2 Samueli 19 – CCL & TNCV

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Samueli 19:1-43

1Yowabu anawuzidwa kuti, “Mfumu ikulira maliro a Abisalomu.” 2Ndipo kwa asilikali onse chipambano cha tsiku limenelo chinasandulika maliro, chifukwa tsiku limenelo anthu anamva kuti mfumu ili pa chisoni chachikulu chifukwa cha mwana wake. 3Ankhondo analowa mu mzinda mwakachetechete tsiku limenelo ngati momwe amalowera anthu mwamanyazi chifukwa athawa ku nkhondo. 4Mfumu inaphimba nkhope yake ndipo inalira mofuwula, “Iwe mwana wanga Abisalomu! Iwe Abisalomu, mwana wanga, mwana wanga!”

5Kenaka Yowabu analowa mʼnyumba ya mfumu nafika kwa mfumuyo ndipo anati, “Lero mwachititsa manyazi asilikali anu onse, amene apulumutsa moyo wanu ndiponso moyo wa ana anu aamuna ndi aakazi, kudzanso moyo wa akazi anu ndi wa azikazi anu. 6Inu mumakonda amene amadana nanu ndipo mumadana ndi amene amakukondani. Inuyo mwaonetsa lero poyera kuti simusamala za atsogoleri anu a nkhondo ndi asilikali awo. Ine ndikuona kuti inu mukanakondwera ngati Abisalomu akanakhala ndi moyo lero, tonsefe titafa. 7Tsopano pitani mukawalimbikitse asilikali anu. Ine ndikulumbira mwa Yehova kuti ngati inu simupita palibe munthu amene adzatsale ali ndi inu polowa dzuwa. Ichi chidzakhala choyipa kwambiri kuposa zovuta zonse zimene zinakugwerani kuyambira muli mnyamata mpaka lero.”

8Kotero mfumu inanyamuka ndipo inakhala pa mpando wake pa chipata. Pamene asilikali anawuzidwa kuti, “Mfumu yakhala pa chipata,” onse anabwera kwa iye.

Davide Abwerera ku Yerusalemu

Nthawi imeneyi nʼkuti Aisraeli atathawira ku nyumba zawo. 9Pakati pa mafuko onse a Israeli, anthu amakangana ndipo amati, “Mfumu inatipulumutsa mʼmanja mwa adani anthu. Iye ndi amene anatilanditsa mʼdzanja la Afilisti. Koma tsopano wathawa mʼdziko muno chifukwa cha Abisalomu. 10Ndipo Abisalomu amene ife tinamudzoza kuti atilamulire wafa pa nkhondo. Tsono nʼchifukwa chiyani simukunena kanthu za kubweretsanso mfumu?”

11Mfumu Davide inatumiza uthenga uwu kwa ansembe Zadoki ndi Abiatara, “Funsani akuluakulu a Yuda, ‘Nʼchifukwa chiyani inu mukukhala otsiriza kuyitana mfumu ku nyumba yake yaufumu, pakuti zimene zikunenedwa mu Israeli yense zamveka kwa mfumu ndi onse amene akukhala nayo. 12Inu ndinu abale anga enieni, mafupa anga ndi mnofu wanga. Nʼchifukwa chiyani inuyo mukukhala otsiriza kubweretsa mfumu?’ 13Ndipo munene kwa Amasa, ‘Kodi iwe si mʼbale wanga weniweni? Mulungu andilange, andilange kwambiri ngati kuyambira tsopano sukhala mtsogoleri wa ankhondo anga kulowa mʼmalo mwa Yowabu.’ ”

14Davide anakopa mitima ya anthu onse a Yuda ndipo anthuwo anakhala ngati munthu mmodzi. Iwo anatumiza mawu kwa mfumu, “Bwererani inu ndi anthu anu onse.” 15Kotero mfumu inabwerera ndipo inakafika mpaka ku Yorodani.

