungu wina ndi uti wofanana nanu Yehova?

Ndipo ndani amene ndi Thanthwe kupatula Mulungu wathu?

33Ndi Mulungu amene anandipatsa mphamvu

ndi kulungamitsa njira yanga.

34Iye amasandutsa mapazi anga kukhala ngati ambawala yayikazi;

Iye amandithandiza kuyimirira pamwamba pa mapiri.

35Iye amaphunzitsa manja anga kuchita nkhondo;

manja anga amatha kuthyola uta wachitsulo.

36Inu mundipatsa ine chishango chanu cha chigonjetso;

mumawerama kuti mundikweze.

37Inu mwalimbitsa njira yanga kuti ndiyende bwino,

kuti mapazi anga asaterereke.

38“Ine ndinathamangitsa adani anga ndi kuwakantha;

sindinabwerere mpaka iwo atawonongedwa.

39Ndinawakantha kotheratu, ndipo sanathe kudzukanso;

Iwo anagwera pansi pa mapazi anga.

40Inu munandipatsa ine mphamvu yochitira nkhondo;

munagwaditsa adani anga pa mapazi anga.

41Inu muchititsa kuti adani anga atembenuke ndi kuthawa;

ndipo ndinawononga adani anga.

42Iwo anafuwula kupempha thandizo, koma panalibe ndi mmodzi yemwe owapulumutsa.

Analirira kwa Yehova, koma sanawayankhe.

43Ine ndinawaperesa ngati fumbi la pa dziko lapansi;

ndinawasinja ndipo ndinawapondaponda ngati matope a mʼmisewu.

44“Inu mwandipulumutsa mʼmanja mwa mitundu ya anthu;

Inu mwandisunga kuti ndikhale mtsogoleri wa anthu a mitundu ina.

Anthu amene sindikuwadziwa ali pansi pa ulamuliro wanga.

45Alendo amadzipereka okha pamaso panga;

akangomva za ine, amandigonjera.

46Iwo onse anataya mtima;

anatuluka mʼmalinga awo akunjenjemera.

47“Yehova ndi wamoyo! Litamandidwe Thanthwe langa.

Akuzike Mulungu, Thanthwe, Mpulumutsi wanga!

48Iye ndi Mulungu amene amabwezera chilango,

amene amayika anthu a mitundu yonse pansi pa ulamuliro wanga,

49amene amandimasula mʼmanja mwa adani anga.

Inu munandikuza kuposa adani anga;

munandilanditsa mʼmanja mwa anthu ankhanza.

50Choncho ine ndidzakutamandani Inu Yehova, pakati pa anthu a mitundu ina;

ndidzayimba nyimbo zotamanda dzina lanu.

51“Iye amapereka chipambano chachikulu kwa mfumu yake,

amaonetsa kukoma mtima kwa wodzozedwa wake,

kwa Davide ndi zidzukulu zake kwamuyaya.”