Tsono anthu a ku Yuda anabwera ku Giligala kuti akakumane ndi mfumu ndi kumuwolotsa Yorodani. 16Simei mwana wa Gera, wa fuko la Benjamini wa ku Bahurimu, anabwera mofulumira pamodzi ndi Ayuda kudzakumana ndi mfumu Davide. 17Iyeyo anali ndi anthu 1,000 a fuko la Benjamini pamodzi ndi Ziba, wantchito wa banja la Sauli ndi ana ake aamuna khumi ndi asanu ndi antchito ake makumi awiri. Iwo anathamangira ku Yorodani kumene kunali mfumu. 18Iwo anawoloka mtsinje kukatenga banja lonse la mfumu ndi kuchita zonse zimene mfumuyo imafuna.

Pamene Simei mwana wa Gera anawoloka Yorodani, anagwa pansi chafufumimba pamaso pa mfumu, 19ndipo anati, “Mbuye wanga musaganizire za kulakwa kwanga. Musakumbukire zolakwa zimene mtumiki wanu anakuchitirani tsiku limene mbuye wanga mfumu mumachoka mu Yerusalemu. Mfumu musazikumbukirenso zimenezi. 20Pakuti ine mtumiki wanu ndazindikira kuti ndachimwa. Koma lero ndabwera ngati woyamba wa nyumba ya Yosefe yonse kudzakumana nanu mbuye wanga mfumu.”

21Ndipo Abisai mwana wa Zeruya anati, “Kodi Simei saphedwa chifukwa cha ichi? Iye anatukwana wodzozedwa wa Yehova.”

22Davide anayankha kuti, “Kodi inu ana a Zeruya, ndikuchitireni chiyani? Lero lino iwe wakhala mdani wanga! Kodi wina aphedwe lero mu Israeli? Kodi ine sindikudziwa kuti lero ndine mfumu mu Israeli?” 23Ndipo mfumu inati kwa Simei, “Iwe Simei suphedwa.” Ndipo mfumuyo inalonjeza ndi lumbiro.

24Mefiboseti, mdzukulu wa Sauli, nayenso anabwera kudzakumana ndi mfumu. Kuyambira tsiku limene mfumu inachoka mpaka tsiku limene inabwerera mu mtendere, iye sanasambe mapazi kaya kumeta ndevu kapena kuchapa zovala zake. 25Pamene anafika kuchokera ku Yerusalemu kudzakumana ndi mfumu, mfumu inamufunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani sunapite nane Mefiboseti?”

26Iye anayankha kuti, “Mbuye wanga mfumu, pakuti ine wantchito wanu ndine wolumala. Ndinati, ‘Andikonzere chishalo cha bulu wanga ndipo ndidzakwera kuti ndipite ndi mfumu.’ Koma Ziba wantchito wanga anandilakwitsa. 27Ndipo wayankhula zosinjirira za ine mtumiki wanu kwa inu mbuye wanga mfumu. Mbuye wanga mfumu ali ngati mngelo wa Mulungu ndipo chitani chimene chikukomerani. 28Zidzukulu zonse za agogo anga sizinayenera chilichonse koma imfa kuchokera kwa inu mbuye wanga mfumu, koma inu munapereka malo kwa mtumiki wanu pakati pa amene amadya pa tebulo lanu. Tsono ine ndili ndi chiyaninso kuti ndipitirize kudandaula kwa mfumu?”

29Mfumu inayankha kuti, “Uneneranji zambiri? Ine ndikulamula kuti iwe ndi Ziba mugawane minda.”

30Mefiboseti anati kwa mfumu, “Muloleni atenge zonse, pakuti tsopano mbuye wanga mwafika kwanu mu mtendere.”

31Barizilai Mgiliyadi anabweranso kuchokera ku Rogelimu kudzawoloka Yorodani ndi mfumu ndi kumuperekeza kuchokera kumeneko. 32Tsono Barizilai anali wokalamba kwambiri, wa zaka makumi asanu ndi atatu. Iye ndi amene anapereka zinthu kwa mfumu pamene anali ku Mahanaimu pakuti anali wolemera kwambiri. 33Mfumu inati kwa Barizilai, “Woloka nane ndipo ukakhale ndi ine mu Yerusalemu ndipo ineyo ndidzakusamalira.”

34Barizilai anayankha mfumu kuti, “Kodi zakhala zaka zingati zoti ndikhale ndi moyo, kuti ndipite ku Yerusalemu ndi mfumu? 35Ine tsopano ndili ndi zaka 80. Kodi ndingathe kusiyanitsa pakati pa chabwino ndi choyipa? Kodi mtumiki wanu angathe kuzindikira kukoma kwa zimene akudya ndi kumwa? Kodi ndingathe kumva kuyimba kwa amuna ndi akazi? Nʼchifukwa chiyani wantchito wanu akakhale ngati katundu kwa mbuye wanga mfumu? 36Koma ine mtumiki wanu ndingoyenda pangʼono kuti ndiwoloke Yorodani pamodzi ndi mfumu. Amfumu mungandipatsirenji mphotho yotere? 37Muloleni, mtumiki wanu abwerere, kuti ndikafere kwathu pafupi ndi manda a abambo ndi amayi anga. Koma nayu mtumiki wanu Kimuhamu. Muloleni iye awoloke nanu mbuye wanga mfumu. Mumuchitire chilichonse chimene chikukomereni!”

38Mfumu inati, “Kimuhamu adzawoloka ndi ine, ndipo ndidzamuchitira iye chilichonse chimene chidzakondweretsa iwe. Ndipo chilichonse chimene udzandipempha ine ndidzakuchitira.”

39Kotero anthu onse anawoloka Yorodani ndipo kenaka mfumu inawoloka. Mfumu inapsompsona Barizilai ndi kumupatsa madalitso ndipo Barizilaiyo anabwerera kwawo.

40Pamene mfumu inawolokera ku Giligala, Kimuhamu anawoloka naye. Ankhondo onse a Yuda ndi theka la ankhondo a Israeli onse anaperekeza mfumu.

41Kenaka Aisraeli onse amabwera kwa mfumu nʼkumati kwa iye, “Nʼchifukwa chiyani abale athu, anthu a ku Ayuda, anakubani mfumu, nawoloka nanu Yorodani inu ndi banja lanu, pamodzi ndi anthu ake onse?”

42Ayuda onse anayankha Aisraeli kuti, “Ife timachita zimenezi chifukwa mfumu ndi mʼbale wathu. Nʼchifukwa chiyani inu mwapsa mtima ndi zimenezi? Kodi ife tinadya chakudya chilichonse cha mfumu? Kodi chilipo chimene ife tatenga kukhala chathu?”

43Aisraeli anayankha Ayuda kuti, “Ife ndi magawo khumi mwa mfumu imeneyi, ndipo kuwonjezera apo, ife tili ndi zinthu zambiri mwa Davide kuposa inu. Tsono nʼchifukwa chiyani mukutichita chipongwe? Kodi ife si amene tinayamba kunena za kubweretsa mfumu yathu?”

Koma anthu a Yuda anayankha mwaukali kwambiri kupambana anthu a ku Israeli.

Thai New Contemporary Bible

2ซามูเอล 19:1-43

1เมื่อโยอาบทราบว่ากษัตริย์ทรงกันแสงและอาลัยถึงอับซาโลม 2และเมื่อทั้งกองทัพทราบว่ากษัตริย์ทรงเศร้าโศกเสียใจเรื่องราชโอรส ความปลื้มปีติในชัยชนะใหญ่หลวงในวันนั้นก็กลับกลายเป็นความโศกสลด 3ทั้งกองทัพค่อยๆ เคลื่อนเข้าสู่กรุงอย่างเงียบเหงาเหมือนคนที่เข้ามาอย่างอับอายเพราะหนีจากการรบ 4ดาวิดซบพระพักตร์ลงกับพระหัตถ์คร่ำครวญว่า “โอ อับซาโลมลูกของพ่อ! โอ อับซาโลมลูกของพ่อ ลูกของพ่อ!”

5โยอาบจึงเข้าไปยังที่ประทับ และกราบทูลว่า “วันนี้ฝ่าพระบาททรงทำให้คนของฝ่าพระบาท ผู้ได้ปกป้องพระชนม์ชีพของฝ่าพระบาทรวมทั้งชีวิตของราชโอรส ราชธิดา มเหสี และสนมไว้นั้นรู้สึกอัปยศอดสู 6ฝ่าพระบาททรงรักอาลัยผู้ที่ชิงชังฝ่าพระบาท และทรงชิงชังผู้ที่รักฝ่าพระบาท ในวันนี้ฝ่าพระบาททรงแสดงให้เห็นชัดว่าบรรดานายทัพ และทหารล้วนไม่มีความหมายอะไรเลยสำหรับฝ่าพระบาท หากอับซาโลมมีชีวิตอยู่และพวกข้าพระบาทตายไปหมด ฝ่าพระบาทคงจะพอพระทัย 7บัดนี้ขอทรงโปรดเสด็จออกไปประทานกำลังใจแก่พวกทหาร ข้าพระบาทขอสาบานโดยอ้างองค์พระผู้เป็นเจ้าว่า หากไม่เสด็จไปจะไม่เหลือพวกเขาแม้แต่คนเดียวในคืนนี้ นี่จะเป็นสิ่งเลวร้ายสำหรับฝ่าพระบาท ยิ่งกว่าที่ฝ่าพระบาทเคยประสบภัยพิบัติใดมาตลอดพระชนม์ชีพ”

8กษัตริย์จึงเสด็จออกไปประทับอยู่ที่ประตูเมือง และเมื่อเขาทั้งปวงทราบว่ากษัตริย์ประทับอยู่ที่นั่น พวกเขาก็พากันมาเข้าเฝ้า

ขณะเดียวกันคนอิสราเอลก็หนีกลับบ้านของตน

ดาวิดเสด็จกลับกรุงเยรูซาเล็ม

9ผู้คนถกเถียงกันทั่วทุกเผ่าของอิสราเอลว่า “กษัตริย์ได้ทรงกอบกู้เราให้พ้นจากมือของศัตรู ทรงช่วยเราให้พ้นจากมือของชาวฟีลิสเตีย แต่บัดนี้พระองค์ทรงหนีจากแผ่นดินไปเพราะอับซาโลม 10และอับซาโลมผู้ที่พวกเราเจิมตั้งให้ปกครองเรา ก็สิ้นพระชนม์แล้วในสงคราม ทำไมเราไม่มาพูดถึงเรื่องทูลเชิญกษัตริย์กลับมา?”

11กษัตริย์ดาวิดทรงส่งข่าวไปถึงปุโรหิตศาโดกและปุโรหิตอาบียาธาร์ว่า “จงถามบรรดาผู้อาวุโสของยูดาห์ว่า ‘ทำไมท่านเป็นพวกสุดท้ายที่เชิญกษัตริย์กลับพระราชวังของพระองค์ เพราะว่ากษัตริย์ได้ยินสิ่งที่พวกท่านพูดกันทั่วอิสราเอล 12พวกท่านเป็นพี่น้องร่วมตระกูล เป็นเลือดเนื้อเชื้อไขเดียวกันแท้ๆ ทำไมจึงกลายเป็นพวกสุดท้ายที่มาทูลเชิญกษัตริย์กลับ?’ 13และให้ไปบอกอามาสาว่า ‘เจ้าก็เป็นเลือดเนื้อเชื้อไขเดียวกับเราไม่ใช่หรือ? ขอพระเจ้าทรงจัดการกับเราอย่างสาหัส หากเจ้าไม่ได้เป็นแม่ทัพของเราแทนโยอาบนับแต่นี้’”

14ดังนั้นบรรดาคนยูดาห์ก็ได้รับการโน้มน้าวใจจนมีมติเป็นเอกฉันท์ พวกเขามากราบทูลกษัตริย์ว่า “เชิญเสด็จกลับมาหาพวกข้าพระบาท พร้อมทั้งบรรดาผู้ที่ร่วมเสด็จด้วย” 15กษัตริย์จึงเสด็จกลับ และมาถึงแม่น้ำจอร์แดน

ชาวยูดาห์พากันมาที่กิลกาลเพื่อรับเสด็จและส่งเสด็จข้ามแม่น้ำจอร์แดน 16ฝ่ายชิเมอีบุตรเกรา คนเบนยามินจากบาฮูริมรีบรุดมาสมทบกับคนยูดาห์เพื่อรับเสด็จกษัตริย์ดาวิด 17คนที่มากับชิเมอีคือคนเบนยามินหนึ่งพันคน พร้อมทั้งศิบาข้าราชบริพารของซาอูล บุตรชายทั้งสิบห้าคนและคนใช้ยี่สิบคนของศิบา พวกเขารีบรุดมายังแม่น้ำจอร์แดนที่กษัตริย์ประทับอยู่ 18พวกเขากุลีกุจอส่งเชื้อพระวงศ์ข้ามฟาก และให้ความช่วยเหลือต่างๆ นานา

เมื่อชิเมอีบุตรเกราข้ามแม่น้ำจอร์แดนมา เขาหมอบกราบลงต่อหน้ากษัตริย์ดาวิด 19และทูลว่า “ขอโปรดอภัยโทษแก่ข้าพระบาท และอย่าทรงจดจำสิ่งผิดพลาดที่ข้าพระบาทได้ทำเมื่อครั้งฝ่าพระบาทเสด็จออกจากเยรูซาเล็มด้วยเถิด 20เพราะผู้รับใช้สำนึกว่าได้ทำบาปไปแล้ว ข้าพระบาทจึงมาที่นี่ในวันนี้เป็นคนแรกสุดของวงศ์วานโยเซฟที่มารับเสด็จ”

21อาบีชัยบุตรนางเศรุยาห์ทูลว่า “ชิเมอีไม่สมควรตายหรอกหรือที่ได้บังอาจแช่งด่ากษัตริย์ที่องค์พระผู้เป็นเจ้าทรงเจิมตั้งไว้?”

22ดาวิดตรัสว่า “บุตรนางเศรุยาห์เอ๋ย เจ้าเกี่ยวข้องอะไรกับเรื่องนี้ เจ้ามีสิทธิ์อะไรมาก้าวก่าย! ควรหรือที่จะมีใครในอิสราเอลถูกประหารในวันนี้? เราไม่รู้หรือว่าวันนี้เราคือกษัตริย์ของอิสราเอล?” 23แล้วกษัตริย์จึงตรัสกับชิเมอีว่า “เราไว้ชีวิตเจ้า” และทรงสาบานรับรอง

24เมฟีโบเชทหลานชายของซาอูลก็มารับเสด็จด้วย เขาไม่ได้ดูแลเท้าหรือซักเสื้อผ้าหรือขริบเคราเลยตั้งแต่วันที่กษัตริย์เสด็จจากไปจวบจนเสด็จกลับมาโดยสวัสดิภาพ 25เมื่อเมฟีโบเชทเดินทางจากเยรูซาเล็มมาเข้าเฝ้า กษัตริย์ตรัสถามว่า “เมฟีโบเชท ทำไมเจ้าจึงไม่ไปกับเรา?”

26เขาทูลว่า “ข้าแต่องค์กษัตริย์ เพราะข้าพระบาทขาพิการจึงสั่งศิบาว่า ‘จงจัดอานลาให้เราได้ตามเสด็จ’ แต่ศิบาทรยศ 27เขาทูลใส่ร้ายหาว่าข้าพระบาทไม่ยอมไป แต่ฝ่าพระบาททรงเป็นเหมือนทูตของพระเจ้า ขอทรงทำต่อข้าพระบาทตามที่ทรงเห็นชอบเถิด 28วงศ์วานทั้งหมดของเสด็จปู่ของข้าพระบาท ไม่สมควรได้รับสิ่งใดจากฝ่าพระบาทนอกจากความตาย แต่ฝ่าพระบาทกลับประทานเกียรติให้ร่วมโต๊ะเสวย ดังนั้นข้าพระบาทจะปริปากทูลอะไรได้?”

29ดาวิดตรัสว่า “จะพูดให้มากความไปทำไม? เจ้ากับศิบาจงแบ่งที่ดินกัน”

30เมฟีโบเชททูลว่า “ให้เขาเอาไปทั้งหมดเถิด ในเมื่อฝ่าพระบาทเสด็จกลับมาโดยปลอดภัยเช่นนี้แล้ว”

31บารซิลลัยชาวกิเลอาดก็มาจากเมืองโรเกลิมด้วยเพื่อตามเสด็จข้ามแม่น้ำจอร์แดนและส่งเสด็จ 32บารซิลลัยชรามาก อายุได้แปดสิบปีแล้ว เขาได้นำเสบียงอาหารมาถวายขณะกษัตริย์ประทับอยู่ที่มาหะนาอิม เพราะเขาร่ำรวยมาก 33กษัตริย์ตรัสกับบารซิลลัยว่า “ข้ามมาอยู่กับเราที่กรุงเยรูซาเล็มเถิด เราจะดูแลท่านเอง”

34แต่บารซิลลัยกราบทูลว่า “ข้าพระบาทจะอยู่ไปได้อีกกี่ปี พระองค์จึงให้ตามเสด็จไปกรุงเยรูซาเล็ม? 35บัดนี้ข้าพระบาทอายุแปดสิบปีแล้ว อะไรดีไม่ดีจะแยกแยะได้หรือ? กินดื่มอะไรจะลิ้มรสได้หรือ? เสียงนักร้องชายหญิงจะได้ยินหรือ? ควรหรือที่ผู้รับใช้ของฝ่าพระบาทจะไปเพิ่มภาระให้แก่ฝ่าพระบาท? 36ข้าพระบาทจะขอตามเสด็จข้ามแม่น้ำจอร์แดนไปเท่านั้น ฝ่าพระบาทจะปูนบำเหน็จให้ทำไมเล่า? 37ข้าพระบาทขอกลับไปตายที่บ้านเกิดเมืองนอน ใกล้ๆ อุโมงค์ฝังศพของบิดามารดา แต่นี่คือคิมฮามผู้รับใช้ของฝ่าพระบาท ขอให้เขาตามเสด็จฝ่าพระบาทไป ขอทรงทำแก่เขาตามที่ทรงเห็นชอบเถิด”

38กษัตริย์ดาวิดตรัสว่า “คิมฮามจะไปกับเรา เราจะปฏิบัติต่อเขาตามที่ท่านเห็นสมควร สิ่งใดที่ท่านอยากได้จากเรา เราจะทำให้ท่าน”

39ฉะนั้นประชากรทั้งหมดจึงข้ามแม่น้ำจอร์แดน แล้วกษัตริย์ก็เสด็จข้ามไป ดาวิดทรงจูบและให้พรแก่บารซิลลัย แล้วบารซิลลัยก็กลับบ้าน

40กษัตริย์เสด็จต่อไปยังกิลกาล ให้คิมฮามตามเสด็จไปด้วย กำลังพลยูดาห์ทั้งหมดและทหารอิสราเอลครึ่งหนึ่งคอยรับเสด็จอยู่ที่นั่นแล้ว

41แล้วคนอิสราเอลทั้งหมดมาเข้าเฝ้ากษัตริย์และทูลว่า “เหตุใดพี่น้องชนยูดาห์จึงชิงตัดหน้าเชิญกษัตริย์กับราชวงศ์และข้าราชบริพารข้ามแม่น้ำจอร์แดนไปก่อน?”

42คนยูดาห์โต้ตอบว่า “เราทำเช่นนั้นก็เพราะกษัตริย์ทรงเกี่ยวโยงใกล้ชิดกับพวกเรา ทำไมเรื่องแค่นี้พวกท่านต้องโกรธด้วย? เรากินเสบียงใดๆ ของกษัตริย์หรือ? มีสิ่งใดที่เราฉกฉวยมาเป็นของตนหรือ?”

43คนอิสราเอลโต้กลับว่า “พวกเรามีสิทธิ์ในองค์กษัตริย์สิบส่วน มิหนำซ้ำเรามีสิทธิ์ในกษัตริย์ดาวิดมากกว่าพวกท่าน ทำไมพวกท่านไม่ไว้หน้าพวกเรา? เราเป็นพวกแรกใช่ไหมที่พูดถึงเรื่องการเชิญกษัตริย์เสด็จกลับมา?”

แต่คนยูดาห์โต้ตอบด้วยวาจาเผ็ดร้อนยิ่งกว่าคนอิสราเอล